1When Jesus had finished all these sayings, he said to his disciples,OCCLYesu atamaliza kuyankhula zonsezi, anati kwa ophunzira ake,
2"You know Passover comes after two days, and the Son of Man is handed over to be crucified."OCCL“Monga mukudziwa, kwatsala masiku awiri kuti Paska ifike ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti apachikidwe.”
3Then the chief priests and elders of the people gathered in the courtyard of the high priest Caiaphas,OCCLPamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa,
4and they plotted together to seize Jesus secretly and kill him.OCCLndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha.
5But they said, "Not during the festival, or there will be an uproar among the people."OCCLNdipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.”
6Now when Jesus was in Bethany, in the house of Simon the leper,OCCLYesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate,
7a woman came to him with an alabaster jar of very expensive perfume and poured it on his head as he sat at the table.OCCLmayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.
8Seeing this, the disciples were angry, saying, "Why this waste?OCCLOphunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere?
9For this could have been sold for a large sum and given to the poor."OCCLMafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”
10Jesus knew this and said to them, "Why trouble this woman? She has done a beautiful thing to me.OCCLYesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino.
11For you always have the poor with you, but you will not always have me.OCCLOsauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse.
12For when she poured this perfume on my body, she did it to prepare me for burial.OCCLPamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda.
13Truly I tell you: wherever this gospel is preached worldwide, what she did will also be told, in memory of her."OCCLZoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.”
14Then one of the Twelve, the one called Judas Iscariot, went to the chief priests,OCCLPamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe
15and said, "What are you willing to give me, and I will hand him over to you?" And they counted out thirty pieces of silver for him.OCCLnafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu.
16And from then on he looked for an opportunity to betray him.OCCLKuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu.
17On the first day of Unleavened Bread, the disciples asked Jesus, "Where do you want us to prepare for you to eat the Passover?"OCCLPa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?”
18He said, "Go into the city to a certain man and tell him, 'The Teacher says: My time is near. I'll keep Passover at your house with my disciples.'"OCCLIye anayankha kuti, “Pitani mu mzinda kwa munthu wakutiwakuti ndipo kamuwuzeni kuti, ‘Aphunzitsi akuti, nthawi yanga yoyikidwa yayandikira. Ine ndidzadya phwando la Paska ndi ophunzira anga ku nyumba kwako.’ ”
19And the disciples did as Jesus directed them, and they prepared the Passover.OCCLPamenepo ophunzira ake anachita monga momwe Yesu anawawuzira ndipo anakonza Paska.
20When evening came, he sat at the table with the Twelve.OCCLKutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiriwo anakhala pa tebulo nʼkumadya.
21And as they were eating, he said, "Truly I tell you, one of you will betray me."OCCLAkudya, Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka.”
22Deeply grieved, they each asked him, "Surely not I, Lord?"OCCLIwo anamva chisoni kwambiri ndipo anayamba kuyankhulana naye mmodzimmodzi nati, “Kodi nʼkukhala ine Ambuye?”
23He replied, "The one who has dipped his hand in the bowl with me will betray me.OCCLYesu anayankha nati, “Iye amene akusunsa mʼmbale pamodzi ndi Ine, yemweyo adzandipereka.
24The Son of Man goes, just as is written of him. But how terrible for the man who betrays him—better for him had he never been born."OCCLMwana wa Munthu adzaphedwa monga mmene kunalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene apereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
25Judas, his betrayer, said, "Surely not I, Rabbi?" He said to him, "You have said so."OCCLNdipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?” Yesu anayankha nati, “Iwe watero.”
26As they ate, Jesus took bread, blessed and broke it, gave it to the disciples, and said, "Take, eat; this is my body."OCCLPamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, idyani; ili ndi thupi langa.”
27Taking a cup and giving thanks, he gave it to them, saying, "Drink from it, all of you,OCCLKenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati, “Imwani nonsenu.
28for this is my blood of the covenant, poured out for many for forgiveness of sins.OCCLAwa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri kuti akhululukidwe machimo.
