Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Numbers 34 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 And our Father spoke to Moses, saying, Yehova anawuza Mose kuti,
2 "command the Israelites: when you enter the land of Canaan, this is the land that will fall to you as inheritance—the land of Canaan, within its borders. “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:
3 Your south side runs from the Zin wilderness along Edom's edge; your south border starts at the Dead Sea's end, eastward. “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere.
4 Your border will turn south of the Ascent of Akrabbim, cross to Zin, reach south of Kadesh-barnea, go on to Hazar-addar, and pass to Azmon. Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni,
5 From Azmon the border turns to Egypt's Brook, ending at the Sea. kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.
6 "Your western border will be the Mediterranean Sea and its coast. “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.
7 "This will be your north border: from the Mediterranean Sea draw your line to Mount Hor. “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori
8 From Mount Hor mark a line to Lebo-hamath, ending at Zedad; ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi,
9 then the border will extend to Ziphron and end at Hazar-enan. This will be your northern border. ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
10 "You will mark out your eastern border from Hazar-enan to Shepham. “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu.
11 The border will go down from Shepham to Riblah, east of Ain, then go down and reach the slope east of the Sea of Chinnereth. Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti.
12 The border goes down to the Jordan, ending at the Dead Sea. This will be your land, with its borders all around." Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere. “ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”
13 Moses commanded the Israelites: This is the land you will inherit by lot, which our Father commanded to give to the nine tribes and the half-tribe. Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka,
14 The tribe of Reuben's sons, by their fathers' houses, and the tribe of Gad's sons, by their fathers' houses, have already taken their inheritance; so has the half-tribe of Manasseh. chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo.
15 The two and a half tribes received their inheritance across the Jordan from Jericho, eastward toward the sunrise. Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
16 And our Father spoke to Moses, saying, Yehova anawuza Mose kuti,
17 "names of the men who will divide the land for you as inheritance: Eleazar the priest and Joshua son of Nun. “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18 And you will take one leader from each tribe to divide the land for inheritance. Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo.
19 These are the names of the men: from the tribe of Judah, Caleb the son of Jephunneh; Mayina awo ndi awa: Kalebe mwana wa Yefune, wochokera ku fuko la Yuda,
20 from the tribe of the sons of Simeon, Shemuel the son of Ammihud; Semueli mwana wa Amihudi, wochokera ku fuko la Simeoni;
21 from the tribe of Benjamin, Elidad the son of Chislon; Elidadi mwana wa Kisiloni, wochokera ku fuko la Benjamini;
22 from the tribe of the sons of Dan, a leader, Bukki the son of Jogli; Buki mwana wa Yogili, mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;
23 from Joseph's sons: from Manasseh's tribe, leader Hanniel son of Ephod, Hanieli mwana wa Efodi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;
24 and from the tribe of the sons of Ephraim, a leader, Kemuel the son of Shiphtan; Kemueli mwana wa Sifitani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.
25 from the tribe of the sons of Zebulun, a leader, Elizaphan the son of Parnach; Elizafani mwana wa Parinaki, mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;
26 from the tribe of the sons of Issachar, a leader, Paltiel the son of Azzan; Palitieli mwana wa Azani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,
27 from the tribe of the sons of Asher, a leader, Ahihud the son of Shelomi; Ahihudi mwana wa Selomi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;
28 and from the tribe of the sons of Naphtali, a leader, Pedahel the son of Ammihud." Pedaheli mwana wa Amihudi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”
29 These are the ones our Father commanded to divide the inheritance among the children of Israel in the land of Canaan. Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]