Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 45 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 This is what our Father says to his anointed, to Cyrus, whose right hand I have grasped to subdue nations before him and to strip kings of their armor, to open doors before him so that gates will not be shut: Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake Koresi amene anamugwira dzanja lamanja kuti agonjetse mitundu ya anthu ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo, ndi kutsekula zitseko kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
2 I will go before you and level the mountains; I will shatter the doors of bronze and cut through the bars of iron. Ine ndidzayenda patsogolo pako, ndi kusalaza mapiri; ndidzaphwanya zitseko za mkuwa ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
3 I will give you the treasures of darkness and hoards stored in secret places, so that you may know that I am the Father of Israel, who calls you by your name. Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima, katundu wa pamalo obisika, kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
4 For the sake of my servant Jacob, and Israel my chosen, I have called you by your name; I give you a title of honor, though you do not know me. Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo, chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli, Ine ndakuyitana pokutchula dzina ndipo ndakupatsa dzina laulemu ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
5 I am the Father, and there is no other; besides me there is none. I equip you for battle, though you do not know me, Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina; kupatula Ine palibenso Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu, ngakhale sukundidziwa Ine,
6 so that people may know, from the rising of the sun to the place of its setting, that there is none besides me. I am the Father, and there is no other. kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha. Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
7 I form light and create darkness, I make well-being and create calamity; I am the Father, who does all these things. Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
8 Rain down, O heavens, from above, and let the skies pour down righteousness; let the earth open wide, that salvation may bear fruit and righteousness spring up together. I, the Father, have created it. “Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba; mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo. Dziko lapansi litsekuke, ndipo chipulumutso chiphuke kuti chilungamo chimereponso; Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.
9 Woe to the one who quarrels with his Maker—a pottery shard among the shards of the earth! Does the clay say to the one who forms it, "What are you making?" or, "Your work has no handles"? “Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake, ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti, ‘Kodi ukuwumba chiyani?’ Kodi ntchito yako inganene kuti, ‘Ulibe luso?’
10 Woe to the one who says to a father, "What are you fathering?" or to a woman, "What are you bringing to birth?" Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti, ‘Kodi munabereka chiyani?’ Kapena amayi ake kuti, ‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’
11 This is what the Holy One of Israel—our Father—and the one who formed him—says: Will you question me about my children, and give me orders about the work of my hands? “Yehova Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena, zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi: Kodi iwe ukundifunsa za ana anga, kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
12 I made the earth and created humanity upon it. It was my hands that stretched out the heavens, and I commanded all their host. Ndine amene ndinapanga dziko lapansi ndikulenga munthu kuti akhalemo. Ine ndi manja anga ndinayalika thambo; ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
13 I have stirred him up in righteousness, and I will make all his ways straight. He will rebuild my city and set my exiles free, not for price or reward, says the Father of heaven's armies. Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe: ndipo ndidzawongolera njira zake zonse. Iye adzamanganso mzinda wanga ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo, wopanda kupereka ndalama kapena mphotho, akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
14 Our Father says: The wealth of Egypt and the merchandise of Cush, and the Sabeans, men of stature, will come over to you and be yours; they will follow behind you, coming over in chains. They will bow down to you and plead with you, saying, "Surely God is with you, and there is no other; there is none besides him." Yehova akuti, “Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu. Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba adzabwera kwa inu ndipo adzakhala anthu anu; iwo adzidzakutsatani pambuyo panu ali mʼmaunyolo. Adzakugwadirani ndi kukupemphani, ponena kuti, ‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina; palibenso mulungu wina.’ ”
15 Truly you are a Father who has hidden yourself, the Father of Israel, the Savior. Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
16 All of them are ashamed and disgraced; the makers of idols go off together in confusion. Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa. Adzakhala osokonezeka maganizo.
17 But Israel is saved by our Father with an everlasting salvation; you will not be ashamed or disgraced for all eternity. Koma Yehova adzapulumutsa Israeli ndi chipulumutso chamuyaya; simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka mpaka kalekale.
18 For this is what the Father says, who created the heavens—he is the Father!—who formed the earth and made it; he established it. He did not create it empty; he formed it to be inhabited: I am the Father, and there is no other. Yehova analenga zinthu zakumwamba, Iye ndiye Mulungu; amene akulenga dziko lapansi, ndi kulikhazikitsa, sanalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma analipanga kuti anthu akhalemo. Iyeyu akunena kuti: Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
19 I did not speak in secret, in a land of darkness; I did not say to the descendants of Jacob, "Seek me in vain." I, your Father, speak what is right; I declare what is true. Ine sindinayankhule mwachinsinsi, pamalo ena a mdima; Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti, “Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.” Ine Yehova, ndimayankhula zoona; ndikunena zolungama.
20 Gather together and come; draw near, you survivors of the nations! They have no knowledge—those who carry around their wooden idols and keep praying to a god that cannot save. Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere; yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina. Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo, amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
21 Declare and present your case; let them consult together! Who foretold this long ago and declared it from ancient times? Was it not I, the Father? There is no other besides me—a righteous Father and a Savior; there is none besides me. Fotokozani mlandu wanu, mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale? Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana? Kodi si Ineyo Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine, Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa, palibenso wina kupatula Ine.
22 Turn to me and be saved, all the ends of the earth! For I am the Father, and there is no other. “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke, inu anthu onse a pa dziko lapansi, pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
23 By myself I have sworn; a word has gone out from my mouth in righteousness that will not return: To me every knee will bow, every tongue will swear allegiance. Ndalumbira ndekha, pakamwa panga patulutsa mawu owona, mawu amene sadzasinthika konse akuti, bondo lililonse lidzagwada pamaso panga; anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
24 They will say of me, "Only in God are righteousness and strength." To him all who raged against him will come, and they will be ashamed. Iwo adzanene kwa Ine kuti, ‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ” Onse amene anamuwukira Iye adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
25 In our Father all the children of Israel will be justified, and in him they will glory. Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli zidzapambana ndi kupeza ulemerero.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]