Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

1 Timothy 3 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Achogoleli pa gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito

1Mawu yaya niyauzene, mundhu uyo wafuna kukhala mchogoleli wa gulu la wandhu amkhulupilila Yesu, mmeneyo wakhumbila njhito ya bwino. 2Chipano mchogoleli wafunika wakhale mundhu uyo siwadandaulidwa, wafunika wakhale ni wamkazi mmojhipe, Wakhale mundhu uyo wajhichelekeza, ni uyo wali ni busala, uyo walemekezeka, wajhilandila alendo, ni wakhoze kuyaluza. 3Siwadakhala mundhu wolojhela kapina mundhu wandewo, nambho wakhale wotonda. Sidakhala wokwiya chisanga kapina mundhu uyo wakumbila ndalama. 4Wafunika wakhale mundhu uyo wakhoza kusunga bwino nyumba yake, ni kwayaluza wana wake akhale ovela ni akhale ni ulemu. 5Pakuti ngati mundhu siwakoza kuisunga bwino nyumba yake, siwakhoze bwanji kulisunga gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito yawo ali Amnungu? 6Mundhu uyo siwadakwime mchikhulupililo siwadaikidwa kukhala mchogoleli pa gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito, wakhoza kujhidama, ni kulamulidwa ngati mujha Satana wadalamulidwa. 7Wafunika wakhale mundhu uyo wakambidwa kwa ubwino pakati pa wandhu ali kubwalo kwa wandhu mkhulupilila Kilisito, wasadakhalapo mundhu uyo wamkamba kuipa.

Otangatila pa gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito

8Wandhu atangatila wandhu pa gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito afunika akhale wandhu aukhalo wabwino, wandhu yawo achita vindhu ivo vili vabwino, siamamwa mowa mopitilila, ni sadakhala ni kumbilo la ndalama, 9Ifunika kuchoka mkhati mwa mitima yawo achate uzene wa mkhati wa chikhulupi. 10Ifunika apimidwe uti, niakaoneka kuti akhoza pamenepo aloledwe kuchita njhito yawo yotangatila. 11Achakazawo nawo afunika akhale bwino ni wandhu, samaakamba wina pambephete, akhale ojhichekeleza ni okhulupilika pa vindhu vonjhe. 12Wotangatila pa gulu la wandhu amkhulupilia Kilisito ifunika wakhale ni wamkazi mjojhipe, ni uyo wakhoza kusunga bwino wana wake ni wandhu a mnyumba mwake. 13Pakuti otangatila anyiawo achita bwino njhito yawo apata matamando yabwino, ni akhoza kuchikambilila bwino chikhulupi chawo popande mandha.

Chisisi cha chikulu

14Ata ngati nikhulupilila kujha kwako posachedwa pano, nikulembela kalata ino iwe Timoseo dala, 15ngati nikachedwa, kalata ino sikujhiwiche ukhalo uwo ufunika tikhale nawo pa nyumba ya Mnungu, nyumba imeneyo ni gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito. Gulu limenelo nde nyumba ya Mnungu wali wamoyo, ni gulu limenelo la wandhu amkhulupilila Kilisito ninjhiki ni chiyambo cha uzene. 16Palibe kukhaikila kwalikhojhe kwa ukulu wa chisisi cha kulambila kwathu,Wadaoneka mundhu ngati ife,wadachimikizidwa ni mzimu kuti walibe cholakwa,wadaoneka ni atumiki akumwamba a Mnungu.Wadalalikidwa mmaiko yonjhe,wadakhulupililidwa pajhikowadatengedwa kumwamba pa ulemelelo.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]