Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 24 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Look—our Father lays the earth waste and leaves it empty; he twists its surface and scatters its inhabitants. Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansi ndi kulisandutsa chipululu; Iye adzasakaza maonekedwe ake ndi kumwaza anthu ake onse.
2 It will be the same for the people as for the priest, for the servant as for his master, for the maid as for her mistress, for the buyer as for the seller, for the lender as for the borrower, for the creditor as for the debtor. Aliyense zidzamuchitikira mofanana: wansembe chimodzimodzi munthu wamba, antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna, antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi, wogula chimodzimodzi wogulitsa, wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa, okongola chimodzimodzi okongoza.
3 The earth will be utterly laid waste and utterly plundered, for our Father has spoken this word. Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthu ndi kusakazikiratu. Yehova wanena mawu awa.
4 The earth mourns and withers; the world fades and withers; the exalted ones of the earth fade away. Dziko lapansi likulira ndipo likufota, dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma, anthu omveka a dziko lapansi akuvutika.
5 The earth lies defiled beneath its inhabitants, for they have disobeyed the teachings, violated the statute, and broken the everlasting covenant. Anthu ayipitsa dziko lapansi; posamvera malangizo ake; pophwanya mawu ake ndi pangano lake lamuyaya.
6 Therefore a curse devours the earth, and those who dwell in it bear their guilt; therefore the earth's inhabitants are burned away, and few people are left. Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi; anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo, iwo asakazika ndipo atsala ochepa okha.
7 The new wine mourns, the vine grows weak; all the merrymakers sigh. Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota; onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni.
8 The joy of the tambourines is stilled, the uproar of the revelers has ceased, the joy of the lyre is stilled. Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha, phokoso la anthu osangalala latha, zeze wosangalatsa wati zii.
9 No longer do they drink wine with song; strong drink turns bitter to those who drink it. Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo; akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo.
10 The city of chaos is shattered; every house is shut up, with no way in. Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka; nyumba iliyonse yatsekedwa.
11 In the streets there is an outcry over the wine; all gladness has gone dark, the joy of the earth is driven away. Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo; chimwemwe chonse chatheratu, palibenso chisangalalo pa dziko lapansi.
12 Only desolation is left in the city; the gate is battered to ruins. Mzinda wasanduka bwinja zipata zake zagumuka.
13 For so it will be throughout the earth, among the peoples: like an olive tree beaten bare, like the grapes left behind when the harvest is done. Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi ndiponso pakati pa mitundu ya anthu. Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa, kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.
14 They lift up their voices, they sing for joy; over the majesty of our Father they cry aloud from the west. Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe; anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.
15 Therefore in the east give glory to our Father; on the shores of the sea, glorify the name of our Father, the God of Israel. Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova; ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.
16 From the ends of the earth we hear songs: "Glory to the Righteous One!" But I said, "I waste away, I waste away—woe to me! The treacherous betray; with treachery the treacherous betray." Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda “Wolungamayo.” Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo, inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”
17 Terror and pit and snare are upon you, you who dwell on the earth! Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenje ndi msampha zikukudikirani.
18 Whoever flees at the sound of the terror will fall into the pit, and whoever climbs out of the pit will be caught in the snare. For the windows of heaven are opened, and the foundations of the earth tremble. Aliyense wothawa phokoso la zoopsa adzagwa mʼdzenje; ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo adzakodwa ndi msampha. Zitseko zakumwamba zatsekulidwa, ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.
19 The earth is utterly broken apart, the earth is torn apart, the earth is violently shaken. Dziko lapansi lathyokathyoka, ndipo lagawika pakati, dziko lapansi lagwedezeka kotheratu.
20 The earth staggers like a drunkard, it sways like a hut; its rebellion lies heavy upon it, and it falls and will not rise again. Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba; lalemedwa ndi machimo ake. Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.
21 On that day our Father will punish the host of the heights in the heights, and the kings of the earth on the earth. Tsiku limenelo Yehova adzalanga amphamvu a kumwamba ndiponso mafumu apansi pano.
22 They will be herded together like prisoners into a pit; they will be locked up in a dungeon, and after many days they will be punished. Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi ngati amʼndende amene ali mʼdzenje. Adzawatsekera mʼndende ndipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali.
23 Then the moon will be ashamed and the sun put to shame, for the Father of heaven's armies reigns on Mount Zion and in Jerusalem, and before his elders his glory shines. Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira; pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]