Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 12 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 These are the men who came to David at Ziklag while he was still banned from Saul son of Kish's presence—mighty warriors who helped him in battle. Nawa anthu amene anabwera kwa Davide ali ku Zikilagi pamene iye anathamangitsidwa ndi Sauli mwana wa Kisi (iwowo anali mʼgulu la asilikali amene ankamuthandiza pa nkhondo.
2 Armed with bows, able to sling stones or shoot arrows with right hand or left—Benjaminites, Saul's relatives. Iwo anali ndi mauta ndipo amadziwa kuponya mivi komanso miyala, ndipo amatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwo anali abale ake a Sauli ochokera ku fuko la Benjamini.
3 Ahiezer the chief, then Joash, sons of Shemaah of Gibeah; Jeziel and Pelet, sons of Azmaveth; Beracah; Jehu of Anathoth; Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri ndi Yowasi ana a Semaya wa ku Gibeya; Yezieli ndi Peleti ana a Azimaveti; Beraka, Yehu wa ku Anatoti,
4 Ishmaiah of Gibeon, a mighty warrior among the thirty, commander over the thirty; Jeremiah, Jahaziel, Johanan, Jozabad of Gederah; ndi Isimaiya wa ku Gibiyoni, munthu wamphamvu mʼgulu la anthu makumi atatu aja, yemwenso anali mtsogoleri wawo; Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gederi,
5 Eluzai, Jerimoth, Bealiah, Shemariah, and Shephatiah the Haruphite; Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya ndi Sefatiya Mharufi;
6 Elkanah, Isshiah, Azarel, Joezer, and Jashobeam, the Korahites; Elikana, Isiya, Azareli, Yowezeri ndi Yasobeamu a ku banja la Kora;
7 and Joelah and Zebadiah, the sons of Jeroham of Gedor. ndi Yowela ndi Zebadiya ana a Yerohamu wa ku Gedori.
8 Some Gadites defected to David at the wilderness stronghold—mighty warriors trained for battle, skilled with shield and spear, faces like lions, swift as gazelles on the mountains. Asilikali ena a fuko la Gadi anathawira kwa Davide ku linga lake ku chipululu. Iwo anali asilikali olimba mtima, okonzekera nkhondo ndipo amadziwa kugwiritsa ntchito chishango ndi mkondo. Iwowo anali woopsa ngati mikango ndipo anali aliwiro ngati ngoma zamʼmapiri.
9 Ezer was the chief, Obadiah second, Eliab third, Mtsogoleri wawo anali Ezeri, wotsatana naye anali Obadiya, wachitatu anali Eliabu,
10 Mishmannah fourth, Jeremiah fifth, wachinayi anali Misimana, Yeremiya anali wachisanu,
11 Attai sixth, Eliel seventh, wachisanu ndi chimodzi anali Atai, Elieli anali wachisanu ndi chiwiri,
12 Johanan eighth, Elzabad ninth, wachisanu ndi chitatu anali Yohanani, Elizabadi anali wachisanu ndi chinayi,
13 Jeremiah tenth, Machbannai eleventh. wakhumi anali Yeremiya ndipo Makibanai anali wa 11.
14 These Gadites were army commanders; the least matched 100, and the greatest 1,000. Anthu a fuko la Gadi amenewa anali atsogoleri; angʼonoangʼono amalamulira anthu 100 pamene akuluakulu amalamulira anthu 1,000.
15 These were the men who crossed the Jordan in the first month, when it overflowed all its banks, and routed everyone in the valleys, east and west. Awa ndi amene anawoloka Yorodani mwezi woyamba pamene mtsinje unali utasefukira mbali zonse, ndipo anathamangitsa aliyense amene amakhala mʼchigwa, mbali ya kumadzulo ndi kummawa.
16 Some of the men of Benjamin and Judah also came to David at the stronghold. Anthu ena a fuko la Benjamini ndi ena ochokera ku Yuda anabweranso kwa Davide pamene anali ku linga lake.
17 David went out to meet them and said to them, "If you have come to me in peace to help me, my heart will join with you; but if to betray me to my enemies, though my hands hold no violence, may the God of our fathers see it and judge you." Davide anapita kukakumana nawo ndipo anati, “Ngati mwabwera kwa ine mwamtendere, kuti mundithandize, ndakonzeka kugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, ngakhale kuti sindinalakwe, Mulungu wa makolo anthu aone izi ndipo akuweruzeni.”
18 Then the Spirit of our Father clothed Amasai, chief of the thirty, who said: "We are yours, David! We are with you, son of Jesse! Peace, peace to you, peace to your helpers, for your Father helps you." David received them, making them leaders of his raiders. Kenaka Mzimu anabwera pa Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja ndipo anati: “Inu Davide, ife ndife anu! Tili nanu limodzi, inu mwana wa Yese! Kupambana, Kupambana kwa inu, ndiponso kupambana kukhale kwa iwo amene akukuthandizani pakuti Mulungu wanu adzakuthandizani.” Kotero Davide anawalandira ndipo anawayika kukhala atsogoleri a magulu ake a ankhondo.
