Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Mark 15 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 At dawn the chief priests, elders, scribes, and the whole council consulted together, bound Jesus, led him away, and handed him over to Pilate. Mmamawa, akulu a ansembe pamodzi ndi akuluakulu, aphunzitsi amalamulo ndi olamulira onse anamanga fundo. Anamumanga Yesu, namutenga ndi kukamupereka kwa Pilato.
2 Pilate asked him, "Are you the King of the Jews?" "You say so," Jesus replied. Pilato anafunsa kuti, “Kodi Iwe ndi Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
3 The chief priests kept accusing him of many things. Akulu a ansembe anamunenera zinthu zambiri.
4 So Pilate questioned him again: "Have you no answer? See how many charges they bring against you." Ndipo Pilato anamufunsanso Iye kuti, “Kodi Iwe suyankhapo kanthu? Tamva zinthu zambiri akukunenerazi.”
5 But Jesus said nothing more, and Pilate was amazed. Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa.
6 Now at the festival, Pilate used to release one prisoner for them—whoever they asked for. Pa nthawi ya Phwando, panali chizolowezi chomasula munthu wamʼndende amene anthu amupempha.
7 A man called Barabbas was in prison with the rebels who had committed murder during the uprising. Munthu wotchedwa Baraba anali mʼndende pamodzi ndi anthu owukira amene anapha anthu pa nthawi ya chipolowe.
8 The crowd came up and began asking Pilate to do for them what he always did. Gulu la anthu linabwera kwa Pilato ndi kumufunsa kuti awachitire zimene amachita nthawi zonse.
9 "Do you want me to release for you the King of the Jews?" Pilate answered, “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” Pilato anafunsa,
10 for he knew it was out of envy that the chief priests had handed him over. podziwa kuti akulu a ansembe anamupereka Yesu kwa iye chifukwa cha nsanje.
11 But the chief priests stirred up the crowd to have him release Barabbas for them instead. Koma akulu a ansembe anasonkhezera anthu kuti Pilato amasule Baraba mʼmalo mwa Yesu.
12 "So what do you want me to do with the one you call King of the Jews?" Pilate asked them again. Pilato anawafunsa kuti, “Kodi nanga ndichite chiyani ndi uyu amene mukumutcha mfumu ya Ayuda?”
13 Crucify him!" they shouted back. Anafuwula kuti, “Mpachikeni!”
14 "Why? What evil has he done?" Pilate asked. But they shouted all the louder, "Crucify him!" Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?” Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!”
15 To satisfy the crowd, Pilate released Barabbas to them. He had Jesus flogged, and handed him over to be crucified. Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.
16 Soldiers led him away into the palace (the governor's headquarters) and called together the whole company of soldiers. Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali.
17 They dressed him in purple, twisted together a crown of thorns, and set it on him. Anamuveka Iye mwinjiro wofiira, kenaka analuka chipewa cha minga ndi kuyika pa mutu pake.
18 And they began to salute him: "Hail, King of the Jews!" Ndipo anayamba kunena kwa lye kuti, “Ulemu kwa inu Mfumu ya Ayuda!”
19 They kept beating his head with a staff, spat on him, and knelt in mock homage to him. Ndipo anamugogoda pa mutu mobwerezabwereza ndi ndodo ndi kumulavulira. Anamugwadira ndi kumulambira Iye.
20 After mocking him, they stripped off the purple and put his own clothes on him, then led him out to crucify him. Ndipo anamuchita chipongwe, anamuvula mwinjiro wofiira uja ndi kumuveka zovala zake. Kenaka anamutenga kuti akamupachike.
21 They forced a passerby coming from the countryside—Simon of Cyrene, father of Alexander and Rufus—to carry his cross. Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda.
22 They brought Jesus to the place called Golgotha (which means Place of a Skull). Anafika naye Yesu pa malo otchedwa Gologota (kutanthauza kuti, malo a bade)
23 They offered him wine mixed with myrrh, but he did not take it. Kenaka anamupatsa Iye vinyo wosakaniza ndi mure, koma Iye sanamwe.
24 They crucified him. They divided his clothes among them, casting lots for what each would get. Ndipo anamupachika Iye. Anachita maere ogawana zovala zake kuti aone chimene aliyense angatenge.
25 It was nine in the morning when they crucified him. Linali ora lachitatu mmawa pamene anamupachika Yesu.
26 The written notice of the charge against him read: THE KING OF THE JEWS. Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: mfumu ya ayuda.
27 They crucified two rebels with him, one on his right and one on his left. Achifwamba awiri anapachikidwanso pamodzi ndi Iye, wina kumanja kwake ndi wina kumanzere kwake.
28 Not in this edition (Ndipo malemba anakwaniritsidwa amene amati, “Iye anayikidwa mʼgulu la anthu oyipa).”
29 Those passing by insulted him, shaking their heads, saying, "Ha! You who tear down the temple and build it in three days, Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu,
30 save yourself and come down from the cross!" tsika kuchoka pa mtandapo ndipo udzipulumutse wekha!”
31 Likewise the chief priests and scribes mocked him among themselves: "He saved others; himself he can't save. Chimodzimodzinso akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamunyoza Iye pakati pawo. Iwo anati, “Anapulumutsa ena, koma sangathe kudzipulumutsa yekha!
32 Let the Christ, King of Israel, come down from the cross now, so we can see and believe." Those crucified with him also insulted him. Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira.
33 At noon, darkness came over the whole land until three in the afternoon. Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana.
34 At three in the afternoon Jesus cried out loudly, "Eloi, Eloi, lema sabachthani?" meaning, "My God, my God, why have you forsaken me?" Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?”
35 When some of those standing nearby heard this, they said, "Listen, he's calling Elijah." Ena amene anali pafupi atamva izi anati, “Tamverani, akuyitana Eliya.”
36 One ran, filled a sponge with sour wine, put it on a reed, and gave him a drink. "Let him be," he said, "let's see if Elijah comes to take him down." Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”
37 With a loud cry, Jesus breathed his last. Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza.
38 And the curtain of the temple was torn in two from top to bottom. Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi.
39 The centurion facing Jesus saw how he breathed his last and said, "Truly this man was the Son of God." Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.”
40 Women were also watching from a distance, including Mary Magdalene, Mary the mother of James the younger and Joses, and Salome. Amayi ena anali patali kuonerera. Pakati pawo panali Mariya Magadalena, Mariya amayi a Yakobo wamngʼono ndi Yose ndi Salome.
41 These women had followed him in Galilee and served him; many others who came up with him to Jerusalem were also there. Amayi awa ankamutsatira Iye mu Galileya ndi kumutumikira Iye pa zosowa zake. Amayi enanso ambiri amene anabwera naye ku Yerusalemu analinso pomwepo.
42 Evening had come, and since it was Preparation Day—the day before the Sabbath. Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira,
43 Joseph of Arimathea, a prominent council member who himself was waiting for the kingdom of our Father, dared to go to Pilate and ask for Jesus' body. Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu.
44 Pilate was surprised he was already dead; summoning the centurion, he asked if Jesus had been dead long. Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale.
45 When he learned from the centurion that it was so, he granted the body to Joseph. Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe.
46 Joseph bought linen, took the body down, wrapped it in the cloth, and laid it in a tomb cut from rock. Then he rolled a stone against the tomb's entrance. Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo.
47 Mary Magdalene and Mary the mother of Joses saw where he was laid. Mariya Magadalena ndi Mariya amayi a Yose anaona kumene anamuyika Yesu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]