Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Amos 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Hear this word that I raise as a lament over you, house of Israel: Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:
2 Fallen, never to rise again, is the virgin Israel; she lies abandoned on her own land, with no one to raise her up. “Namwali Israeli wagwa, moti sadzadzukanso, wasiyidwa mʼdziko lake lomwe, popanda woti ndi kumudzutsa.”
3 For the Sovereign Father says: The city that marches out 1,000 will have one hundred left; the one marching out one hundred will have ten left—for the house of Israel. Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”
4 For this is what our Father says to the house of Israel: Seek me and live. Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi: “Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;
5 But do not seek Bethel, do not go to Gilgal, do not cross over to Beersheba; for Gilgal will surely go into exile, and Bethel will come to nothing. musafunefune Beteli, musapite ku Giligala, musapite ku Beeriseba. Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, ndipo Beteli adzawonongekeratu.”
6 Seek our Father and live, or he will sweep like fire through the house of Joseph; it will devour, with no one to quench it for Bethel. Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo, mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto; motowo udzawononga, ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.
7 You who turn justice into bitter poison and throw righteousness to the ground. Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa ndi kunyoza chilungamo.
8 He who made the Pleiades and Orion, who turns deep darkness into morning and darkens day into night, who summons the waters of the sea and pours them out over the face of the earth—our Father is his name. (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake.
9 He flashes destruction on the strong, and ruin comes upon the fortress. Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),
10 They hate the one who reproves in the gate, and they despise the one who speaks the truth. inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu ndi kunyoza amene amanena zoona.
11 Therefore, because you trample on the poor and exact from him a tax of grain, you have built houses of cut stone, but you will not live in them; you have planted lovely vineyards, but you will not drink their wine. Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake.
12 For I know how many are your offenses and how great your sins—you who afflict the righteous and take bribes and push aside the needy in the gate. Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.
13 Therefore the prudent keep silent in such a time, for it is an evil time. Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu, popeza ndi nthawi yoyipa.
14 Seek good and not evil, that you may live; and so the Father of heaven's armies will be with you, just as you have claimed. Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa, kuti mukhale ndi moyo. Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu, monga mmene mumanenera kuti ali nanu.
15 Hate evil and love good, and establish justice in the gate; perhaps the Father of heaven's armies will be gracious to the remnant of Joseph. Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino; mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu. Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.
16 So the Father of heaven's armies says: In every square, wailing; in every street, they cry, "Alas! Alas!" They call the farmer to mourning, and those skilled in lament to wailing. Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena: “Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula, ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse. Adzayitana alimi kuti adzalire, ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.
17 In all the vineyards there will be wailing, for I will pass through your midst, says our Father. Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,” akutero Yehova.
18 Woe to you who long for the day of our Father! Why would you want the day of our Father? It is darkness, not light. Tsoka kwa inu amene mumalakalaka tsiku la Yehova! Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova? Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.
19 It will be as if a man fled from a lion only to meet a bear, or went into his house and rested his hand on the wall only to be bitten by a snake. Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango amakumana ndi chimbalangondo, ngati pamene munthu walowa mʼnyumba, natsamira dzanja lake pa khoma ndipo njoka nʼkuluma.
20 Will not the day of our Father be darkness, not light—pitch-dark, with no brightness in it? Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala, mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?
21 I hate, I despise your festivals; I take no delight in your solemn assemblies. “Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza; sindikondwera nayo misonkhano yanu.
22 Even if you offer me burnt offerings and your grain offerings, I will not accept them; and the peace offerings of your fattened animals I will not even look at. Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya, Ine sindidzazilandira. Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano, Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.
23 Take away from me the noise of your songs; I will not listen to the music of your harps. Musandisokose nazo nyimbo zanu! Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.
24 But let justice roll down like waters, and righteousness like an ever-flowing stream. Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi, chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!
25 Did you bring me sacrifices and offerings those forty years in the wilderness, house of Israel? “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?
26 You have lifted up Sikkuth your king and Kiyyun your star-god, the images you made for yourselves. Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene munadzipangira.
27 So I will send you into exile beyond Damascus, says our Father—the Father of heaven's armies is his name. Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,” akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]