Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Deuteronomy 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Moses called all Israel and said to them: "Listen, Israel, to the statutes and rulings I speak in your hearing today. Learn them and carefully do them." Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati: Tamverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuwuzeni lero. Muwaphunzire ndi kuonetsetsa kuti mukuwatsata.
2 Our Father made a covenant with us at Horeb. Yehova Mulungu wathu anachita pangano ndi ife ku Horebu.
3 This covenant our Father made not with our ancestors but with us—all of us alive here today. Yehova sanachite pangano ndi makolo athu koma ndi ife, tonse amene tili moyo lero.
4 Our Father spoke with you face to face at the mountain, from within the fire. Yehova anayankhula nanu maso ndi maso kuchokera mʼmoto pa phiri paja.
5 At that time I stood between our Father and you to tell you our Father's word, because you feared the fire and did not go up the mountain. He said: (Pa nthawi imeneyo ine ndinayimirira pakati pa Yehova ndi inu kuti ndikuwuzeni mawu a Yehova, chifukwa inu munkachita mantha ndi moto ndipo simunakwere ku phiri). Ndipo Iye anati:
6 "I am your Father, who brought you out of Egypt, the house of slavery. “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.
7 "You must have no other gods before me. “Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.
8 "Don't make yourself a carved image, any form of what's in the heavens above, on the earth below, or in the waters under the earth. “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko.
9 Do not bow to them or serve them, for I, your Father, am a jealous Father, charging the fathers' wrongdoing to the children, to the third and fourth generation of those who hate me, Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane,
10 but showing covenant love to 1,000 generations of those who love me and keep my commandments. koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.
11 "Do not misuse your Father's name, for our Father will not leave anyone who misuses his name unpunished. “Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.
12 "Observe the Sabbath day, to keep it holy, as your Father commanded you. “Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika monga momwe Yehova Mulungu wako anakulamulira.
13 Six days you are to labor and do all your work, Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi,
14 but the seventh day is a Sabbath to your Father. Do no work—you, your son or daughter, your male or female servant, your ox, donkey, or any livestock, or the foreigner in your towns—so your male and female servants may rest like you. koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi kapena wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu kapena ngʼombe yanu kapena bulu wanu kapena ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu, motero ndiye kuti wantchito wanu wamwamuna ndi wantchito wanu wamkazi adzapumula monga inuyo.
15 Remember you were a slave in Egypt, and your Father brought you out from there with a strong hand and outstretched arm. So your Father commanded you to keep the Sabbath day. Kumbukira kuti unali kapolo ku Igupto ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi lotambasuka. Choncho Yehova Mulungu wako akukulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata.
16 "Honor your father and your mother, as your Father commanded you, so your days are long and it goes well with you in the land your Father is giving you. “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
17 "You must not murder. “Usaphe.
18 "You must not commit adultery. “Usachite chigololo.
19 "You must not steal. “Usabe.
20 "You must not give false testimony against your neighbor. “Usapereke umboni womunamizira mnzako.
21 "Don't crave your neighbor's wife. Don't desire your neighbor's house, field, male or female servant, ox, donkey, or anything your neighbor owns." “Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”
22 These words our Father spoke to your whole assembly at the mountain, from within the fire, cloud, and deep darkness, in a loud voice; he added nothing more. He wrote them on two stone tablets and gave them to me. Awa ndi malamulo amene Yehova anayankhula ndi mawu okweza kwa gulu lanu lonse pa phiri paja mʼmoto, mtambo ndi mdima woopsa, sanawonjezerepo kanthu. Ndipo anawalemba pa mapale awiri amiyala ndi kundipatsa.
23 When you heard the voice from the darkness, the mountain blazing with fire, you came to me—all your tribal heads and elders, Mutamva mawu kuchokera mu mdimawo, phiri lili moto lawilawi, atsogoleri onse a mafuko anu ndi akuluakulu anu anabwera kwa ine.
24 and you said, "Look, our Father showed us his glory and greatness; we heard his voice from the fire. Today we saw our Father speak with a person, and that person still lives. Ndipo munati, “Yehova Mulungu wathu wationetsa ulemerero ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto. Lero taona kuti munthu akhoza kukhala ndi moyo ngakhale Mulungu atayankhula naye.
25 Now why should we die? This great fire will consume us. If we keep hearing our Father's voice any longer, we die. Koma tsopano tife chifukwa chiyani? Moto waukuluwu utinyeketsa, ndipo tifa tikapitirirabe kumva mawu a Yehova Mulungu wathu.
26 Who of all humanity has heard the living Father's voice speaking from inside the fire, like us, and lived? Pakuti ndi munthu uti wolengedwa amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo akuyankhula kuchokera mʼmoto, monga tachitiramu, nakhala ndi moyo?
27 Go near, hear all our Father says, then tell us all our Father tells you, and we will listen and obey." Pita pafupi kuti ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akunena. Kenaka udzatiwuze chilichonse chimene Yehova Mulungu wathu akunena ndipo tidzamvera ndi kuchita.”
28 Our Father heard your words to me, and our Father told me: "I heard this people's words to you. All they said is right. Yehova anakumvani pamene munkayankhula kwa ine ndipo Yehova anati kwa ine, “Ndamva zimene anthuwa anena kwa iwe. Chilichonse chimene anena ndi chabwino.
29 If only they kept this heart—fearing me and keeping all my commands always—so it goes well with them and their children forever! Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya.
30 Go and tell them, 'Return to your tents.' “Pita uwawuze kuti abwerere ku matenti awo.
31 But you, stand here with me, and I will tell you the whole command—the statutes and judgments—you are to teach them, so they will do them in the land I am giving them to possess." Koma iwe ukhale kuno ndi ine kuti ndikupatse malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene azitsatira mʼdziko limene ndiwapatse kuti alitenge.”
32 So be careful to do as your Father commanded you; do not turn aside right or left. Choncho samalirani kuchita zimene Yehova Mulungu wanu akukulamulirani inu, musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.
33 Walk the whole way your Father commanded, to live, thrive, and last long in the land you will possess. Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]