Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Matthew 15 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Then Pharisees and scribes came to Jesus from Jerusalem and said, Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti,
2 "Why do your disciples break the elders' tradition? They don't wash their hands when they eat." “Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”
3 He answered, "Why do you also break our Father's commandment for your tradition? Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu?
4 For our Father said, 'Honor your father and your mother,' and, 'Whoever curses father or mother must surely be put to death.' Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’
5 But you say, 'Whoever tells his father or mother, "Whatever you gained from me is a gift devoted to our Father," Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’
6 he need not honor his father with it.' You've canceled our Father's word for your tradition's sake. iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu.
7 You hypocrites! Isaiah prophesied rightly about you when he said: Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,
8 'This people honors me with their lips, but their heart is far from me; “ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
9 they worship me in vain, teaching the commandments of men as doctrine.'" Amandilambira Ine kwachabe ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”
10 Then he called the crowd to him and said, "Listen and understand: Yesu anayitana gulu la anthu nati, “Mverani ndipo zindikirani.
11 Not what enters the mouth makes a person unclean, but what comes out of the mouth makes a person unclean." Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”
12 Then the disciples came to him and said, "Do you know the Pharisees were offended hearing this saying?" Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”
13 He replied, "Every plant my heavenly Father didn't plant will be uprooted. Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe.
14 Leave them; they are blind guides. If a blind man guides a blind man, both fall into a pit." Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”
15 Peter said to him, "Explain this parable to us." Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”
16 "Are you still as dull as the others?" Jesus said. Yesu anawafunsa kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa?
17 "Don't you understand that whatever enters the mouth passes into the stomach and is then expelled? Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi?
18 But what comes out of the mouth comes from the heart, and that makes a person unclean. Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa.
19 For the heart produces evil thoughts: murder, adultery, sexual sin, theft, false testimony, slander. Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.
20 These make a person unclean, but eating with unwashed hands does not make anyone unclean." Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”
21 Leaving that place, Jesus withdrew to the region of Tyre and Sidon. Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni.
22 A Canaanite woman from that region came, crying out, "Have mercy on me, Lord, Son of David! My daughter is severely tormented by a demon." Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”
23 He answered her nothing. His disciples came and urged him, "Send her away—she keeps shouting after us." Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”
24 He answered, "I was sent only to the lost sheep of the house of Israel." Iye anayankha kuti, “Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha.”
25 But she came and knelt before him, saying, "Lord, help me!" Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!”
26 He replied, "It is not right to take the children's bread and throw it to the dogs." Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.”
27 "Yes, Lord," she said, "yet even the dogs eat the crumbs that fall from their masters' table." Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”
28 Jesus replied, "Woman, your faith is great. Let it happen as you wish." And her daughter was healed from that hour. Pomwepo Yesu anayankha kuti, “Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.
29 Leaving there, Jesus went along the Sea of Galilee, went up the mountain, and sat down there. Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi.
30 Large crowds came to him with the lame, blind, crippled, mute, and many others, laying them at his feet, and he healed them. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye ndi anthu olumala, osaona, ofa ziwalo, osayankhula ndi ena ambiri nawagoneka pa mapazi ake ndipo Iye anawachiritsa.
31 So the crowd was amazed, seeing the mute speak, the crippled healed, the lame walk, and the blind see; they gave glory to the Father of Israel. Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.
32 Jesus called his disciples to him and said, "I feel for this crowd—they've already been with me three days with nothing to eat. I don't want to send them away hungry; they might collapse on the road." Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira.”
33 The disciples asked, "Where in this remote place could we find enough bread to feed such a crowd?" Ophunzira anayankha kuti, “Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?”
34 "How many loaves do you have?" Jesus asked. "Seven," they said, "and a few small fish." Yesu anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?” Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono.”
35 So he told the crowd to sit down on the ground. Iye anawuza gululo kuti likhale pansi.
36 And he took the seven loaves and fish, gave thanks, broke them, gave them to the disciples, and they gave them to the crowds. Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo.
37 They all ate and were satisfied, and they gathered up seven baskets full of the leftover pieces. Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri.
38 Those who ate were 4,000 men, besides women and children. Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana.
39 After sending the crowds away, he boarded the boat and went to the region of Magadan. Yesu atatha kuwuza gululo kuti lipite kwawo, analowa mʼbwato ndipo anapita kudera la Magadala.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]