Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Genesis 11 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Now the whole earth had one language and a common speech. Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi.
2 And as they migrated eastward, they found a plain in the land of Shinar and settled there. Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.
3 They said to each other, "Come, let's make bricks and fire them hard." They used brick for stone, tar for mortar. Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.
4 Then they said, "Come, let's build us a city and tower with its top in the sky, and make us a name, so we don't scatter over the face of the whole earth." Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
5 But our Father came down to see the city and the tower that the people were building. Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga.
6 And our Father said, "Look, they are one people with one language, and this is only the start of what they will do. Now nothing they plan to do will be impossible for them. Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita.
7 Come, let's go down there and scramble their language, so no one understands a neighbor's language." Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”
8 So our Father scattered them from there across all the earth's face, and they stopped building the city. Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo.
9 So it was called Babel, for there our Father confused all the earth's language, and from there scattered them over all the earth's face. Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
10 This is Shem's account: at 100, he fathered Arpachshad, two years after the flood. Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi.
11 Shem lived 500 years after he fathered Arpachshad, and had other sons and daughters. Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
12 When Arpachshad had lived thirty-five years, he fathered Shelah. Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela.
13 Arpachshad lived 403 years after he fathered Shelah, and had other sons and daughters. Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
14 When Shelah had lived thirty years, he fathered Eber. Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi.
15 Shelah lived 403 years after he fathered Eber, and had other sons and daughters. Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
16 When Eber had lived thirty-four years, he fathered Peleg. Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi.
17 Eber lived 430 years after he fathered Peleg, and had other sons and daughters. Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
18 When Peleg had lived thirty years, he fathered Reu. Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu.
19 Peleg lived 209 years after he fathered Reu, and had other sons and daughters. Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
20 When Reu had lived thirty-two years, he fathered Serug. Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi.
21 Reu lived 207 years after he fathered Serug, and had other sons and daughters. Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
22 When Serug had lived thirty years, he fathered Nahor. Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori.
23 Serug lived 200 years after he fathered Nahor, and had other sons and daughters. Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
24 When Nahor had lived twenty-nine years, he fathered Terah. Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera.
25 Nahor lived 119 years after he fathered Terah, and had other sons and daughters. Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
26 When Terah had lived seventy years, he fathered Abram, Nahor, and Haran. Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
27 Now these are the generations of Terah. Terah fathered Abram, Nahor, and Haran; and Haran fathered Lot. Nayi mibado yochokera mwa Tera. Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti.
28 Haran died in his birthplace, Ur of the Chaldeans, before his father Terah. Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira.
29 Abram and Nahor married; Abram's wife was Sarai, and Nahor's wife was Milcah, daughter of Haran, who was also the father of Iscah. Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani.
30 Now Sarai was unable to conceive; she had no children. Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.
31 Terah took his son Abram, his grandson Lot son of Haran, and his daughter-in-law Sarai, Abram's wife, and left Ur of the Chaldeans for Canaan; they reached Haran and settled there. Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
32 Terah lived 205 years, and died in Haran. Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]