Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Matthew 24 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Jesus was leaving the temple when his disciples came to show him its buildings. Yesu anatuluka mʼNyumba ya Mulungu ndipo akuchoka ophunzira ake anadza kwa Iye ndi kumuonetsa mamangidwe a Nyumbayo.
2 "Do you see all these?" he answered. "Truly I tell you: not one stone here will be left on another; all will be torn down." Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuona zinthu zonsezi? Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti palibe mwala pano umene udzasiyidwe pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
3 While Jesus was sitting on the Mount of Olives, his disciples came to him privately: "Tell us, when will these things happen, and what sign marks your coming and the end of the age?" Pamene Yesu anakhala pansi pa phiri la Olivi, ophunzira ake anabwera kwa Iye mwamseri nati, “Tiwuzeni, kodi izi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi zizindikiro za kutha kwa dziko zidzakhala chiyani?”
4 Jesus answered, "Watch out that no one deceives you. Yesu anayankha kuti, “Onetsetsani kuti wina asakunyengeni.
5 "For many will come in my name, claiming, 'I am the Christ,' and they will deceive many. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati, ‘Ndine Khristu,’ ndipo adzanyenga ambiri.
6 You'll hear of wars and rumors of wars—don't be alarmed. This must happen, but the end isn't yet. Mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, koma onetsetsani kuti musadzidzimuke nazo. Zotere ziyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike.
7 Nation will rise against nation, and kingdom against kingdom, with famines and earthquakes in place after place. Mtundu ndi mtundu udzawukirana, ndipo ufumu ndi ufumu udzawukirana. Kudzakhala njala ndi zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana.
8 All these are the beginning of birth pains. Zonsezi ndi chiyambi chabe cha zowawa.
9 Then they will hand you over to suffering and kill you, hated by all nations because of my name. “Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine.
10 At that time many will fall away and will betray and hate one another, Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake,
11 and many false prophets will appear and deceive many people. ndipo aneneri onama ambiri adzaoneka ndi kunyenga anthu ambiri.
12 Because lawlessness will increase, the love of most will grow cold, Chifukwa cha kuchuluka kwa zoyipa, chikondi cha ambiri chidzazirala,
13 but the one who endures to the end will be saved. koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka.
14 This good news of the kingdom will be announced worldwide as a testimony to all nations, and then the end will come. Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika.”
15 So when you see the desolating abomination Daniel the prophet spoke of standing in the holy place—let the reader understand, “Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire.
16 then let those who are in Judea flee to the mountains. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire ku mapiri.
17 "Let no one on the rooftop go down to take anything out of the house, Yemwe ali pa denga la nyumba yake asatsike kukatulutsa chinthu chilichonse mʼnyumba.
18 and let no one in the field go back to get a coat. Yemwe ali ku munda asapite kukatenga mkanjo wake.
19 How dreadful it will be in those days for pregnant women and nursing mothers! Kudzakhala koopsa kwambiri masiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi kwa oyamwitsa!
20 Pray that your flight will not take place in winter or on the Sabbath. Pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzachitike nthawi yozizira kapena pa Sabata.
21 For then there will be great suffering, unmatched from the world's beginning until now, and never to be matched again. Popeza kudzakhala masautso aakulu, omwe safanana ndi ena ali onse chiyambireni cha dziko lapansi mpaka lero lino ndipo sadzafanananso ndi ena.
22 If those days had not been cut short, no one would survive; but for the elect's sake, those days will be cut short. Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.
23 Then if anyone tells you, 'Look, here's the Christ,' or 'There he is,' don't believe it. Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire.
24 False messiahs and false prophets will arise, performing great signs and wonders to deceive, if possible, even the elect. Chifukwa akhristu onama ndi aneneri onama adzaoneka ndipo adzachita zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kuti akanyenge ngakhale osankhidwawo ngati kukanakhala kotheka kutero.
25 See, I have told you ahead of time. Onani, ndakuwuzani izi nthawi isanafike.
26 So if they say, 'Look, he's in the wilderness,' don't go out; 'Look, in the inner rooms,' don't believe it. “Ndiye ngati wina akuwuzani inu kuti, ‘Uyo ali ku chipululu,’ inu musapiteko; kapena akati, ‘Uyu ali kuno mʼchipinda chamʼkati,’ musakhulupirire.