19 Some from Manasseh defected to David when he marched with the Philistines against Saul. But David and his men gave the Philistines no help—after consulting, the Philistine rulers sent David away, saying, "He'll defect to his master Saul, costing us our heads." Anthu ena a fuko la Manase anathawira kwa Davide pamene anapita ndi Afilisti kukamenyana ndi Sauli. (Iye ndi anthu ake sanathandize Afilisti chifukwa, atsogoleri awo atakambirana, anamubweza Davide. Iwo anati, “Ife tidzawonongedwa ngati uyu adzabwerera kwa mbuye wake Sauli).”
20 Going to Ziklag, these from Manasseh defected to him: Adnah, Jozabad, Jediael, Michael, Jozabad, Elihu, Zillethai—commanders of Manasseh's thousands. Davide atapita ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase amene anathawira kwa iye anali awa: Adina, Yozabadi, Yediaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai; atsogoleri a magulu a anthu 1,000 a ku Manase.
21 They helped David against the raiders, for all were mighty warriors, and became commanders in his army. Iwowa anathandiza Davide kulimbana ndi magulu achifwamba, pakuti onsewa anali asilikali olimba mtima ndipo anali atsogoleri mʼgulu lake la ankhondo.
22 Day after day men came to help David, until he had an army as great as our Father's army. Tsiku ndi tsiku anthu amabwera kudzathandiza Davide, mpaka anakhala ndi gulu lalikulu la ankhondo, ngati gulu la ankhondo a Mulungu.
23 These are the counts of men armed for battle who came to David at Hebron to turn Saul's kingdom over to him, just as our Father had said, Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene anabwera kwa Davide ku Hebroni kudzapereka ufumu wa Sauli kwa iye, monga momwe ananenera Yehova:
24 from Judah, carrying shield and spear—6,800 armed for battle; Anthu a fuko la Yuda onyamula chishango ndi mkondo analipo 6,800;
25 from Simeon, mighty warriors ready for battle—7,100; Anthu a fuko la Simeoni, asilikali okonzekera nkhondo analipo 7,100;
26 from Levi—4,600, Anthu a fuko la Levi analipo 4,600,
27 with Jehoiada, leader of the family of Aaron, and 3,700 with him, mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aaroni anabweranso ndi anthu 3,700,
28 and Zadok, a brave young warrior, with twenty-two officers from his own family. ndi Zadoki, mnyamata wankhondo wolimba mtima, anabwera ndi akuluakulu 22 ochokera mʼbanja lake;
29 From Benjamin, Saul's relatives—3,000; most had still kept guard for Saul's house, Anthu a fuko la Benjamini, abale ake a Sauli analipo 3,000 ndipo ambiri anali ndi Sauli ku nyumba yake pa nthawiyi;
30 from Ephraim—20,800, mighty warriors, famous men in their own families; Anthu a fuko la Efereimu, asilikali olimba mtima, otchuka pa mabanja awo analipo 20,800;
31 from the half-tribe of Manasseh—18,000, designated by name to come and make David king; Anthu a fuko latheka la Manase amene anawayitana kuti adzakhazikitse nawo ufumu wa Davide analipo 18,000;
32 from Issachar: 200 chiefs who understood the times, knew what Israel should do, with all their relatives at their command. Anthu a fuko la Isakara amene ankazindikira nthawi ndipo amadziwa zimene Israeli ankayenera kuchita, analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi abale awo onse amene amawatsogolera.
33 From Zebulun: 50,000 seasoned troops, equipped for battle with every weapon, ready to help David wholeheartedly, Anthu a fuko la Zebuloni, analipo 5,000. Iwowa anali asilikali odziwa bwino nkhondo, okhala ndi zida za mtundu uliwonse, okonzekera kudzathandiza Davide ndi mtima umodzi.
34 from Naphtali—1,000 officers, and with them 37,000 men carrying shield and spear; Anthu a fuko la Nafutali, analipo atsogoleri 1,000 pamodzi ndi anthu 37,000 onyamula zishango ndi mikondo;
35 from Dan—28,600 men ready for battle; Anthu a fuko la Dani, okonzekera nkhondo analipo 28,600.
36 from Asher—40,000 seasoned troops ready for battle; Anthu a fuko la Aseri, asilikali odziwa bwino nkhondo, okonzekeradi nkhondo analipo 40,000;
37 from east of the Jordan—Reuben, Gad, half the tribe of Manasseh—120,000, armed with every weapon of war. Ndipo kuchokera kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase, amene anali ndi zida za mtundu uliwonse analipo 120,000.
38 All these were warriors in battle formation who came to Hebron wholeheartedly to make David king over all Israel; the rest of Israel too were of one mind to make David king. Onsewa anali anthu odziwa kumenya nkhondo amene anadzipereka ku magulu awo. Iwo anabwera ku Hebroni ali otsimikiza kudzamuyika Davide kukhala mfumu ya Aisraeli. Aisraeli ena onse anali ndi mtima umodzinso womuyika Davide kukhala mfumu.
39 They stayed there three days with David, eating and drinking; their relatives had prepared food for them. Anthuwa anakhala ndi Davide masiku atatu akudya ndi kumwa pakuti mabanja awo anawapatsa zakudya.
40 Their neighbors as far as Issachar, Zebulun, and Naphtali brought food by donkey, camel, mule, and ox—flour, fig cakes, raisin cakes, wine, oil, cattle, and sheep in abundance, for there was joy in Israel. Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]