1Two days before Passover and Unleavened Bread, the chief priests and scribes were looking for a way to seize Jesus by trickery and kill him.OCCLTsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha.
2For they said, "Not during the feast, or the people might riot."OCCLIwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”
3While he was in Bethany, in Simon the leper's house, reclining at the table, a woman came with an alabaster flask of pure nard perfume, very costly. She broke the flask and poured it on his head.OCCLPamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.
4There were some who said to themselves indignantly, "Why was this perfume wasted like that?OCCLEna mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa?
5For this perfume could have sold for over 300 denarii and given to the poor." And they scolded her.OCCLAkanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.
6But Jesus said, "Leave her alone. Why trouble her? She has done a beautiful thing for me.OCCLYesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino.
7For the poor are always with you, and you can do good for them whenever you want; but you won't always have me.OCCLAnthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse.
8She has done what she could; she has anointed my body beforehand for burial.OCCLWachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda.
9Truly, I tell you, wherever the gospel is preached worldwide, what she did will be told in memory of her."OCCLZoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”
10Then Judas Iscariot, one of the twelve, went to the chief priests to betray Jesus to them.OCCLKenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu.
11Hearing this, they were glad and promised him money. So he looked for a chance to betray Jesus.OCCLIwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.
12On the first day of Unleavened Bread, when they sacrificed the Passover lamb, his disciples asked him, "Where do you want us to go and prepare for you to eat the Passover?"OCCLPa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”
13He sent two of his disciples, "Go into the city; a man carrying a jar of water will meet you. Follow him,OCCLPamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye.
14and wherever he enters, tell the house's owner, 'The Teacher says: Where is my guest room, where I may eat the Passover with my disciples?'OCCLKawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’
15And he will show you a large upper room furnished and ready; there prepare for us."OCCLIye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.”
16The disciples left, went to the city, found things as he had told them, and prepared the Passover.OCCLOphunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.
17And when it was evening, Jesus came with the twelve.OCCLNdipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo.
18While they reclined and ate, Jesus said, "Truly, I tell you, one of you will betray me, one eating with me."OCCLPamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.”
19They began to grieve and ask him, one by one, "Is it I?"OCCLIwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”
20He said to them, "One of the twelve, dipping bread with me into the dish.OCCLIye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine.
21The Son of Man goes as the Scriptures said about him, but how terrible for that man who betrays him—better if he had never been born."OCCLMwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
22As they ate, he took bread, blessed it, broke it, gave it to them, and said, "Take; this is my body."OCCLPamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”
23He took a cup, gave thanks, gave it to them, and they all drank from it.OCCLKenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.
24He said to them, "This is my blood of the covenant, poured out for many.OCCLIye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri.
25Truly I tell you, I will not drink wine again until that day when I drink it new in the kingdom of our Father."OCCLZoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”
26And when they had sung a hymn, they went out to the Mount of Olives.OCCLAtayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.
27Jesus said to them, "You will all stumble, for it's written: 'I will strike the shepherd, and the sheep will be scattered.'OCCLYesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “ ‘Kantha Mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’
28But after I am raised up, I will go ahead of you to Galilee."OCCLKoma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”
29Peter said to him, "Even though they all fall away, I will not."OCCLPetro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.”
30Jesus said to him, "Truly I tell you, today, this night, before the rooster crows twice, you will deny me three times."OCCLYesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.”
31But he insisted, "Even if I must die with you, I will never deny you." They all said the same.OCCLKoma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.
32They arrived at a place called Gethsemane, and he told his disciples, "Sit here while I pray."OCCLNdipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.”
33He took Peter, James, and John, and began to feel deep distress and anguish.OCCLIye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima.
34He said to them, "My soul is crushed with grief, to death. Stay here and stay alert."OCCLIye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.”
35Going a little farther, he fell to the ground and prayed that, if possible, the hour would pass from him.OCCLAtapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire.
36He said, "Abba, Father, all things are possible for you. Take this cup from me—but let it be your will, not mine."OCCLIye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”
37He returned, found them asleep, and said to Peter, "Simon, are you asleep? Couldn't you stay awake one hour?OCCLKenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi?
