Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Colossians 4 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Anyiimwe wakuluakulu yawo muli ni akapopolo achameo, achitileni akapolo wanu vindhu ivo vili vovomelezeka ni vofunika, uku nimujhiwa kuti anyiimwe namwe mulinawo Ambuye kumwamba.

Ivo mfunika kuchita

2Simdasiya kupembhela ata pang'ono. Mkale okonjheka kwa chalichonjhe kwa kupembha ni kumuyamika Mnungu. 3Mutipembhele ni ife kuti Mnungu watipache malo ya kwaakambila wandhu Uthenga Wabwino wa nghani ya Kilisito, ni ndande ya kulalikila uthenga umenewo ine namangidwa kuyambila kale. 4Nipembheleleni kuti nikambe yayo nifunika kuyakamba, kuti nikhoze kuuyika padanga uzene uwu kwa kila mundhu.

5Mukhale ni njelu yapo mkhala ni wandhu yawo sadakhulupilile. Ichitileni njhito bwino ndhawi yanu ngati umo mukhozela. 6Kila yapo mukamba mawu yanu yakhale yabwino siku zonjhe, niyayo yathangatila wina. Nimundhu wakakufunjhani mkhoze kujhiwa umo simumuyanghe.

Poolo wamalizila kalata yake

7Tikiko wali mbale wanga uyo nichita naye njhito ya Kilisito. Iye ni mthandizi wanga wokhulupilika ni wamtumikila Ambuye pamojhi ni ine. Siwakukambileni nghani zanga zonjhe. 8Nimtuma kwanu Tikiko kuti mujhiwe umo tiyendekela, dala wakuthileni mtima. 9Nimtuma iye pamojhi ni Onesimo, mbale wokondedwa ni wokhulupilika uyo wachokela mgulu lanu. Siakukambileni kila chindhu icho chachitika kwathu.

10Alisitako uyo walimndende chipano pamojhi ni ine wakulonjelani. Maluko msooni wa Banaba wakulonjelani, ngati umo nakukambilani nghani za Maluko, wakafika mlandileni. 11Chimchijha mulandilenjho moni kuchokela kwa Jeshua, uyo watanidwanjho Yusto. Anyiyawa atatu wokha nde Ayahudi yawo achita njhito pamohi ni ine ndande ya ufumu wa Mnungu. Anyiyawa anitandiza kupunda.

12Wakulonjelani Epafula, uyo wali mbowa mwina kuchokela kwanu. Iye wachauchika kukupembhelelani kila ndhawi, kuti mkule muuzimu ni kulandila kila chindhu icho Mnungu wafuna. 13Nijhiwa kuti wachita njhito ya kukupembhelani kupunda ndande ya wandhu a ku Laodikiya ni wajha aku Heilapoli. 14Mlandilenjho moni kuchokela kwa bwenji wathu wokondedwa sing'anga Luka, ni kuchokela kwa Dema.

15Mwaalonjele abale wonjhe aku Laodikiya ni mlongo wathu Nimfa pamojhi ni gulu la wandhu yawo amkhulupilila Kilisito, ilo lipezana munyumba yake. 16Yapo simumalize kusoma kwa mvekelo kalata iyi, muipeleke kugulu la wandhu amkulupilila Kilisito la ku Laodikiya kuti nawonjho akaisome. Namwenjho muisome kalata ya ku Laodikiya. 17Mkambileni chimwechi Alikipo, “Wachimikize kuti wamaliza njhito iyo wachidwa ni Ambuye.”

18Izi ni moni zanga nalemba kwa manja yanga namwenenwake, ine Poolo, musadaleka kunikumbukila yapo nili mndende muno. Nikupembhelelani kuti Mnungu wakuchitileni ubwino wonjhe.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]