Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Zechariah 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Again I lifted my eyes and looked, and there before me was a flying scroll. Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona chikalata chimene chimawuluka.
2 He asked, "What do you see?" I answered, "I see a flying scroll, thirty feet long, fifteen feet wide." Mngelo uja anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ndikuona chikalata chikuwuluka, mulitali mwake mamita asanu ndi anayi ndipo mulifupi mwake mamita anayi ndi theka.”
3 Then he said to me, "This is the curse going out over the whole land. Everyone who steals will be purged away, by one side of it; everyone who swears falsely, purged away by the other." Ndipo mngeloyo anandiwuza kuti, “Awa ndi matemberero amene akupita pa dziko lonse lapansi; potsata zimene zalembedwa mʼkati mwa chikalatamo, aliyense wakuba adzachotsedwa, ndipo potsata zomwe zalembedwa kunja kwake, aliyense wolumbira zabodza adzachotsedwanso.
4 "I have sent it out, declares the Father of heaven's armies; it will enter the thief's house and the house of whoever swears falsely by my name, stay there, and consume it—both timbers and stones." Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza, ndipo lidzalowa mʼnyumba ya munthu wakuba ndi munthu wolumbira zabodza mʼdzina langa. Lidzakhala mʼnyumbamo mpaka kuyiwonongeratu, matabwa ake ndi miyala yake yomwe.’ ”
5 Then the angel talking with me came forward and said, "Now look up and see what this is going out." Kenaka mngelo amene amayankhula nane uja anabwera patsogolo panga ndipo anandiwuza kuti, “Kweza maso ako tsopano kuti uwone kuti ndi chiyani chikubwerachi.”
6 I asked, "What is it?" He said, "The basket going out." Then, "This is their guilt across the whole land." Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?” Mngeloyo anayankha kuti, “Limeneli ndi dengu loyezera.” Ndipo anawonjezera kunena kuti, “Umenewu ndi uchimo wa anthu mʼdziko lonse.”
7 Suddenly, the lead cover was lifted, and there was a woman sitting inside the basket. Pamenepo chovundikira chake chamtovu chinatukulidwa, ndipo mʼdengumo munali mutakhala mkazi.
8 He said, "This is Wickedness." He pushed her back into the basket and forced the lead weight over its mouth. Mngeloyo anati, “Chimenechi ndi choyipa,” ndipo anamukankhira mkaziyo mʼdengu muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.
9 I looked up and saw two women coming, wind in their wings—wings like a stork's—and they lifted the basket between earth and sky. Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi.
10 Then I said to the angel who was speaking with me, "Where are they taking the basket?" Ine ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Dengulo akupita nalo kuti?”
11 He said to me, "To build a house for it in the land of Shinar; and when it's ready, the basket will be set there on its base." Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]