Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Deuteronomy 4 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Now, Israel, listen to the statutes and rules I am teaching you to follow, so you may live and go take possession of the land your Father, the God of your ancestors, is giving you. Mverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuphunzitseni. Muwatsatire kuti mukhale ndi moyo ndi kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani.
2 Do not add to the word I command you, or take from it, so you keep the commandments of your Father that I command you. Musawonjezere pa zimene ndikukulamulirani ndipo musachotserepo, koma muwasunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.
3 Your own eyes saw what your Father did at Baal-peor: he destroyed from among you every man who followed the Baal of Peor. Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita ku Baala-Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga aliyense amene anatsata Baala wa ku Peori pakati panu.
4 But you who held fast to your Father, the LORD, are all alive today. Koma inu nonse amene munagwiritsitsa Yehova Mulungu wanu mukanali ndi moyo mpaka lero.
5 See, I taught you statutes and rules, as your Father commanded me, to do them in the land you are entering to possess. Taonani, ndakuphunzitsani malangizo ndi malamulo monga Yehova Mulungu wanga anandilamulira kuti inuyo muwatsatire mʼdziko limene mukulowa ndi kulitengali.
6 Keep and do them; this is your wisdom and understanding before the nations, who will hear all these decrees and say, 'This great nation is truly a wise and understanding people.' Muwasunge mosamalitsa pakuti zimenezi zidzaonetsa nzeru zanu ndi kuzindikira kwanu kwa anthu a mitundu ina, amene adzamva za malangizo onsewa nati, “Ndithudi, mtundu waukulu uwu ndi wa anthu anzeru ndi ozindikira.”
7 What great nation has a god as near to it as your Father is to us whenever we call on him? Mtundu wina wa anthu ndi uti umene uli waukulu chomwechi, woti ukhoza kukhala ndi milungu yawo pafupi monga mmene alili Yehova Mulungu wathu ndi ife nthawi zonse pamene tipemphera kwa Iye?
8 What great nation has statutes and rules as just as all this law I set before you today? Ndipo ndi mtundu uti mwa mitundu ya anthu umene ndi waukulu chotere kuti nʼkukhala ndi malangizo ndi malamulo olungama ngati malamulo amene ndikuyika pamaso panu lero?
9 Only be careful and watch yourself closely, so you do not forget what your eyes have seen, and they do not leave your heart all your days. Make them known to your children and your children's children. Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo.
10 Remember the day you stood before your Father at Horeb, when he told me, "Gather the people to me, and I will let them hear my words, so they learn to fear me all the days they live on the earth, and teach their children." Kumbukirani tsiku limene munayimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebu, pamene anati kwa ine, “Sonkhanitsa anthu pamaso panga kuti amve mawu anga ndi kuti aphunzire kundilemekeza mʼmoyo wawo onse mʼdzikomo ndi kuti ana awo aziwaphunzitsa zimenezi.”
11 You came near and stood at the mountain's foot while it burned with fire to the heart of heaven—wrapped in darkness, cloud, and deep gloom. Munabwera pafupi ndi kuyima pa tsinde pa phiri pamene phirilo limayaka moto umene umafika mpaka kumwamba. Panalinso mtambo wakuda ndi mdima wambiri.
12 Your Father spoke to you from within the fire. You heard the sound of words but saw no form—only a voice. Kenaka Yehova anayankhula nanu kuchokera mʼmotowo. Inu munamva mawu ake okha koma simunamuone pakuti panali mawu chabe.
13 He declared his covenant to you, commanding you to keep it—the Ten Words—and wrote them on two stone tablets. Iye anakuwuzani Malamulo Khumi omwe ndi pangano lake limene anakulamulirani kuti mutsatire. Ndipo anawalemba malamulowo pa mapale awiri a miyala.
14 And your Father commanded me then to teach you statutes and rules to follow in the land you are crossing to possess. Ndipo Yehova anandilamula nthawi imene ija kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi malamulo amene muyenera kutsata mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani.
15 So watch yourselves very carefully, since you saw no form the day your Father spoke to you at Horeb from the fire, Tsiku limene Yehova anayankhula nanu ku Horebu mʼmoto uja, simunaone thupi lake. Choncho mudziyangʼanire nokha mosamalitsa,
16 be careful not to act corruptly by making a carved image for yourselves, in the form of any figure, the likeness of male or female, kuti musasokonezeke ndi kudzipangira nokha fano kapena chifanizo cha mtundu uliwonse, kaya chokhala ngati mwamuna kapena ngati mkazi,
17 the likeness of any animal on the earth, the likeness of any winged bird that flies in the sky, kaya chokhala ngati nyama iliyonse ya pa dziko lapansi kapena mbalame iliyonse yowuluka mlengalenga.