38Watch and pray, so you don't fall into temptation. The spirit is willing, but the flesh is weak."OCCLKhalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”
39And again he went away and prayed, saying the same words.OCCLKenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi.
40Again he found them sleeping, eyes heavy, not knowing how to answer him.OCCLIye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.
41He came a third time and said, "Still sleeping and resting? Enough—the hour has come. Look, the Son of Man is handed over into the hands of sinners.OCCLAtabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa.
42Rise, let us be going; see, my betrayer is here."OCCLNyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!”
43While he was still speaking, Judas—one of the twelve—arrived, and with him a crowd with swords and clubs from the chief priests, scribes, and elders.OCCLIye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.
44His betrayer had given them a signal: "The one I kiss is him—seize him and take him away securely."OCCLTsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.”
45He came up to Jesus at once, said, "Rabbi!" and kissed him.OCCLAtapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona.
46And they laid hands on him and seized him.OCCLAnthu anamugwira Yesu ndi kumumanga.
47One of the bystanders drew his sword, struck the high priest's servant, and cut off his ear.OCCLKenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake.
48Jesus said to them, "Have you come out with swords and clubs to seize me, like a robber?OCCLYesu anati, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira, kuti mubwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira?
49Every day I was with you in the temple teaching, and you didn't arrest me. But let the Scriptures be fulfilled."OCCLTsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.”
50And they all left him and fled.OCCLPamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.
51And a young man followed him, wearing nothing but a linen cloth. And they seized the young man,OCCLMnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira,
52but he left the linen cloth and ran away naked.OCCLanathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo.
53They led Jesus to the high priest, and all the chief priests and elders and scribes gathered.OCCLAnamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi.
54Peter had followed at a distance, all the way into the high priest's courtyard, and sat with the guards, warming himself by the fire.OCCLPetro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.
55The chief priests and the whole council sought testimony against Jesus to put him to death, but found none.OCCLAkulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse.
56For many gave false testimony against him, but their testimony did not agree.OCCLAmbiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane.
57And some stood up and gave false testimony against him, saying,OCCLKenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti,
58"We heard him say, 'I will destroy this temple made by hands, and in three days build another not made by hands.'"OCCL“Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ”
59Yet even about this their testimony did not agree.OCCLNgakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane.
60The high priest stood up in the midst and asked Jesus, "You have no answer? What are these men testifying against you?"OCCLKenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?”
61He stayed silent, answered nothing. Again the high priest asked him, "Are you the Christ, the Son of the Blessed?"OCCLKoma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe. Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?”
62Jesus said, "I AM, and you will see the Son of Man seated at the right hand of the Mighty One and coming with heaven's clouds."OCCLYesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”
63And the high priest tore his clothes and said, "What further witnesses do we need?OCCLMkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso?
64You have heard his blasphemy. What is your decision?" And they all condemned him as deserving death.OCCLMwamva mwanowo. Muganiza chiyani?” Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa.
65Some began spitting on him, covering his face, and punching him, saying to him, "Prophesy!" Then the guards slapped him.OCCLKenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.
66While Peter was below in the courtyard, one of the high priest's servant girls came,OCCLPetro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera.
67seeing Peter warming himself, she looked at him and said, "You too were with the Nazarene, Jesus."OCCLAtaona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa. Iye anati, “Iwenso unali pamodzi ndi Mnazareti, Yesu.”
68But he denied it: "I don't know or understand what you mean." Then he went out to the entrance, and a rooster crowed.OCCLKoma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata.
69The servant girl saw him and again told the bystanders, "This man is one of them."OCCLPamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.”
70But he denied it again. A little later the bystanders again told Peter, "You truly are one of them, for you're a Galilean."OCCLAnakananso kachiwiri. Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.”
71He began to call down curses on himself and swear, "I don't know this man you're talking about."OCCLIye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.”
72At once a rooster crowed a second time. Peter remembered Jesus' words: "Before the rooster crows twice, you will deny me three times." He broke down and wept.OCCLNthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.