Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 9 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Jesus called the twelve together, gave them power and authority over all the demons and to heal diseases. Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda.
2 And he sent them out to proclaim the kingdom of our Father and to heal the sick. Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala.
3 He said to them, "Take nothing for the road: no staff, bag, bread, or money, and don't take two tunics each. Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera.
4 Whatever house you enter, stay there, and leave from there. Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo.
5 Wherever they won't welcome you, shake the dust off your feet as you leave that town, as a testimony against them." Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.”
6 So they set out and went from village to village, proclaiming the good news and healing everywhere. Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse.
7 Herod the tetrarch heard all that was happening, and was puzzled, because some said John had been raised from the dead, Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa,
8 others that Elijah had appeared, and still others that one of the prophets of old had risen. ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.
9 Herod said, "I beheaded John—so who is this I hear such things about?" He kept seeking to see him. Koma Herode anati, “Ine ndinamudula mutu Yohane. Nanga uyu ndani amene ndikumva zinthu zotere za Iye?” Ndipo iye anayesetsa kuti amuone Iye.
10 When the apostles returned, they told Jesus all they had done. He took them and withdrew privately to a town called Bethsaida. Atumwi atabwerera, anamuwuza Yesu zimene anachita. Kenaka Iye anawatenga napita kwa okha ku mudzi wa Betisaida.
11 But the crowds found out and followed him. He welcomed them, spoke to them of our Father's kingdom, and healed those who needed it. Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso.
12 As the day was ending, the Twelve came and said to him, "Send the crowd away to find lodging and food in the villages and countryside around us—we're in a remote place here." Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.”
13 He said, "You give them something to eat." They said, "We have only five loaves and two fish—unless we go and buy food for this whole crowd." Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.” Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.”
14 For there were about 5,000 men. He told his disciples, "Seat them in groups of about fifty each." (Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000). Koma Iye anati kwa ophunzira ake, “Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu.”
15 They did so, and had everyone sit down. Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi.
16 He took the five loaves and two fish, looked up to heaven, blessed and broke them, then kept giving them to the disciples to serve the crowd. Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu.
17 All ate and were satisfied; the leftover pieces filled twelve baskets. Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala.
18 Once, while praying alone with his disciples nearby, Jesus asked them, "Who do the crowds say I am?" Nthawi ina pamene Yesu amapemphera malo a yekha ali ndi ophunzira ake, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”
19 They answered, "John the Baptist. Others say Elijah. Still others, that an ancient prophet has risen." Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.”
20 "But who do you say that I am?" he asked. Peter answered, "The Christ of our Father." Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?” Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”
21 Jesus strictly warned them, ordering them to tell no one this, Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi.
22 saying, "The Son of Man must suffer many things and be rejected by the elders, chief priests, and scribes, and be killed, and on the third day be raised." Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”
23 Then he told them all, "Whoever wants to come after me must deny himself and take up his cross daily and follow me. Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine.
24 For whoever intends to save his life will lose it, but whoever loses his life because of me will save it. Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa.
25 For what use is it if someone gains the whole world, yet loses or forfeits himself? Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini?
26 Whoever is ashamed of me and my words, the Son of Man will be ashamed of him when he comes in his own glory and the glory of the Father and the holy angels. Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.
27 But I tell you truly, some standing here will not taste death before they see the kingdom of our Father." Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”
28 About eight days after these words, Jesus took Peter, John, and James up a mountain to pray. Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera.
29 As he was praying, the appearance of his face changed, and his clothing became dazzling white. Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri.
30 And there were two men talking with him—Moses and Elijah, Anthu awiri, Mose ndi Eliya,
31 who appeared in glory, speaking of his departure, which he was about to fulfill in Jerusalem. anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu.
32 Peter and his companions were weighed down with sleep; fully awake, they saw his glory and the two men standing with him. Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye.
33 As they were leaving him, Peter said to Jesus, "Master, it's good we're here. Let's make three shelters—one for you, one for Moses, one for Elijah." He didn't know what he was saying. Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, “Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya.” (Iye sanadziwe chimene amayankhula).
34 As he spoke, a cloud came and covered them in shadow; entering it, they were afraid. Pamene Iye ankayankhula, mtambo unaonekera ndi kuwaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene mtambowo unawakuta.
