Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

1 Timothy 1 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Ine Poolo, mtumwi wa Yesu kilisito kwa lamulo la Mnungu muomboli wathu ni Kilisito Yesu chikhulupi chathu, 2Nikulembela iwe Timoseo mwanawanga pa chikhulupililo. Nikufunila ubwino, lisungu ni mtendele kuchokela kwa Mnungu Tate wathu ni Kilisito Mbuye wathu.

Mayaluzo ya unami

3Nikonda ukhale kumeneko ku Efeso, ngati umo nidakupembha yapo nimapita ku Makedoniya. Alipo wandhu wina kumeneko ayaluza mayaluzo yamthila. Wakanize sadaayaluza wandhu mayaluzo yameneyo. 4Wakambile asiyane ni nghani izo zilibe mate ni kuchula mayina ya mibadwa iyo ilibe pothela iyo isongozela michuchano, ni siichita njhito ya mnungu pa chikhulupililo. 5Dala la lamulo ili ni chikondi, icho chichokela mumtima wabwino, maganizo yabwino ni chikhulupi cha uzene. 6Wandhu wina avisiya vindhu vimenevo ni kunga'anamukila mawu yayo yalibe mate. 7Akonda kukhala oyaluza thauko la Mnungu ilo wadampacha Musa, nambho sachata yajha ayakamba, kapina yajha ayakambichicha. 8Tijhiwa kuti thauko la Mnungu ilo wadampacha Musa ni labwino, ngati likatumilidwa umo ifunikila. 9Nambho tifunika kukumbukila kuti thauko la Mnungu siliikidwa ndande ya wandhu abwino, nambho liikidwa ndande ya wandhu wowananga ni yawo sagwila thauko, yao samlambila Mnungu ni yawo ali ni machimo, wandhu yawo sakhala ngati umo wafunila Mnungu ni wandhu yawo samlemekeza Mnungu, wandhu yawo akupha obala wao, ni akupha mundhu waliyonjhe mujha. 10Thauko la Mnungu laikidwa ndande ya wandhu achita chigololo, ni wammuna uyo wamchita wammuna mnjake ngati mkazake, yawo agulicha makapolo ni amthila ni anyiiawo alumbila mthila ni yawo achita chalichoche icho chichuchana ni mayaluzo ya uzene. 11Mayaluzo yameneyo yapezeka mu Uthenga wa Bwino uwo ulangiza ukulu wa Mnungu uyo wali ni mwawi wonjhewo. Uthenga umenewo ndeuwo napachidwa kuti niulalikile.

Mayaniko ndande ya lisungu la Mnungu

12Naayamika Ambuye wathu Yesu Kilisito anipacha mbhavu ndande adaniona ine kuti ni wokhulupilika ni wanisangha dala natumikile. 13Ata ngati poyambila ine nidamtukwana Ambuye Yesu ni kwavuticha wandhu wake. Nambho Mnungu wadanilengela lisungu, ndande nidalibe chikhulupi, ni sinimajhiwe icho nimachichita. 14Nambho Ambuye wathu adanichitila vindhu vabwino vambili, ni adanipachanjho kumkhulupilila Kilisito ni chikondi icho chili mkati mwake. 15Mawu yayo yakamba kuti Kilisito wadajha pajhiko kutiombola ife wandhu amachimo, ine ni woipa kupitilila anyiiwo wonjhe, niyauzene ni niyofunika kuvomelezeka. 16Nambho Mnungu wadanilengela lisungu, dala Kilisito walangize kulimba mtima kwake konjhe kwa ine, dala anyiwajha wonjhe yawo pambuyo samkhulupilile anichatize ine ni kulandila umoyo wa muyaya. 17Chipano iye walimfumu wa muyaya uyo walibe mathelo, uyo siwaoneka, uyo wali Mnungu yokha, wapachidwe ulemu ni ulemelelo muyaya ni muyaya. Ikhale chimwecho.

18Mwanawanga Timoseo, nikupacha agizo ili, kuchokana ni mawu ya ulosi yayo yadakambidwa kale ndande yako. Ukhoze kuichita njhito bwino ya kulalikila Uthenga Wabwino Mawu limenelo. 19Uendekele kukhulupilila mawu ya Mnungu ni kuchita chijha uchiona kuti chili chabwino, wandhu wina akana kuchita vabwino, ni mchimwecho adasiya kukhulupilila. 20Pakati pawo wandhu achamenewo alimo Humenenayo ni Alekizanda yawo nampacha satana, kuti ayaluzidwe dala sadamtukwana Mnungu.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]