Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 18 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 After this, David defeated the Philistines, subduing them, and took Gath and its villages from the Philistines' hand. Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Iye analanda Gati ndi midzi yake yozungulira mʼmanja mwa Afilistiwo.
2 He also defeated Moab, and the Moabites became subject to David and brought him tribute. Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye.
3 David defeated Hadadezer king of Zobah, up to Hamath, going to extend his power to the Euphrates River. Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
4 David captured from him 1,000 chariots, 7,000 horsemen, and 20,000 foot soldiers. He hamstrung all the chariot horses, keeping enough for one hundred chariots. Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.
5 When Aram of Damascus came to help Hadadezer king of Zobah, David struck down 22,000 Arameans. Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000.
6 David placed garrisons in Aram-Damascus; the Arameans became his servants, paying tribute. And our Father gave David victory wherever he went. Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.
7 David took the gold shields carried by Hadadezer's officers and brought them to Jerusalem. Davide anatenga zishango zagolide zimene ankanyamula akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu.
8 From Tibhath and Cun, Hadadezer's cities, David took huge amounts of bronze; with it Solomon made the bronze Sea, the pillars, and bronze vessels. Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa.
9 When Tou king of Hamath heard David had defeated Hadadezer king of Zobah's whole army, Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri mfumu ya Zoba,
10 he sent his son Hadoram to King David to greet and bless him for fighting and defeating Hadadezer, who had often warred with Tou. Hadoram brought gold, silver, and bronze articles of every kind. anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa.
11 King David dedicated these to our Father, with the silver and gold he had taken from all the nations: Edom, Moab, the Ammonites, the Philistines, and Amalek. Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki.
12 Abishai son of Zeruiah struck down 18,000 Edomites in the Valley of Salt. Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere.
13 David placed garrisons in Edom; all Edomites became his subjects, and our Father gave him victory wherever he went. Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.
14 So David reigned over all Israel, administering justice and righteousness for all his people. Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse.
15 Joab son of Zeruiah commanded the army; Jehoshaphat son of Ahilud was recorder; Yowabu, mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika;
16 Zadok son of Ahitub and Ahimelech son of Abiathar were priests; Shavsha was secretary; Zadoki, mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Savisa anali mlembi;
17 Benaiah son of Jehoiada led the Cherethites and Pelethites; David's sons served as top officials beside the king. Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali alangizi a mfumu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]