Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Micah 6 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Hear what our Father says: Stand, plead your case before the mountains; let the hills hear your voice. Tamverani zimene Yehova akunena: “Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri; zitunda zimve zimene inu muti muyankhule.
2 Listen, mountains, to our Father's case, and you lasting foundations of the earth; for our Father has a case against his people, and he will contend with Israel. Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri; tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi. Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake; Iye akutsutsa Aisraeli.
3 My children, what have I done to you? How have I wearied you? Answer me! “Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani? Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni.
4 For I brought you up from the land of Egypt and redeemed you from the house of slavery; I sent before you Moses, Aaron, and Miriam. Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo. Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni, pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.
5 My children, remember what Balak king of Moab planned, and what Balaam son of Beor answered him, from Shittim to Gilgal, so you will know the righteous acts of your Father. Anthu anga, kumbukirani zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha. Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala, kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”
6 What should I bring when I come before our Father? How should I bow before our Father on high? Will I come to him with burnt offerings, with year-old calves? Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba? Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza, ndi ana angʼombe a chaka chimodzi?
7 Will our Father be pleased with thousands of rams, with 10,000 rivers of oil? Will I give my firstborn for my rebellion, the child of my own body for the sin of my soul? Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000, kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta? Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga? Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?
8 He has told you what is good; and what does our Father require of you but to do justice, to love kindness, and to walk humbly with your Father? Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
9 The voice of our Father calls to the city—and it is sound wisdom to fear your name—"Listen, tribe, and the one who appointed it! Tamverani! Yehova akuyitana anthu okhala mu mzinda ndi nzeru kuopa dzina lanu. “Mverani mfumu ndi Iye amene anayikhazikitsa.
10 Are there still treasures of wickedness in the house of the wicked, and the accursed short measure? Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa?
11 Will I declare innocent the one with dishonest scales, with a bag of deceitful weights? Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo, ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake?
12 Your rich men are full of violence, your inhabitants speak lies, and their tongues are full of deceit. Anthu ake olemera amachita zachiwawa; anthu ake ndi abodza ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo.
13 So I myself have begun to strike you, making you desolate because of your sins. Choncho, ndayamba kukuwonongani, kukusakazani chifukwa cha machimo anu.
14 You will eat but not be satisfied, and your hunger will stay within you; you will store up but not save, and what you save I will give over to the sword. Mudzadya, koma simudzakhuta; mudzakhalabe ndi njala. Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika, chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga.
15 You will sow but not reap; you will press olives but have no oil to use, and press the grapes but not drink the wine. Mudzadzala, koma simudzakolola. Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito. Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake.
16 For you have kept the statutes of Omri and all the works of the house of Ahab, and you have followed their ways; so I will make you a desolation and your inhabitants a mockery, and you will bear the scorn of my children." Inu mwatsatira malangizo a Omuri ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu, ndi khalidwe lawo lonse. Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu; mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]