Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Exodus 17 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 All Israel's community left the Wilderness of Sin, journeying stage by stage as our Father commanded, and camped at Rephidim—but there was no water for the people to drink. Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa.
2 The people argued with Moses: "Give us water to drink." Moses replied, "Why argue with me? Why test our Father?" Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.” Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?”
3 The people were thirsty there for water and grumbled against Moses, saying, "Why did you bring us up from Egypt to kill us and our children and our livestock with thirst?" Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?”
4 Moses cried out to our Father, "What should I do with this people? They're about to stone me." Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.”
5 Our Father said to Moses, "Go ahead of the people. Take some elders of Israel with you, and take in your hand the staff you struck the Nile with, then go. Yehova anati kwa Mose, “Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka.
6 I will stand there before you on the rock at Horeb. Strike the rock, and water will come out of it for the people to drink." Moses did so as Israel's elders watched. Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli.
7 He named the place Massah and Meribah, because the people of Israel quarreled and tested our Father, asking, "Is our Father among us or not?" Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?”
8 Then Amalek came and fought against Israel at Rephidim. Amaleki anabwera ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraeli.
9 Moses said to Joshua, "Choose men for us, and go out to fight Amalek. Tomorrow I will stand on the hilltop with our Father's staff in my hand." Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.”
10 Joshua did as Moses said and fought Amalek; Moses, Aaron, and Hur went up to the hilltop. Ndipo Yoswa anachitadi monga Mose anamulamulira. Iye anapita kukamenyana ndi Aamaleki ndipo Mose, Aaroni ndi Huri anapita pamwamba pa phiri.
11 Now whenever Moses held up his hand, Israel prevailed; but whenever he lowered his hand, Amalek prevailed. Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana.
12 Moses' hands grew heavy, so they set a stone under him and he sat on it, while Aaron and Hur supported his hands, one on each side, so they stayed steady until sunset. Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa.
13 And Joshua overwhelmed Amalek and his people with the edge of the sword. Kotero Yoswa anagonjetsa asilikali ankhondo a Amaleki ndi lupanga.
14 Our Father told Moses, "Write this in a book as a reminder, and recite it aloud to Joshua: I will completely erase Amalek's memory from under heaven." Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”
15 Moses built an altar and named it "Our Father Is My Banner," Mose anamanga guwa lansembe ndipo analitcha Yehova Chipambano Changa (Yehova Nisi).
16 and he said, "For a hand is on the throne of our Father: He will war against Amalek generation after generation." Ndipo anati, “Kwezani mbendera ya Yehova. Yehova adzachitabe nkhondo ndi mibado yonse ya Aamaleki.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]