Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Ezra 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 In Cyrus king of Persia's first year, to fulfill our Father's word through Jeremiah, our Father stirred Cyrus king of Persia's spirit, so that he sent a proclamation throughout all his kingdom and put it in writing: Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.
2 This is what Cyrus king of Persia says: "The LORD, God of heaven, has given me all the kingdoms of the earth, and has appointed me to build him a house at Jerusalem in Judah. Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti, “ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.
3 Whoever among you of all his people—may his God be with him—let him go up to Jerusalem in Judah and rebuild the house of the LORD, the God of Israel; he is the God in Jerusalem. Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu.
4 Let every survivor, wherever he lives, be helped by the people of his place with silver, gold, goods, and livestock, along with voluntary offerings for the house of God in Jerusalem." Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”
5 Then the family heads of Judah and Benjamin, the priests and Levites—everyone whose spirit our Father had stirred—set out to go up and rebuild the house of our Father in Jerusalem. Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.
6 All their neighbors supported them with articles of silver and gold, goods, livestock, and valuable gifts, besides everything freely offered. Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija.
7 King Cyrus also brought out the articles of our Father's house that Nebuchadnezzar had taken from Jerusalem and put in his own gods' house. Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake.
8 Cyrus king of Persia had Mithredath the treasurer bring them out, counting them to Sheshbazzar the prince of Judah. Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.
9 This was their number: 30 gold basins, 1,000 silver basins, 29 incense burners, Chiwerengerochi chinali motere: Mabeseni agolide 30 mabeseni asiliva 1,000 a zopereka 29
10 30 gold bowls, 410 silver bowls of another kind, and 1,000 other articles. timiphika tagolide 230 timiphika tasiliva 410 ziwiya zina 1,000.
11 The gold and silver articles numbered 5,400. Sheshbazzar brought them all up when the exiles came up from Babylon to Jerusalem. Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]