Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Deuteronomy 8 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Carefully obey every commandment I'm giving you today, so you may live, multiply, enter, and possess the land our Father swore to your ancestors. Samalani potsata lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mukhale ndi moyo ndi kuchulukana kuti mulande ndi kulowa mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu.
2 Remember the whole way your Father led you these forty years in the wilderness, to humble and test you, to know what was in your heart—whether you would keep his commandments or not. Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi.
3 He humbled you, made you hungry, then fed you manna which neither you nor your ancestors knew, to teach you that man does not live by bread alone, but by every word from the mouth of our Father. Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.
4 Your clothing did not wear out on you, nor your feet swell, these forty years. Mʼzaka makumi anayi zimenezi, zovala zanu sizinangʼambike ndipo mapazi anu sanatupe.
5 Know then in your heart that, as a man disciplines his son, so your Father disciplines you. Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.
6 So keep the commandments of your Father, walking in his ways and fearing him. Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye.
7 For your Father is bringing you into a good land—a land of streams, springs, and deep waters flowing through valleys and hills, Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino, dziko lokhala ndi mitsinje ndi mathawale a madzi, akasupe oyenderera mu zigwa ndi mʼmapiri,
8 a land of wheat and barley, vines, figs, and pomegranates; a land of olive oil and honey. dziko lokhala ndi tirigu ndi barele, mpesa ndi mitengo ya mkuyu, makangadza, mafuta a olivi ndi uchi;
9 A land where you'll eat bread without scarcity, lacking nothing—a land of iron stone, whose hills you'll dig for copper. dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa.
10 When you have eaten and are full, you are to bless your Father for the good land he gave you. Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.
11 Be careful not to forget your Father, failing to keep his commandments, rules, and statutes I command you today, Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero,
12 for when you have eaten and are full, and have built fine houses and live in them, kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo,
13 and your herds and flocks multiply, your silver and gold multiply, and all you have multiplies, ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka,
14 then your heart grows proud, and you forget your Father, who brought you from the land of Egypt, from the house of slavery, mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo.
15 who led you through that vast, dreadful wilderness of venomous snakes and scorpions, of drought and no water, who brought you water out of flint rock, Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma.
16 who fed you manna in the wilderness, unknown to your ancestors, to humble and test you, and in the end do you good. Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino.
17 Watch out—don't say in your heart, "My power, my hand's strength, made this wealth for me." Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.”
18 Remember your Father, for he gives you power to gain wealth, to confirm his covenant that he swore to your ancestors, as it is today. Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.
19 But if you ever forget your Father, go after other gods, serve and bow down to them, I testify against you today: you will surely perish. Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu.
20 Like the nations our Father destroys before you, you too will perish, since you would not obey your Father's voice. Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]