Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Mark 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The beginning of the gospel of Jesus Christ, the Son of our Father. Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu,
2 As written in Isaiah the prophet: "Look, I send my messenger ahead of you, who will prepare your way. monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya: “Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu, amene adzakonza njira yanu,”
3 A voice calling out in the wilderness: 'Prepare the way of the Lord, make his paths straight.'" “Mawu a wofuwula mʼchipululu, ‘Konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.’ ”
4 John appeared, baptizing in the wilderness and proclaiming a baptism of repentance for the forgiveness of sins. Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo.
5 All Judea and everyone in Jerusalem went out to him, and he baptized them in the Jordan River as they confessed their sins. Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani.
6 John was dressed in camel's hair, with a leather belt around his waist, eating locusts and wild honey. Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo.
7 He announced: "After me comes one stronger than I; I'm not worthy to stoop and untie his sandal strap. Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake.
8 I have baptized you with water, but he will baptize you with the Holy Spirit." Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
9 In those days Jesus came from Nazareth of Galilee and was baptized by John in the Jordan. Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani.
10 Immediately, as he came up out of the water, he saw the heavens split open and the Holy Spirit come down on him like a dove. Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda.
11 And a voice came from heaven: "You are my beloved Son; in you I delight." Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
12 And immediately the Holy Spirit drove him out into the wilderness. Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu,
13 He was in the wilderness forty days, tempted by Satan, with the wild animals, and the angels served him. ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
14 Now after John was arrested, Jesus came into Galilee, proclaiming the gospel of our Father, Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati,
15 and saying, "The time is fulfilled, and our Father's kingdom is near; repent and believe the good news." “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
16 Passing the Sea of Galilee, he saw Simon and his brother Andrew casting a net in the sea, for they were fishermen. Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi.
17 And Jesus said to them, "Follow me, and I will make you become fishers of people." Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”
18 And immediately they left their nets and followed him. Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
19 Going a little farther, he saw James son of Zebedee and John his brother in their boat, mending the nets. Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo.
20 At once he called them; leaving their father Zebedee in the boat with the hired hands, they followed him. Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.
21 They went to Capernaum. At once, on the Sabbath, he entered the synagogue and began teaching. Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa.
22 They were amazed at his teaching, for he taught them with authority, not like the scribes. Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo.
23 And immediately there was in their synagogue a man with an unclean spirit, and he cried out. Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti,
24 Why meddle with us, Jesus of Nazareth? Have you come to destroy us? I know who you are—God's Holy One! “Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
25 But Jesus rebuked him, saying, "Be silent, and come out of him!" Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye!”
26 And the unclean spirit, convulsing him and crying out with a loud voice, came out of him. Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.
27 All were amazed, and they questioned each other: "What is this? A new teaching with authority - he commands even the unclean spirits, and they obey him!" Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.”
28 And at once his fame spread everywhere throughout all the surrounding region of Galilee. Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira.
29 Immediately he left the synagogue and went to Simon and Andrew's house, with James and John. Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya.
30 Now Simon's mother-in-law lay sick with a fever, and immediately they told him about her. Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye.
31 He came, took her hand, raised her up. The fever left her, and she served them. Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.
32 That evening, when the sun set, they brought him all who were sick and those oppressed by demons. Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda.
33 And the whole city was gathered together at the door. Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo,
34 He healed many sick with various diseases and drove out many demons, not letting the demons speak, since they knew him. Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.
35 Long before dawn, while still dark, he got up, went out to a deserted place, and prayed there. Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera.
36 And Simon and those who were with him searched for him, Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye,
37 and they found him and said to him, "Everyone is looking for you." ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”
38 He said, "Let us go elsewhere, to the neighboring towns, so I can preach there too, for that is why I came." Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.”
39 And he went throughout all Galilee, preaching in their synagogues and casting out demons. Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.
40 A man with leprosy came, knelt, and begged him, "If you're willing, you can make me clean." Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
41 Moved with deep compassion, he stretched out his hand, touched him, and said to him, "I am willing; be clean." Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!”
42 And immediately the leprosy left him, and he was made clean. Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.
43 Sternly warning him, he sent him away at once, Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti,
44 and told him, "Make sure you tell no one—but go, show yourself to the priest, and offer what Moses commanded for your cleansing, as proof to the people." “Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.”
45 But he went out, proclaiming it freely and spreading the news, so Jesus could no longer enter a town openly, but stayed in lonely places. Yet people came to him from everywhere. Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]