Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Genesis 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 This is the account of Noah's sons—Shem, Ham, and Japheth. Sons were born to them after the flood. Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
2 The sons of Japheth: Gomer, Magog, Madai, Javan, Tubal, Meshech, and Tiras. Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
3 The sons of Gomer: Ashkenaz, Riphath, and Togarmah. Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
4 The sons of Javan: Elishah, Tarshish, Kittim, and Rodanim. Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
5 From these the coastland peoples divided into their lands, each by language, clan, and nation. (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
6 The sons of Ham: Cush, Mizraim, Put, and Canaan. Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.
7 The sons of Cush: Seba, Havilah, Sabtah, Raamah, and Sabteca. The sons of Raamah: Sheba and Dedan. Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
8 Cush fathered Nimrod, who was the first mighty man on the earth. Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.
9 He was a mighty hunter before God, so they say, "Like Nimrod, a mighty hunter before God." Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
10 The beginning of his kingdom was Babel, Erech, Accad, and Calneh, in the land of Shinar. Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
11 From that land he went out to Assyria and built Nineveh, Rehoboth-Ir, Calah, Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,
12 and Resen, between Nineveh and Calah; this is the great city. ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
13 Mizraim fathered the Ludim, the Anamim, the Lehabim, the Naphtuhim, Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
14 the Pathrusim, the Casluhim (from whom the Philistines came), and the Caphtorim. Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
15 Canaan fathered Sidon his firstborn, and Heth, Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;
16 and the Jebusites, the Amorites, the Girgashites, Ayebusi, Aamori, Agirigasi;
17 the Hivites, the Arkites, the Sinites, Ahivi, Aariki, Asini,
18 the Arvadites, the Zemarites, and the Hamathites. Afterward the clans of the Canaanites spread out. Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse,
19 Canaan's border ran from Sidon toward Gerar to Gaza, and toward Sodom, Gomorrah, Admah, and Zeboiim, to Lasha. mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
20 These are Ham's sons, by their clans, languages, lands, and nations. Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
21 Children were also born to Shem, older brother of Japheth, father of all Eber's descendants. Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
22 The sons of Shem: Elam, Asshur, Arphaxad, Lud, and Aram. Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
23 The sons of Aram: Uz, Hul, Gether, and Mash. Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
24 Arphaxad fathered Shelah, and Shelah fathered Eber. Aripakisadi anabereka Sela, ndipo Selayo anabereka Eberi.
25 Eber had two sons: one named Peleg, for the earth was divided in his days, and his brother named Joktan. A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
26 Joktan fathered Almodad, Sheleph, Hazarmaveth, Jerah, Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
27 Hadoram, Uzal, Diklah, Hadoramu, Uzali, Dikila,
28 Obal, Abimael, Sheba, Obali, Abimaeli, Seba,
29 Ophir, Havilah, and Jobab; all these were the sons of Joktan. Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
30 Their territory extended from Mesha toward Sephar, to the hill country of the east. Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
31 These are Shem's sons, by their clans, languages, lands, and nations. Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
32 These are the clans of Noah's sons, by their lines of descent, in their nations; from these the nations spread across the earth after the flood. Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]