Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Matthew 14 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 At that time Herod the tetrarch heard the reports about Jesus. Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu.
2 He told his attendants, "This is John the Baptist, raised from the dead—that's why these powers are at work in him." Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.”
3 For Herod had arrested John, chained him, and locked him in prison over Herodias, his brother Philip's wife, Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo.
4 because John had been telling him, "It is not lawful for you to have her." Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.”
5 Herod wanted to kill him but feared the crowd, since they held John as a prophet. Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri.
6 But when Herod's birthday came, the daughter of Herodias danced before them and pleased Herod, Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri.
7 so he promised with an oath to give her whatever she asked. Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe.
8 Prompted by her mother, she said, "Give me John the Baptist's head here, on a platter." Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”
9 The king was grieved, but because of his oaths and his dinner guests, he gave the order, Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe;
10 and he sent and had John beheaded in the prison. ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende.
11 His head was brought on a platter, given to the girl, who brought it to her mother. Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake.
12 Then John's disciples came, took the body, and buried it; and they went and told Jesus. Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.
13 Hearing this, Jesus withdrew by boat to a remote place alone. But the crowds heard and followed him on foot from the towns. Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda.
14 When he went ashore, he saw a big crowd, felt compassion for them, and healed their sick. Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.
15 When evening came, the disciples said to him, "This is an isolated place, and the hour is already late. Send the crowds away to go into the villages and buy themselves food." Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”
16 But Jesus told them, "They don't need to leave. You feed them." Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”
17 They said to him, "We have nothing here but five loaves and two fish." Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”
18 He said, "Bring them here to me." Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.”
19 He told the crowds to sit on the grass. Taking the five loaves and two fish, he looked up to heaven, gave thanks, broke the loaves, and gave them to the disciples, who gave them to the crowds. Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu.
20 They all ate and were satisfied, and they picked up twelve baskets full of the leftover pieces. Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri.
21 Those who ate were about 5,000 men, besides women and children. Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.
22 Immediately he made the disciples board the boat and go ahead of him to the other side, while he sent the crowds away. Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo.
23 After sending the crowds away, he went up the mountain privately to pray. When evening came, he was there alone. Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha.
24 The boat was already far from land, battered by waves, the wind against them. Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.
25 About three o'clock in the morning he came to them, walking on the sea. Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja.
26 Seeing him walking on the sea, the disciples were terrified, saying, "A ghost!" and cried out in fear. Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.
27 But Jesus spoke to them at once: "Take courage! It is I; do not be afraid." Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.”
28 Peter answered him, "Lord, if it is you, command me to come to you on the water." Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”
29 He said, "Come." Peter got out of the boat, walked on water, and went toward Jesus. Iye anati, “Bwera.” Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu.
30 But seeing the strong wind, he was afraid, and beginning to sink, he cried out, "Lord, save me!" Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”
31 Jesus immediately reached out his hand, caught him, and said, "You of little faith, why did you doubt?" Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”
32 And when they got into the boat, the wind died down. Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka.
33 Then those in the boat worshiped him, saying, "Truly you are the Son of our Father." Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”
34 When they had crossed over, they came to land at Gennesaret. Atawoloka, anafika ku Genesareti.
35 When the men of that place recognized him, they sent word through that whole region and brought him all who were sick. Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye.
36 They begged him to let them just touch the fringe of his robe, and all who touched it were healed. Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]