Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

1 Timothy 5 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Icho wafunika kuchita mundhu wamkhulupilila Kilisito

1Siudamnyindila wamnuna mzee, nambho ukambe nayo bwino ngati mujha wadakakhala tate wako. Anyamata waone ngati achabale wako, 2wachikazi azee waone ngati anyamaye wako, ni anyamata wachikazi ngati alongo wako, kwa ubwino waonjhe.

3Walemekeze wachikazi yawo afedwa ni achamunao, yawo alibe mthandizo. 4Ngati mundhu wafedwa ni mmunake wali ni wana kapina ajhukulu, achameneo ifunika amsunge wamkazi mmeneyo ngati umo lifunikila pa gulu la wandhu lamkhulupilila Kilisito, pakuti mmeneyo ni mundhu wao achinawene. Kwa kuchita chimwecho siikhale ngati kwapacha malipilo obala wao ni azee wao, pakuti chimenecho ni chindhu cho kwadilicha pachogolo pa Mnungu. 5Wamkazi uyo wafedwa ni mmunake, uyo walibe wa kumthangatila waika chikhulupi chake kwa Mnungu naye waendekela kupembhela usiku ni usana kuti Mnungu wamtangatile. 6Nambho wamkazi wafedwa ni mmunake, uyo wakhala ukhalo ojhikondwecha mmeneyo wamwalila atangati wali wamoyo. 7Apache wandhu maagizo yaya, dala wasadakhalapo mundhu waliyonjhe wokamba kuti wandhu amkhulupilila Kilisito achita kuyipa. 8Nambho ngati mundhu siwaasunga wandhu wake, hasa wajha ali kukhomo lake, mundhu mmeneyo wachikana chikhulupililo, ni woipa kupunda kupitilila mundhu uyo siwadakhulupilile.

9Wamkazi wafedwa ni mmunake siwadalembedwa mchikalakala mbaka wakwane vyaka sitini. Niifunika wakhale wamkazi uyo wadakwatiwa mala kamojhipe, 10ni wakhale mundhu uyo wakambidwa kwa ubwino, uyo wadalela bwino wana wake, uwo wadalandila alendo kukhomo lake, uyo wadaachuka myendo wandhu wa Mnungu, uyo wamathangatila wandhu osauka, niuyo wamajhichocha kuchita vichito vabwino. 11Siudaalembecha wachikazi yawo afedwa ni achamunao yawo ali anyamata, pakuti makhumbilo ya mathupi yawo yakapunda kukhala ni mbhavu kupitilila kujhichocha kwawo kwa Kilisito, afunanjho kukwatiwa, 12ni achamenewo saoneke kuti osati okhulupilika, ndande yachijha adakamba pajha poyamba. 13Wachikazi ngati achamenewo akhala ni tabia ya ulesi, uku niayenda nyumba mbaka nyumba, ni osati akhala alesipe, nambho akamba wandhu wina pambhepete, ni kuchatilila vindhu va wandhu wina, ni kukamba vindhu ivo sadafunike kuvikamba. 14Mchimwecho nifuna wachikazi afedwa ni achamunao yawo ali anyamata akwatiwe, apate wana ni kusunga nyumba zao, dala adani wathu sadapata malo ya kutikamba ife kuipa. 15Pakuti wachikazi wina yawo afedwa ni achamunao athomsiya Mnungu ni kumchata Satani. 16Nambho ngati wamkazi uyo wamkulupilila Kilisito wali ni wachikazi yawo afedwa ni achamunao kukhomo lake, wafunika waasunge niosati kulisiila gulu la wandhu amkulupilila Kilisito njhito imeneyo, dala gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito likhoze kwasunga wachikazi afedwa, anyiyawo alibe wandhu akwathangatila.

17Achogoleli a gulu la wandhu amkhulipilila Kilisito, yawo achogoza bwino afunika alipidwe bwino, hasa anyiwajha ayaluza ni kuuzila. 18Pakuti yalembedwa mmalembo ya Mnungu kuti, “Siudaimanga ng'ombe kukamwa yapo wathangatila kuchita njhito yopulusula mbeu za ngano mviphutu,” ni “Uyo wachita njhito ifunika wapate mkokolo wake.” 19Siudavomela kulandila milandhu iyo yausu achogoleli mbaka ichimikizidwe ni wandhu awili kapina atatu. 20Wajha ayendekela kuchita machimo anyindile padanga, dala wina akhoze kuopa.

21Nikuagiza pachogolo pa Mnungu, ni pachogolo pa Kilisito ni pachogolo pa atumiki akumwamba a Mnungu uyagwile maagizo yaya popande kusiaa ata limojhi kapina kukondelela. 22Siudakhala ni msanga kumuikila mundhu manja ni siudavomela mundhu waliyonjhe wakuguza kuchita machimo yake, jhisunge ni ukhale wabwino.

23Siudamwa majhipe, nambho umwe ni divai pang'ono ndande ya mmimba mwako ni ndande udwala tetete.

24Machimo ya wandhu wina yaoneka padanga nayo yachogoza kupita kumalamulo, ni machimo ya wandhu wina yaoneka pambuyo. 25Mchimwecho vichito vabwino vioneka padanga, ni hata vijha asati vabwino sivikhoza kubisika.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]