18 the likeness of anything that creeps on the ground, of any fish in the water below the earth. Kapena cholengedwa chilichonse choyenda pa nthaka kapena nsomba ya mʼmadzi akuya.
19 And do not lift your eyes to the heavens and, seeing the sun, moon, and stars—all the host of heaven—be drawn away to bow to them and serve them, which your Father allotted to all peoples under the whole heaven. Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi.
20 Your Father took you and brought you out of Egypt, the iron furnace, to be his own people, his inheritance, as you are today. Koma inuyo, Yehova anakutengani ndi kukutulutsani mʼngʼanjo yosungunulira zitsulo, ku Igupto kuti mukhale anthu olandira chuma chake monga mmene mulili tsopano.
21 Now your Father was angry with me because of you and swore I would not cross the Jordan or enter the good land your Father is giving you to inherit. Yehova anakwiya nane chifukwa cha inu, ndipo analumbira kwathunthu kuti sindidzawoloka Yorodani ndi kulowa mʼdziko labwinolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani inu ngati cholowa chanu.
22 I must die in this land; I will not cross the Jordan. But you are crossing to take that good land. Ine ndifera mʼdziko lino, sindiwoloka Yorodani. Koma inu mwatsala pangʼono kuwoloka ndi kukatenga dziko labwinolo.
23 Be careful not to forget the covenant your Father made with you, and make a carved image in the form of anything your Father has forbidden you. Samalani, musayiwale pangano limene Yehova Mulungu wanu anapangana nanu ndipo musadzipangire nokha fano la chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu waletsa.
24 For your Father is a consuming fire, a jealous Father. Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.
25 When you have children and grandchildren and have grown old in the land, if you act wickedly by making a carved image in the form of anything, and do what is evil in your Father's sight, provoking him to anger, Mukadzakhala nthawi yayitali mʼdzikomo ndi kubereka ana ndi kukhala ndi zidzukulu ndipo mukadzasokonekera ndi kupanga fano la mtundu uliwonse, nʼkumachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kumukwiyitsa,
26 today I call heaven and earth to witness against you: you'll soon perish completely from the land you cross the Jordan to possess. Your days there will be few; you'll be totally wiped out. ine ndi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni lero zokutsutsani kuti mudzawonongedwa msanga ndipo mudzachotsedwa mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani. Simudzakhalitsa kumeneko koma mudzawonongedwa ndithu.
27 Your Father will scatter you among the peoples, and you will be left few in number among the nations where your Father drives you. Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu ena. Ochepa okha pakati panu ndi amene adzapulumuke pakati pa anthu a mitundu ina kumene Yehova adzakupirikitsireniko.
28 There you will serve gods of wood and stone, the work of human hands, that cannot see, hear, eat, or smell. Kumeneko mudzapembedza milungu ya mitengo ndi miyala yopangidwa ndi anthu, imene singaone kapena kumva kapena kudya kapena kununkhiza.
29 But from there you will seek your Father and find him, if you search for him with all your heart and soul. Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
30 When you are in distress and all these things come upon you in later days, you will return to your Father and obey his voice. Mukadzakhala pa chipsinjo ndipo zonsezi zikadzakuchitikirani, ndi pamene pambuyo pake mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera Iye.
31 Your Father is a merciful Father; he will not abandon you, destroy you, or forget the covenant he swore to your ancestors. Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo, Iye sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuyiwala pangano lake ndi makolo anu, limene analitsimikiza mwa lumbiro.
32 Look back over the days long past, since our Father created humanity on the earth, and ask from one end of heaven to the other: has anything this great ever happened or been heard of? Tsopano tafunsani za masiku a mʼmbuyomu, zakale inu musanabadwe, kuyambira tsiku limene Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani kuyambira kumapeto mpaka mapeto anzake a thambo. Kodi chinachitikako china chachikulu ngati ichi, kapena chinayamba chamvekako chokhala ngati ichi?
33 Has any people heard a god's voice speaking from within fire, as you have, and lived? Kodi uliponso mtundu wina wa anthu umene unamva mawu a Mulungu akuyankhula kuchokera mʼmoto nʼkukhala ndi moyo monga mwachitira inumu?
