Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Hebrews 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The law is only a shadow of the good things to come, not the true form of those realities, and so, by the same sacrifices offered year after year without end, can never perfect those who draw near. Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza.
2 Otherwise, wouldn't they have stopped being offered, since worshipers, cleansed once, would no longer be conscious of sins? Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo.
3 But in these sacrifices there is a yearly reminder of sins. Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka.
4 For it is impossible for the blood of bulls and goats to take away sins. Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.
5 Therefore, when Christ came into the world, he said: "Sacrifice and offering you did not desire, but a body you prepared for me; Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati, “Simunafune nsembe kapena zopereka, koma thupi munandikonzera.
6 "in burnt offerings and sin offerings you took no pleasure. Simunakondwere nazo nsembe zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.
7 Then I said, 'Look, I have come—in the scroll of the book it is written of me—to do your will, my Father.'" Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ”
8 Above he said, "Sacrifices, offerings, burnt offerings, and sin offerings you did not desire or delight in"—though the law requires them, Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe.
9 then he said, "Look, I have come to do your will." He removes the first to establish the second. Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri.
10 By this will, we have been made holy through the offering of Jesus Christ's body, once for all. Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.
11 Every priest stands daily, serving and repeatedly offering the same sacrifices that can never remove sins. Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo.
12 But he offered one sacrifice for sins forever, then sat down at the right hand of our Father, Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu.
13 waiting from that time until his enemies are made a footstool for his feet. Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake.
14 For by one offering he has perfected for all time those who are being made holy. Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.
15 And the Holy Spirit also testifies to us; for after saying, Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,
16 "This is the covenant that I will make with them after those days, says our Father: I will put my laws on their hearts, and write them on their minds." “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo,” akutero Yehova. “Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo, ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”
17 He then adds, "And their sins and their lawless deeds I will remember no more." Ndipo akutinso: “Sindidzakumbukiranso konse machimo awo ndi zolakwa zawo.”
18 Now where these are forgiven, there is no longer any offering for sin. Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.
19 So, brothers and sisters, since we have confidence to enter the holy places by Jesus' blood, Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu.
20 a new, living way he opened for us through the curtain—his flesh, Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake.
21 and since we have a great priest over the house of our Father, Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu.
22 let us draw near with a genuine heart, fully assured by faith, hearts sprinkled clean from a guilty conscience, and bodies washed with pure water. Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera.
23 Let us hold tightly to the hope we declare, unshaken, for he who promised is faithful. Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.
24 And let us consider how to spur one another on to love and good works, Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino.
25 not giving up meeting together, as some habitually do, but encouraging each other—even more as you see the Day approaching. Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
26 For if we go on sinning deliberately after receiving the knowledge of the truth, no sacrifice for sins remains, Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
27 but only a terrible expectation of judgment and a raging fire that will consume the adversaries. Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu
28 Anyone who rejects Moses' law dies without mercy on two or three witnesses' testimony. Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu.
29 How much worse punishment, do you think, does the one deserve who trampled the Son of our Father underfoot, treated as unholy the blood of the covenant that made him holy, and insulted the Spirit of grace? Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?
30 For we know the one who said, "Justice is mine; I will repay," and again, "Our Father will judge his people." Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”
31 It is a terrible thing to fall into the hands of the living Father. Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.
32 Remember the earlier days, when after being enlightened you endured a hard struggle with suffering, Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri.
33 at times publicly shamed by insults and suffering, at times standing with those treated that way. Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere.
34 For you suffered with prisoners and joyfully accepted your possessions being seized, knowing you yourselves had a better, lasting possession. Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.
35 So do not throw away your confidence; it holds a great reward. Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.
36 You need endurance, so that having done our Father's will, you may receive the promise. Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza.
37 For yet "in a very little while, the coming one will come and will not delay; Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe, Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
38 but my righteous one will live by faith, and if he shrinks back, my soul takes no pleasure in him." Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro. Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha, Ine sindidzakondwera naye.
39 But we don't belong to those who shrink back into destruction, but to those who have faith and preserve their souls. Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]