29I tell you: I won't drink this fruit of the vine again, from now until the day I drink it new with you in my Father's kingdom."OCCLNdikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mtengo wa mpesa kuyambira lero mpaka tsiku ilo pamene ndidzamwenso mwatsopano ndi inu mu ufumu wa Atate anga.”
30And when they had sung a hymn, they went out to the Mount of Olives.OCCLAtayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi.
31Then Jesus told them, "Tonight you will all fall away because of me.For it is written: 'I will strike the shepherd, and the flock's sheep will be scattered.'OCCLPamenepo Yesu anawawuza kuti, “Usiku omwe uno inu nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “ ‘Kantha mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’
32But after I am raised up, I will go ahead of you to Galilee."OCCLKoma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”
33Peter said to him, "Though they all fall away because of you, I will never fall away."OCCLPetro anayankha nati, “Ngakhale onsewa atakuthawani, ine ndekha ayi.”
34Jesus said to him, "I tell you the truth: before the rooster crows tonight, you will deny me three times."OCCLYesu anayankha nati, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti usiku omwe uno, asanalire tambala, udzandikana Ine katatu.”
35Peter said, "Even if I must die with you, I won't deny you." All the disciples said the same.OCCLKoma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi.
36Then Jesus came with them to a place called Gethsemane and told the disciples, "Sit here while I go pray over there."OCCLKenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti, “Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo.”
37And taking with him Peter and the two sons of Zebedee, he became deeply grieved and distressed.OCCLAnatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima.
38Then he told them, "My soul is crushed with sorrow, even to death. Stay here and watch with me."OCCLPamenepo anawawuza kuti, “Moyo wanga uli ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo dikirani pamodzi ndi Ine.”
39Going a little farther, he fell on his face and prayed, "My Father, if possible, let this cup pass from me. Yet not as I will, but as you will."OCCLAtapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, “Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.”
40He came to the disciples and found them asleep. He said to Peter, "So, couldn't you stay awake with me one hour?OCCLKenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti, “Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha?
41Stay alert and pray, so you don't fall into temptation; the spirit is willing, but the flesh is weak."OCCLKhalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.”
42A second time he went away and prayed, "My Father, if this cannot pass unless I drink it, your will be done."OCCLAnachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, “Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.”
43And he came again and found them sleeping, for their eyes were heavy.OCCLAtabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo.
44So leaving them again, he went away and prayed a third time, saying the same words again.OCCLChoncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi.
45Then he came to the disciples and said to them, "Still sleeping and resting? Look, the hour has come, and the Son of Man is betrayed into the hands of sinners.OCCLKenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo, “Kodi mukanagonabe ndi kupumula? Taonani, ora layandikira ndipo Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa ochimwa.
46Get up, let's go! Look, the one who betrays me is here!"OCCLImirirani, tiyeni tizipita! Wondipereka Ine wafika!”
47While he was still speaking, Judas, one of the Twelve, suddenly came with a large crowd carrying swords and clubs, sent by the chief priests and elders of the people.OCCLAkuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu.
48Now the betrayer had given them a signal: "The one I kiss is him—seize him."OCCLWomuperekayo anawawuziratu chizindikiro anthuwo kuti, “Amene ndidzapsompsona ndi iyeyo; mugwireni.”
49And immediately he came up to Jesus and said, "Greetings, Rabbi!" And he kissed him.OCCLPamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye.
50Jesus told him, "Friend, do what you came to do." Then they came, grabbed Jesus, and held him.OCCLYesu anayankha kuti, “Bwenzi langa, chita chimene wabwerera.” Pamenepo anthuwo anabwera patsogolo namugwira Yesu ndi kumumanga.
51And look, one of those with Jesus reached out his hand, drew his sword, struck the high priest's servant, and cut off his ear.OCCLPa chifukwa ichi, mmodzi wa anzake a Yesu anagwira lupanga lake, nalisolola ndi kutema wantchito wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.
52Then Jesus said to him, "Put your sword back in its place. All who take the sword will die by the sword.OCCLYesu anati kwa iye, “Bwezera lupanga lako mʼchimake, chifukwa onse amene amapha ndi lupanga adzafa ndi lupanga.
