Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Timothy 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 First of all, then, I urge that petitions, prayers, intercessions, and thanksgivings be offered for all people, Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika.
2 for kings and all in authority, so we may live peaceful, quiet lives in full godliness and dignity. Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.
3 This is good and pleasing to our Father, our Savior, Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu,
4 who wants all people to be saved and to come to know the truth. amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.
5 For there is one Father, and one mediator between the Father and humanity, the man Christ Jesus, Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.
6 who gave himself as a ransom for all—the testimony given at the proper time. Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera.
7 For this I was made a preacher and apostle—I'm telling the truth, not lying—a teacher of the nations in faith and truth. Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.
8 I want the men in every place to pray, lifting up holy hands without anger or argument. Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.
9 Likewise, women should dress properly, with modesty and self-control, not in braided hair, gold, pearls, or costly clothing, Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.
10 but with good works, as is right for women who profess reverence for our Father. Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.
11 A woman should learn quietly, in full submission. Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu.
12 I don't allow a woman to teach or have authority over a man; instead, she should stay quiet. Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete.
13 For Adam was formed first, then Eve. Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava.
14 And Adam was not deceived, but the woman was deceived and became a transgressor. Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa.
15 But she will be saved through childbearing, if they remain in faith, love, holiness, with self-control. Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]