34 Or has any god dared to take a nation out of another nation for himself, by trials, signs, wonders, war, a mighty hand, an outstretched arm, and great terrors, according to all that your Father did for you in Egypt before your eyes? Kodi alipo mulungu amene anayeserapo kudzitengera mtundu wa anthu kuwachotsa mu mtundu unzake mwa mayesero, zizindikiro zozizwitsa, nkhondo, komanso mwa mphamvu zake zopanda malire, kapena mwa zochita zazikulu ndi zochititsa mantha, monga zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Igupto inu mukupenya?
35 It was shown to you, so you would know our Father is the Father; there is no other besides him. Iye anakuonetsani zonsezi kuti inu muzindikire kuti Yehova ndiye Mulungu, palibenso wina wofanana naye.
36 From heaven he made you hear his voice to discipline you; on earth he showed you his great fire, and you heard his words from within the fire. Kuchokera kumwamba, Iye anafuna kuti inu mumve mawu ake ndi kuti mukhale osunga mwambo. Pa dziko lapansi anakuonetsani moto waukulu, ndipo inu munamva mawu ake kuchokera mʼmotomo.
37 Because he loved your ancestors and chose their descendants after them, he brought you out of Egypt himself, by his great power, Popeza anakonda makolo anu ndi kusankha adzukulu awo, a pambuyo pawo, anakutulutsani kuchoka ku Igupto ali pakati panu ndi mphamvu yake,
38 driving out before you nations greater and stronger than you, to bring you in and give you their land as an inheritance, as it is today. kuti akupirikitsireni mayiko akuluakulu ndi amphamvu kuposa inu, ndi kukubweretsani inu ku dziko lawo kuti likhale lanu, monga liliri lero.
39 Know today, and take it to heart, that our Father is the Father in heaven above and on the earth below; there is no other. Vomerezani lero ndipo dziwani mu mtima mwanu kuti Yehova ndiye Mulungu kumwamba ndi pa dziko lapansi. Palibenso wina.
40 Keep his statutes and commandments, which I command you today, so it goes well with you and your children after you, and you live long in the land your Father gives you for all time. Sungani malangizo ake ndi malamulo ake amene ndikukupatsani lero lino, kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana anu kutsogoloko, ndi kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kwa nthawi zonse.
41 Then Moses set apart three cities in the region beyond the Jordan toward the sunrise, Kenaka Mose anapatula mizinda itatu cha kummawa kwa Yorodani,
42 so anyone who killed his neighbor unintentionally, without having hated him before, could flee to one of these cities and live: kumene aliyense amene wapha munthu akhoza kuthawirako ngati wopha munthuyo sanaphe mnzakeyo mwadala ndi maganizo oyipa. Iye akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi napulumutsa moyo wake.
43 Bezer in the wilderness on the plateau for the Reubenites, Ramoth in Gilead for the Gadites, and Golan in Bashan for the Manassites. Mizindayo inali iyi: ku fuko la Rubeni, unali mzinda wa Bezeri ku mapiri a ku chipululu; ku fuko la Gadi, unali Ramoti ku Giliyadi; ndipo ku fuko la Manase, unali Golani ku Basani.
44 This is the law that Moses set before the people of Israel. Awa ndi malamulo amene Mose anapereka kwa Aisraeli.
45 These are the testimonies, statutes, and rules Moses spoke to Israel when they came out of Egypt. Izi ndi ndondomeko, malangizo ndi malamulo amene Mose anawapatsa iwo pamene anatuluka ku Igupto.
46 East of the Jordan, in the valley opposite Beth-peor, in the land of Sihon the Amorite king who lived in Heshbon, whom Moses and Israel defeated after leaving Egypt. Anali ku chigwa cha kufupi ndi Beti-Peori mbali ya kummawa kwa Yorodani, mʼdziko la Sihoni mfumu ya Aamori amene ankalamulira ku Hesiboni ndipo anagonjetsedwa ndi Mose ndi Aisraeli pamene ankachokera ku Igupto.
47 They took possession of his land and the land of Og king of Bashan, the two Amorite kings who lived beyond the Jordan toward the sunrise, Iye anamulanda dziko lake ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. Awa anali mafumu awiri Aamori a kummawa kwa Yorodani.
48 from Aroer on the edge of the Arnon Valley to Mount Sion (that is, Hermon), Dziko ili linayambira ku Aroeri cha kumphepete kwa khwawa la Arinoni ku phiri la Siyoni (limeneli ndi phiri la Herimoni),
49 with all the Arabah beyond the Jordan eastward, to the Sea of the Arabah, below the slopes of Pisgah. ndi kuphatikizapo dziko lonse la Araba cha kummawa kwa Yorodani mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, kumunsi kwa Phiri la Pisiga.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]