53Do you think I can't call on my Father, who'd at once send me more than twelve legions of angels?OCCLKodi mukuganiza kuti sindingathe kupempha Atate anga ndipo nthawi yomweyo nʼkundipatsa magulu a angelo oposa khumi ndi awiri?
54But how then would the Scriptures be fulfilled, that it must happen this way?"OCCLKoma nanga malemba akwaniritsidwa bwanji amene akuti ziyenera kuchitika motere?”
55At that hour Jesus said to the crowds, "Did you come out with swords and clubs to seize me, as against a bandit? I sat teaching in the temple daily, and you didn't arrest me.OCCLPa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo, “Kodi ndine mtsogoleri wa anthu owukira kuti mwabwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mʼNyumba ya Mulungu kuphunzitsa, koma simunandigwire.
56But all this happened to fulfill the prophets' Scriptures." Then all the disciples abandoned him and fled.OCCLKoma zonsezi zachitika kuti zolembedwa ndi aneneri zikwaniritsidwe.” Pamenepo ophunzira anamusiya nathawa.
57Then those who arrested Jesus brought him to Caiaphas the high priest, where the scribes and the elders had gathered.OCCLIwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana.
58Peter followed at a distance, to the high priest's courtyard, went in, and sat with the guards to watch how it would end.OCCLKoma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira.
59The chief priests and the whole Council sought false testimony against Jesus, to put him to death,OCCLAkulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu.
60but they found none, though many false witnesses came forward. At last two came forward,OCCLKoma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka. Pomalizira mboni ziwiri zinabwera patsogolo.
61and said, "This man said, 'I can destroy God's temple and rebuild it in three days.'"OCCLNdipo zinati, “Munthu uyu anati, ‘Ndikhoza kupasula Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso mʼmasiku atatu.’ ”
62The high priest stood up and said to him, "Have you no answer? What are these men testifying against you?"OCCLPamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?”
63But Jesus was silent. The high priest said, "I put you under oath by the living God: tell us whether you are the Christ, the Son of God."OCCLKoma Yesu anakhalabe chete. Mkulu wa ansembe anati kwa Iye, “Ndikulamulira Iwe ndi lumbiro pamaso pa Mulungu wa Moyo: utiwuze ife ngati ndiwe Khristu Mwana wa Mulungu.”
64Jesus told him, "You've said it. But I tell you: from now on you'll see the Son of Man seated at Power's right hand, coming on heaven's clouds."OCCLYesu anayankha nati, “Mwanena ndinu. Koma ndikunena kwa inu nonse: mʼtsogolomo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera ndi mitambo ya kumwamba.”
65Then the high priest tore his clothes: "He has blasphemed! Why do we still need witnesses? You've now heard the blasphemy.OCCLPamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake.
66What is your judgment?" They answered, "He deserves death."OCCLMukuganiza bwanji?” Iwo anayankha kuti, “Ayenera kuphedwa!”
67Then they spit in his face and struck him; and some slapped him,OCCLKenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi.
68saying, "Prophesy to us, Christ! Who hit you?"OCCLNdipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?”
69Peter sat outside in the courtyard. A servant girl approached, saying, "You too were with Jesus the Galilean."OCCLTsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”
70But he denied it before them all, saying, "I don't know what you're talking about."OCCLKoma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”
71As he went out to the gate, another servant girl saw him and told those there, "This man was with Jesus of Nazareth."OCCLKenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.”
72And again he denied it with an oath, "I do not know the man."OCCLIye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”
73Shortly after, the bystanders came to Peter: "Surely you're one of them too, since your accent gives you away."OCCLPatapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”
74Then he began to curse himself and swear, "I don't know the man." At once a rooster crowed.OCCLPamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!” Nthawi yomweyo tambala analira.
75Peter remembered Jesus' words: "Before the rooster crows, you will deny me three times." He went out and wept bitterly.OCCLNdipo Petro anakumbukira mawu amene Yesu anayankhula kuti, “Tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.” Ndipo anatuluka panja nakalira kwambiri.