Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Ecclesiastes 7 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 A good name is better than fine perfume, and the day of death than the day of birth. Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino, ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
2 It is better to go to the house of mourning than to go to the house of feasting, for that is the end of everyone, and the living should take it to heart. Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero: Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense; anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
3 Sorrow is better than laughter, for a sad face is good for the heart. Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka, pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima.
4 The heart of the wise is in the house of mourning, but the heart of fools is in the house of pleasure. Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa, koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.
5 It is better to hear the rebuke of the wise than to hear the song of fools. Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.
6 For like the crackling of thorns under a pot, so is the laughter of the fool. This too is fleeting. Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika, izinso ndi zopandapake.
7 Surely oppression turns a wise person into a fool, and a bribe corrupts the heart. Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru, ndipo chiphuphu chimawononga mtima.
8 The end of a matter is better than its beginning, and a patient spirit is better than a proud spirit. Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake, ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.
9 Do not be quick in your spirit to become angry, for anger settles in the lap of fools. Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako, pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.
10 Do not say, "Why were the former days better than these?" For it is not from wisdom that you ask this. Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?” pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.
11 Wisdom is good with an inheritance, an advantage to those who see the sun. Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12 For wisdom is a shelter, just as money is, but the advantage of knowledge is this: wisdom preserves the life of the one who has it. Nzeru ndi chitetezo, monganso ndalama zili chitetezo, koma phindu la chidziwitso ndi ili: kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.
13 Consider the work of God: who can straighten what he has made crooked? Taganizirani zimene Mulungu wazichita: ndani angathe kuwongola chinthu chimene Iye anachipanga chokhota?
14 In the day of prosperity be joyful, and in the day of adversity consider: God has made the one as well as the other, so that no one can find out anything that will come after them. Pamene zinthu zili bwino, sangalala; koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino: Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo, ndiponso nthawi imene si yabwinoyo. Choncho munthu sangathe kuzindikira chilichonse cha mʼtsogolo mwake.
15 In my fleeting days I've seen it all: a righteous man dying in his righteousness, a wicked man living long in his evil. Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi: munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake, ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake.
16 Do not be excessively righteous, and do not make yourself overly wise; why should you destroy yourself? Usakhale wolungama kwambiri kapena wanzeru kwambiri, udziwonongerenji wekha?
17 Don't be too wicked, and don't be foolish—why die before your time? Usakhale woyipa kwambiri, ndipo usakhale chitsiru, uferenji nthawi yako isanakwane?
18 Good to grasp this, and not let go of that too, for whoever fears God comes through both. Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi, ndipo usataye njira inayo. Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi.
19 Wisdom makes the wise person stronger than ten rulers who are in a city. Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzeru kupambana olamulira khumi a mu mzinda.
20 Surely there is no one righteous on earth who does good and never sins. Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.
21 Also, do not take to heart everything people say, or you may hear your servant cursing you, Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula, mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,
22 for your own heart knows that many times you yourself have cursed others. pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwako kuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena.
23 I tested all this by wisdom. I said, "I am determined to be wise"—but it was beyond me. Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati, “Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,” koma nzeruyo inanditalikira.
24 Whatever exists is far off and deep, very deep—who can discover it? Nzeru zimene zilipo, zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri, ndani angathe kuzidziwa?
25 I turned my heart to know, explore, and seek wisdom and the sum of things, and to know the evil of foolishness and the foolishness that is madness. Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa misala.
26 I find the woman more bitter than death: her heart is snares and nets, her hands chains. One good before God escapes her; the sinner is caught by her. Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa, mkazi amene ali ngati khoka, amene mtima wake uli ngati khwekhwe, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo, koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.
27 "See, this is what I found," says the Teacher, "adding one to another to find the sum, Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi: “Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira,
28 which my soul kept seeking but didn't find. One man in 1,000 I found, but a woman among all these I didn't find. pamene ine ndinali kufufuzabe koma osapeza kanthu, ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000, koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama.
29 Look, this alone I found: God made humanity upright, but they sought many schemes." Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi: Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama, koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]