Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 24 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 These are the divisions of Aaron's sons. Aaron's sons: Nadab and Abihu, Eleazar and Ithamar. Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
2 Nadab and Abihu died before their father, leaving no sons; so Eleazar and Ithamar served as priests. Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe.
3 David divided them with Zadok, Eleazar's descendant, and Ahimelech, Ithamar's descendant, by their appointed service order. Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira.
4 Eleazar's sons were found to have more leaders than Ithamar's, so they were divided: sixteen family heads for Eleazar's, eight for Ithamar's, by their families. Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara.
5 They divided them by lot, both alike, since officials of the sanctuary and officials of our Father came from the sons of Eleazar and the sons of Ithamar. Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.
6 Shemaiah son of Nethanel, a Levite scribe, wrote them before the king, the officials, Zadok the priest, Ahimelech son of Abiathar, and the heads of the priestly and Levite families—one family chosen for Eleazar, one for Ithamar. Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.
7 The first lot fell to Jehoiarib, the second to Jedaiah, Maere woyamba anagwera Yehoyaribu, achiwiri anagwera Yedaya,
8 the third to Harim, the fourth to Seorim, achitatu anagwera Harimu, achinayi anagwera Seorimu,
9 the fifth to Malchijah, the sixth to Mijamin, achisanu anagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,
10 the seventh to Hakkoz, the eighth to Abijah, achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,
11 the ninth to Jeshua, the tenth to Shecaniah, achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa, a khumi anagwera Sekaniya,
12 the eleventh to Eliashib, the twelfth to Jakim, a 11 anagwera Eliyasibu, a 12 anagwera Yakimu,
13 the thirteenth to Huppah, the fourteenth to Jeshebeab, a 13 anagwera Hupa, a 14 anagwera Yesebeabu,
14 the fifteenth to Bilgah, the sixteenth to Immer, a 15 anagwera Biliga, a 16 anagwera Imeri,
15 the seventeenth to Hezir, the eighteenth to Happizzez, a 17 anagwera Heziri, a 18 anagwera Hapizezi,
16 the nineteenth to Pethahiah, the twentieth to Jehezkel, a 19 anagwera Petahiya, a 20 anagwera Ezekieli,
17 the twenty-first to Jachin, the twenty-second to Gamul, a 21 anagwera Yakini, a 22 anagwera Gamuli,
18 the twenty-third to Delaiah, and the twenty-fourth to Maaziah. a 23 anagwera Delaya, ndipo a 24 anagwera Maaziya.
19 These were their appointed duties for serving in our Father's house, by the order Aaron their father gave them, as our Father of Israel had commanded him. Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.
20 The rest of Levi's sons: of Amram's sons, Shubael; of Shubael's sons, Jehdeiah. Za zidzukulu zina zonse za Levi: Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli; kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.
21 Of Rehabiah: of the sons of Rehabiah, Isshiah the first. Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake: Mtsogoleri anali Isiya.
22 Of the Izharites, Shelomoth; of the sons of Shelomoth, Jahath. Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti; kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.
23 The sons of Hebron: Jeriah the first, Amariah the second, Jahaziel the third, Jekameam the fourth. Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.
24 The sons of Uzziel: Micah; of the sons of Micah, Shamir. Mwana wa Uzieli: Mika; kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.
25 The brother of Micah: Isshiah; of the sons of Isshiah, Zechariah. Mʼbale wa Mika: Isiya; kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.
26 The sons of Merari: Mahli and Mushi. The sons of Jaaziah: Beno. Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Mwana wa Yaaziya: Beno.
27 The sons of Merari through Jaaziah: Beno, Shoham, Zaccur, and Ibri. Ana a Merari: Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.
28 Of Mahli: Eleazar, who had no sons. Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.
29 Of Kish: the sons of Kish, Jerahmeel. Kuchokera kwa Kisi: Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.
30 The sons of Mushi: Mahli, Eder, and Jerimoth. These were the Levites by their families. Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti. Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo.
31 They too cast lots, like their relatives the sons of Aaron, before King David, Zadok, Ahimelech, and the heads of the priestly and Levite families—the head of each family the same as his younger brother. Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]