Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Matthew 22 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Jesus spoke to them again in parables, saying: Yesu anayankhula nawonso mʼmafanizo, nati,
2 "The kingdom of our Father is like a king who prepared a wedding feast for his son. “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna.
3 He sent his servants to summon the invited guests to the wedding feast, but they refused to come. Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.
4 Again he sent other servants, saying, 'Tell those invited: Look, I have prepared my dinner; my oxen and fattened cattle are killed, everything ready. Come to the wedding feast.' “Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’
5 But they paid no attention and went off, one to his farm, another to his business, “Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake.
6 while the rest seized his servants, mistreated them, and killed them. Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha.
7 The king was enraged, and he sent his troops, destroyed those murderers, and burned their city. Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.
8 Then he told his servants, 'The wedding is ready, but those invited weren't worthy. “Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera.
9 Go therefore to the main roads and invite to the wedding feast as many as you find.' Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’
10 Those servants went out into the roads and gathered everyone they found, bad and good, and the wedding hall filled with guests. Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.
11 "But when the king came in to see the guests, he saw a man not dressed in wedding clothes. “Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati.
12 He asked, 'Friend, how did you get in here without wedding clothes?' He was speechless. Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete.
13 Then the king told the servants, 'Tie his hands and feet, and throw him into the outer darkness, where there will be weeping and grinding of teeth.' “Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’
14 For many are called, but few are chosen." “Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.”
15 Then the Pharisees went and plotted how to trap him with his own words. Kenaka Afarisi anatuluka nakakonza njira zomupezera zifukwa Yesu mʼmawu ake.
16 They sent their disciples to him, with the Herodians, saying, "Teacher, we know you are truthful and truly teach God's way; you defer to no one, since you don't judge people by rank. Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani?
17 Tell us, then, what you think: Is it lawful to pay taxes to Caesar, or not?" Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”
18 But Jesus, knowing their malice, said, "Why are you testing me, you hypocrites? Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati, “Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa?
19 Show me the coin used for the tax." And they brought him a denarius. Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari,
20 And he said to them, "Whose image is this, and whose inscription?" ndipo anawafunsa kuti, “Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?”
21 They said, "Caesar's." Then he said to them, "So pay Caesar what belongs to Caesar, and our Father what belongs to our Father." Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.” Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
22 When they heard it, they were amazed; and they left him and went away. Atamva izi, anadabwa, ndipo anamusiya Iye, nachoka.
23 That same day Sadducees came to him, who say there is no resurrection, and they asked him, Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso.
24 saying, "Teacher, Moses said: if a man dies childless, his brother must marry the widow and raise offspring for his brother. Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
25 Now there were seven brothers among us. The first married, died, and, childless, left his wife to his brother. Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo.
26 So too the second and the third, down to the seventh. Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri.
27 Last of all, the woman died. Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso.
28 In the resurrection, then, whose wife of the seven will she be? For they all had her." Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”
29 Jesus answered, "You're mistaken—you know neither the Scriptures nor our Father's power. Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu.
30 For in the resurrection people neither marry nor are married off, but are like angels in heaven. Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba.
31 Now, about the resurrection of the dead, haven't you read what our Father told you: Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,
32 'I'm the God of Abraham, of Isaac, and of Jacob'? He's not God of the dead, but of the living." ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”
33 And when the crowds heard it, they were astonished at his teaching. Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.
34 But when the Pharisees heard that he had silenced the Sadducees, they gathered together. Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi.
35 And one of them, an expert in the Law, asked him a question to test him: Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati,
36 "Teacher, which is the great commandment in the Law?" “Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?”
37 He said to him, "Love your Father with all your heart, with all your soul, and with all your mind. Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.
38 This is the great and first commandment. Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse.
39 And a second is like it: You will love your neighbor as yourself. Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’
40 On these two commandments depend all the Law and the Prophets." Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”
41 Now while the Pharisees were gathered together, Jesus asked them, Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti,
42 "What do you think about the Christ? Whose son is he?" They said to him, "David's." “Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”
43 He asked them, "How then does David, by the Holy Spirit, call him Lord, saying, Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,
44 'Our Father said to my Lord, "Sit at my right hand, until I put your enemies under your feet"'? “Ambuye anati kwa Ambuye wanga: ‘Khala pa dzanja langa lamanja mpaka ndiyike adani ako pansi pa mapazi ako.’
45 If then David calls the Christ Lord, how can the Christ be David's son?" Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?”
46 No one could answer him a word, and from that day no one dared ask him anything else. Panalibe wina anatha kuyankha, ndipo kuchokera pamenepo, panalibe wina anayerekeza kumufunsa funso.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]