27 For just as lightning flashes from the east and shows as far as the west, so will the Son of Man's coming be. Monga momwe mphenzi ingʼanima kuchokera kummawa kupita kumadzulo, momwemonso kudzakhala kubwera kwa Mwana wa Munthu.
28 Wherever there is a carcass, there the vultures will gather. Kulikonse kuli chinthu cha kufa, makwangwala adzasonkhanako.
29 Right after the suffering of those days, the sun will go dark, the moon will give no light, stars will fall from the sky, and the powers of the heavens will shake. “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, “ ‘dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzawala; nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’
30 Then the sign of the Son of Man will appear in heaven, and all earth's peoples will mourn, seeing the Son of Man come on heaven's clouds with power and great glory. “Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.
31 He will send out his angels with a loud trumpet blast, and they will gather his chosen from the four winds, from one end of the sky to the other. Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.
32 Learn this from the fig tree: as soon as its branch softens and leafs out, you know summer is near. “Tsopano kuchokera ku mtengo wamkuyu phunzirani ichi: Pamene uyamba kuphukira, masamba ake akatuluka, mumadziwa kuti dzinja layandikira.
33 So also, when you see all these things, know it is near, at the door. Momwemonso, pamene mudzaona zinthu zonsezi mudzadziwe kuti ali pafupi pa khomo penipeni.
34 Truly I tell you, this generation will certainly not pass away until all these things have happened. Zoonadi, ndikuwuzani kuti mʼbado uwu sudzatha mpaka zinthu zonse zitachitika.
35 Heaven and earth will pass away, but my words will never pass away. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
36 "No one knows that day or hour—not the angels in heaven, not the Son—only the Father. “Palibe amene adziwa za tsikulo kapena nthawi, angakhale angelo akumwamba, angakhale Mwana, koma Atate okha.
37 As in Noah's days, so will be the Son of Man's coming. Monga momwe zinalili nthawi ya Nowa, momwemonso zidzatero pobwera kwa Mwana wa Munthu.
38 For in the days before the flood, people ate and drank, married and gave in marriage, until the day Noah entered the ark; Pakuti masiku amenewo chisanafike chigumula, anthu amadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo;
39 and they knew nothing until the flood came and swept them all away. That is how the coming of the Son of Man will be. ndipo sanadziwe za chimene chikanachitika mpaka pamene chigumula chinafika ndi kuwamiza onse. Umu ndi mmene zidzakhalira pobwera kwa Mwana wa Munthu.
40 Two men will be in the field; one will be taken and the other left. Amuna awiri adzakhala mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.
41 Two women will be grinding with a hand mill; one will be taken and the other left. Amayi awiri adzakhala akusinja pa mtondo; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.
42 Therefore keep watch, because you do not know on what day your Lord will come. “Chifukwa chake yangʼanirani, popeza simudziwa tsiku lanji limene Ambuye anu adzabwera.
43 Understand: had the homeowner known what watch of night the thief was coming, he'd have watched and kept his house from being broken into. Koma zindikirani ichi: Ngati mwini nyumba akanadziwa nthawi yanji ya usiku imene mbala imabwera, sakanagona ndipo sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe.
44 So you too must be ready, because the Son of Man comes at an hour you don't expect. Inunso tsono muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukumuyembekezera.
45 Who then is the faithful and wise servant, whom the master put in charge of his household to give them food at the right time? “Kodi wantchito wokhulupirika ndi wanzeru amene ambuye ake anamuyika kukhala woyangʼanira antchito a mʼnyumba kuti awapatse chakudya chawo pa nthawi yake ndani?
46 It will be good for that servant whose master finds him doing so when he returns. Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi.
47 Truly I tell you, he will put him in charge of all his possessions. Zoonadi, ndikuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense.
48 But suppose that wicked servant says to himself, 'My master is staying away a long time,' Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo ndi woyipa, nati kwa iye yekha, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera,’
49 and then begins to beat his fellow servants and to eat and drink with drunkards. nayamba kumenya antchito anzake, nadya ndi kumwa ndi zidakwa.
50 That servant's master will come on a day he doesn't expect, at an hour he doesn't know. Mbuye wa wantchitoyo adzabwera pa tsiku limene iye samamuyembekezera ndi pa nthawi imene iye sakuyidziwa.
51 He will cut him to pieces and place him with the hypocrites, where people weep and grind their teeth." Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]