Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 11 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Then all Israel gathered to David at Hebron, saying, "Look, we are your bone and flesh. Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife abale anu.
2 Even before, while Saul was king, you led Israel out and back. Your Father told you, 'You will shepherd my people Israel; you will be ruler over my people Israel.'" Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”
3 All Israel's elders came to the king at Hebron, and David made a covenant with them at Hebron before our Father. Then they anointed David king over Israel, as our Father had said through Samuel. Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.
4 David and all Israel went to Jerusalem (that is, Jebus), where the Jebusites, its residents, lived. Davide ndi Aisraeli onse anapita ku Yerusalemu (ku Yebusi). Ayebusi amene ankakhala kumeneko
5 Jebus's people told David, "You won't enter here." But David took the stronghold of Zion—the city of David. anamuwuza Davide kuti, “Simulowa muno.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.
6 David said, "Whoever strikes the Jebusites first becomes head and commander." Joab son of Zeruiah went up first and became head. Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali.
7 David then settled in the stronghold; that is why it was called the city of David. Tsono Davide anakhazikika mu lingamo, ndipo mzindawu anawutcha Mzinda wa Davide.
8 He built the city all around, from the Millo to the encircling wall, while Joab restored the rest of the city. Iye anamanga malo onse ozungulira, kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Ndipo Yowabu anakonzanso mbali ina ya mzindawu.
9 And David became more and more powerful, for the Father of heaven's armies was with him. Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Wamphamvuzonse.
10 These are the chiefs of David's mighty men, who gave him strong support in his kingdom, with all Israel, to make him king, by our Father's word concerning Israel. Awa ndiye anali atsogoleri amphamvu a Davide. Iwo pamodzi ndi Aisraeli onse, anathandiza kulimbikitsa ufumu wake kuti ukwanire madera onse, monga momwe Yehova analonjezera.
11 This is the list of David's mighty men: Jashobeam, a Hachmonite, head of the Three, used his spear to kill 300 men in a single encounter. Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yasobeamu Mhakimoni anali mkulu wa atsogoleri. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300 nthawi imodzi.
12 After him, Eleazar son of Dodo the Ahohite, one of the three mighty warriors. Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi, mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu.
13 He was with David at Pas-dammim when Philistines gathered there for battle, in a field full of barley; the people fled from the Philistines, Iye anali ndi Davide ku Pasi-Damimu pamene Afilisti anasonkhana kudzachita nkhondo. Ankhondo anathawa Afilistiwo pamalo pamene panali munda wodzaza ndi barele.
14 but they stood their ground in the middle of the field, defended it, and struck down the Philistines; our Father saved them with a great victory. Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.
15 Three of the thirty top warriors went down to David at the rock by Adullam's cave, while a Philistine unit camped in the Rephaim Valley. Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu.
16 At that time David was in the stronghold, and a Philistine garrison was at Bethlehem. Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu.
17 David craved water: "If only someone would get me a drink from Bethlehem's well by the gate!" Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!”
18 The three broke through the Philistine camp, drew water from Bethlehem's well by the gate, and brought it to David. But he wouldn't drink it—he poured it out to our Father. Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova.
19 He said, "May my Father forbid it! Should I drink the blood of men who put their lives at risk? They brought it by risking their lives." So he refused to drink it. These were the deeds of the three warriors. Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.
20 Abishai the brother of Joab was chief of the Thirty. He used his spear to kill 300 men, and he made a name for himself among the Three. Abisai mʼbale wa Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300. Choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja.
21 Most honored of the Thirty, he became their commander—yet not one of the Three. Iye analandira ulemu woposa atatuwo. Kotero anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti iyeyo sanali mʼgulu la anthu atatu aja.
22 Benaiah son of Jehoiada, a valiant man from Kabzeel, did great deeds: he struck down two of Moab's mightiest, and went down into a pit on a snowy day and killed a lion. Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.
23 He also killed an Egyptian, a man of great size, about seven and a half feet tall, who had a spear like a weaver's beam. Benaiah went at him with a club, tore the spear from the Egyptian's hand, and killed him with his own spear. Ndipo iye anakanthanso Mwigupto amene anali wotalika mamita awiri ndi theka. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo wofanana ndi ndodo yowombera nsalu mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.
24 These were Benaiah son of Jehoiada's deeds; he gained a name among the three mighty men. Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja.
25 He was honored above the Thirty, but not among the Three. David put him in charge of his own guard. Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.
26 The mighty warriors were: Asahel the brother of Joab, Elhanan son of Dodo of Bethlehem, Ankhondo amphamvuwa anali: Asaheli mʼbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
27 Shammoth the Harorite, Helez the Pelonite, Samoti Mharori, Helezi Mpeloni.
28 Ira son of Ikkesh of Tekoa, Abiezer of Anathoth, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiezeri wa ku Anatoti,
29 Sibbecai the Hushathite, Ilai the Ahohite, Sibekai Mhusati, Ilai Mwahohi,
30 Maharai of Netophah, Heled son of Baanah of Netophah, Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa,
31 Ithai son of Ribai of Gibeah of the Benjaminites, Benaiah of Pirathon, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini, Benaya Mpiratoni,
32 Hurai of the brooks of Gaash, Abiel the Arbathite, Hurai wa ku zigwa za Gaasi, Abieli Mwaribati,
33 Azmaveth of Baharum, Eliahba the Shaalbonite, Azimaveti Mbaharumi, Eliyahiba Msaaliboni,
34 the sons of Hashem the Gizonite, Jonathan son of Shagee the Hararite, ana a Hasemu Mgizoni, Yonatani mwana wa Sage Mharari,
35 Ahiam son of Sachar the Hararite, Eliphal son of Ur, Ahiamu mwana wa Sakari Mharari, Elifali mwana wa Uri,
36 Hepher the Mecherathite, Ahijah the Pelonite, Heferi Mmekerati, Ahiya Mpeloni,
37 Hezro of Carmel, Naarai son of Ezbai, Heziro wa ku Karimeli Naara mwana wa Ezibai,
38 Joel the brother of Nathan, Mibhar son of Hagri, Yoweli mʼbale wa Natani, Mibihari mwana wa Hagiri,
39 Zelek the Ammonite, Naharai of Beeroth, the armor-bearer of Joab son of Zeruiah, Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya.
40 Ira the Ithrite, Gareb the Ithrite, Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,
41 Uriah the Hittite, Zabad son of Ahlai, Uriya Mhiti, Zabadi mwana wa Ahilai,
42 Adina son of Shiza the Reubenite, a leader of the Reubenites, and thirty with him, Adina mwana wa Siza Mrubeni, amene anali mtsogoleri wa Arubeni ndi anthu makumi atatu pamodzi naye,
43 Hanan son of Maacah, Joshaphat the Mithnite, Hanani mwana wa Maaka, Yehosafati Mmitini,
44 Uzzia the Ashterathite, Shama and Jeiel the sons of Hotham the Aroerite, Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyeli ana a Hotamu Mwaroeri,
45 Jediael son of Shimri, and Joha his brother, the Tizite, Yediaeli mwana wa Simiri, ndi Yoha Mtizi mʼbale wake,
46 Eliel the Mahavite, Jeribai and Joshaviah the sons of Elnaam, Ithmah the Moabite, Elieli Mhavati, Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, Itima Mmowabu,
47 Eliel, Obed, and Jaasiel the Mezobaite. Elieli, Obedi ndi Yaasieli Mmeobai.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]