35 A voice from the cloud said, "This is my Son, my Chosen One—listen to him!" Mawu anachokera mu mtambomo nati, “Uyu ndi Mwana wanga amene ndamusankha; mumvereni Iye.”
36 When the voice ended, Jesus was found alone. They stayed silent, telling no one in those days what they had seen. Atamveka mawuwa, anaona kuti Yesu anali yekha. Ophunzirawo anazisunga izi mwa iwo okha ndipo sanawuze wina aliyense pa nthawiyi za zomwe iwo anaziona.
37 The next day, when they came down from the mountain, a large crowd met him. Mmawa mwake, akutsika ku phiri, anthu ambiri anakumana naye.
38 A man from the crowd shouted, "Teacher, please look at my son, because he's my only child. Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, “Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu.
39 A spirit seizes him, and suddenly he cries out; it convulses him until he foams, scarcely leaving him, battering him. Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga.
40 I begged your disciples to drive it out, but they could not." Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera.”
41 Jesus answered, "Distrustful, twisted generation, how long must I stay with you and endure you? Bring your son here." Yesu anayankha kuti, “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”
42 As the boy was coming, the demon threw him down and convulsed him. But Jesus rebuked the unclean spirit, healed the boy, and returned him to his father. Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake.
43 All were astonished at our Father's majesty. While everyone was amazed at everything Jesus did, he said to his disciples, Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu. Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake,
44 "Store these words in your ears: the Son of Man will soon be delivered into human hands." “Tamvetsetsani zimene ndikufuna kukuwuzani: Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.”
45 But they didn't understand this word—hidden from them so they couldn't grasp it—and they were afraid to ask him about it. Koma iwo sanazindikire zimene amatanthauza. Izi zinawadabwitsa kotero sanathe kuzimvetsa ndipo anaopa kumufunsa.
46 Now an argument arose among them as to which of them was the greatest. Mkangano unayambika pakati pa ophunzira wa kuti wamkulu koposa akanakhala ndani mwa iwo.
47 But Jesus, knowing their hearts' thoughts, took a child and stood him beside himself, Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake.
48 and told them, "Whoever receives this child in my name receives me, and whoever receives me receives the one who sent me. For the least among you all—that one is great." Ndipo Iye anawawuza kuti, “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”
49 John said, "Master, we saw someone driving out demons in your name and tried to stop him, because he doesn't follow with us." Yohane anati, “Ambuye, ife tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo tinayesa kumuletsa, chifukwa iyeyo si mmodzi wa ife.”
50 "Do not stop him," Jesus said to him, "for whoever is not against you is for you." Yesu anati, “Wosamuletsa, pakuti amene satsutsana nanu ali mbali yanu.”
51 When the days neared for him to be taken up to heaven, Jesus resolutely set his face to go to Jerusalem. Nthawi itayandikira yoti Iye atengedwe kupita kumwamba, Yesu anatsimikiza zopita ku Yerusalemu,
52 He sent messengers ahead of him. They went and entered a Samaritan village to prepare for him, ndipo anatuma nthumwi kuti zitsogole. Iwo anapita mʼmudzi wa Asamariya kuti akonzekere kumulandira,
53 but the people there did not welcome him, because he was heading for Jerusalem. koma anthu kumeneko sanamulandire chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu.
54 Seeing this, the disciples James and John said, "Lord, do you want us to call down fire from heaven to consume them?" Ophunzira awa, Yohane ndi Yakobo ataona zimenezi, anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukufuna ife tiyitane moto kuchokera kumwamba kuti uwawononge?”
55 But he turned and rebuked them. Koma Yesu anatembenuka ndi kuwadzudzula,
56 And they went on to another village. ndipo iwo anapita ku mudzi wina.
57 As they walked the road, someone said to him, "I'll follow you wherever you go." Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.”
58 Jesus said, "Foxes have dens, birds of the sky have nests, but the Son of Man has nowhere to lay his head." Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake.”
59 To another he said, "Follow me." He replied, "Lord, first let me go bury my father." Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.” Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.”
60 But Jesus told him, "Let the dead bury their own dead, but you go proclaim the kingdom of our Father." Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”
61 Another also said, "I'll follow you, Lord, but first let me say goodbye to those at my house." Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.”
62 Jesus replied, "No one who puts a hand to the plow and looks back is fit for our Father's kingdom." Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]