Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 23 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 When David was old and had lived many years, he made his son Solomon king over Israel. Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.
2 He gathered together all the leaders of Israel, along with the priests and the Levites. Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi.
3 The Levites thirty years old or older were counted, and their total number was 38,000. Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000.
4 Of these, 24,000 were to oversee the work of our Father's house; 6,000 were officers and judges. Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza.
5 4,000 were gatekeepers, and 4,000 praised our Father with instruments David made for praise. Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”
6 And David divided them into divisions according to the sons of Levi: Gershon, Kohath, and Merari. Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
7 Of the Gershonites: Ladan and Shimei. Ana a Geresoni: Ladani ndi Simei.
8 The sons of Ladan: Jehiel the chief, then Zetham and Joel, three in all. Ana a Ladani: Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.
9 Shimei's sons: Shelomoth, Haziel, and Haran—three. These were Ladan's family heads. Ana a Simei: Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu. Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.
10 And the sons of Shimei: Jahath, Zina, Jeush, and Beriah. These four were the sons of Shimei. Ndipo ana a Simei anali: Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya. Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.
11 Jahath was chief, Zizah second; Jeush and Beriah had few sons, so they were counted together as one family, one assignment. Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.
12 The sons of Kohath: Amram, Izhar, Hebron, and Uzziel, four in all. Ana a Kohati: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.
13 The sons of Amram: Aaron and Moses. Aaron was set apart to consecrate the most holy things, he and his sons forever, to make offerings before our Father, to serve him, and to bless in his name forever. Ana a Amramu: Aaroni ndi Mose. Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya.
14 But Moses, man of our Father—his sons were counted among Levi's tribe. Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.
15 The sons of Moses: Gershom and Eliezer. Ana a Mose: Geresomu ndi Eliezara.
16 The sons of Gershom: Shebuel the chief. Zidzukulu za Geresomu: Mtsogoleri anali Subaeli.
17 Eliezer's sons: Rehabiah the chief. Eliezer had no other sons; Rehabiah's sons were very numerous. Zidzukulu za Eliezara: Mtsogoleri anali Rehabiya. Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.
18 The sons of Izhar: Shelomith the chief. Ana a Izihari: Mtsogoleri anali Selomiti.
19 The sons of Hebron: Jeriah the chief, Amariah the second, Jahaziel the third, and Jekameam the fourth. Ana a Hebroni: Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.
20 The sons of Uzziel: Micah the chief and Isshiah the second. Ana a Uzieli: Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.
21 The sons of Merari: Mahli and Mushi. The sons of Mahli: Eleazar and Kish. Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Ana a Mahili: Eliezara ndi Kisi.
22 Eleazar died having no sons, only daughters; so their relatives, the sons of Kish, married them. Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.
23 The sons of Mushi: Mahli, Eder, and Jeremoth, three in all. Ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.
24 These were Levi's sons by family, family heads registered by name, who served in our Father's house, age twenty and up. Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova.
25 For David said, "Our Father, Israel's God, gave his people rest, and lives in Jerusalem forever. Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya,
26 So the Levites no longer carry the tabernacle or all its service vessels." sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.”
27 For by these final instructions of David the Levites were counted from twenty years old or older. Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.
28 Their duty was assisting Aaron's sons in serving the house of our Father: caring for the courts and the chambers, purifying all holy things, and any work in the house of our Father. Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu.
29 They cared for the Bread of the Presence, the fine flour for grain offerings, wafers made without yeast, the baking and mixing, and all measures of quantity and size. Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake.
30 They were to stand every morning to thank and praise our Father, and again in the evening, Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo,
31 and for all burnt offerings to our Father on Sabbaths, new moons, and appointed feasts—in the required number, always before our Father. ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.
32 They kept the charge of the tent of meeting, the charge of the sanctuary, and the charge of their brothers, Aaron's sons, in the service of the house of our Father. Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]