Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Colossians 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Then, since you were raised with Christ, seek what is above, where Christ is seated at the right hand of our Father. Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
2 Set your minds on the things above, not on the things of the earth. Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.
3 For you have died, and your life is hidden with Christ in our Father. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu tsopano wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
4 When Christ, who is your life, appears, then you also will appear with him in glory. Khristu, amene ndiye moyo wanu, akadzaonekanso, pamenepo inunso mudzaoneka naye pamodzi mu ulemerero.
5 So kill what is earthly in you: sexual sin, impurity, lust, evil desire, and greed—which is idolatry. Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.
6 Because of these things the wrath of our Father is coming on those who disobey him. Chifukwa cha zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa ana osamvera.
7 You too once lived this way—that was your life. Inunso kale munkachita zomwezi, mʼmoyo wanu wakale uja.
8 Now get rid of all these: anger, rage, malice, slander, obscene talk from your mouth. Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa.
9 Do not lie to one another, since you have stripped off the old self with its practices, Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake
10 and put on the new self, being renewed in knowledge after the image of its Creator. ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake.
11 No Greek or Jew here, circumcised or uncircumcised, barbarian, Scythian, slave or free—but Christ is all, in all. Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe ndi wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.
12 So, as our Father's chosen, holy and dearly loved, put on heartfelt compassion, kindness, humility, gentleness, and patience. Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.
13 Put up with one another, forgiving whatever complaints you have against each other. Forgive as the Lord forgave you. Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu.
14 And over all these virtues put on love, which binds them all together in perfect unity. Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
15 Let Christ's peace rule your hearts—you were called to it as one body. Be thankful. Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika.
16 Let the word of Christ dwell in you richly, teaching and correcting each other with all wisdom, singing psalms, hymns, and songs from the Spirit, with gratitude in your hearts to our Father. Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.
17 Whatever you do, in word or deed, do it all in the name of the Lord Jesus, thanking our Father through him. Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
18 Wives, submit yourselves to your husbands, as is fitting in the Lord. Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
19 Husbands, love your wives and do not be harsh with them. Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.
20 Children, obey your parents in everything, for this pleases the Lord. Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.
21 Fathers, don't provoke your children, so they won't lose heart. Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.
22 Slaves, obey your earthly masters in everything—not just while watched, to gain favor, but with a sincere heart, fearing the Lord. Inu antchito, mverani mabwana anu mu zonse, ndipo muzichita zimenezi osati nthawi yokhayo imene akukuonani kuti akukondeni, koma muzichite moona mtima ndi mopereka ulemu kwa Ambuye.
23 Whatever you do, work at it wholeheartedly, as for the Lord, not for people, Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.
24 since you know you will receive the inheritance as reward from the Lord; you serve the Lord Christ. Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira.
25 Anyone who does wrong will be repaid for their wrong, and there is no favoritism. Aliyense amene amachita zolakwa adzalandira malipiro molingana ndi kulakwa kwake, ndipo palibe tsankho.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]