Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Acts 15 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Some men came down from Judea and taught the brothers, "Unless you are circumcised by Moses' custom, you cannot be saved." Anthu ena ochokera ku Yudeya anafika ku Antiokeya ndipo amaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuchita mdulidwe potsata mwambo wa Mose, simungapulumuke.”
2 When Paul and Barnabas had fierce dispute and debate with them, the brothers appointed Paul, Barnabas, and some others of them to go up to the apostles and elders in Jerusalem about this question. Zimenezi zinachititsa Paulo ndi Barnaba kuti atsutsane nawo kwambiri. Kotero Paulo ndi Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi abale ena kuti apite ku Yerusalemu kukaonana ndi atumwi ndi akulu ampingo kukakambirana za nkhaniyi.
3 Sent on by the church, they traveled through Phoenicia and Samaria, recounting the Gentiles' conversion, bringing great joy to all the brothers. Mpingo unawaperekeza, ndipo pamene amadutsa ku Foinike ndi Samariya, iwo anafotokoza momwe a mitundu ina anatembenukira mtima. Nkhani imeneyi inakondweretsa kwambiri abale onse.
4 Arriving in Jerusalem, the church, apostles, and elders welcomed them, and they reported all our Father had done with them. Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.
5 But some believers from the Pharisee party stood up and said, "They must be circumcised and ordered to keep the law of Moses." Kenaka, okhulupirira ena amene kale anali a gulu la Afarisi anayimirira ndipo anati, “Anthu a mitundu ina ayenera kuchita mdulidwe ndi kusunga malamulo a Mose.”
6 Then the apostles and the elders gathered together to look into this matter. Atumwi ndi akulu ampingo anasonkhana kuti akambirane za nkhaniyi.
7 After much debate, Peter stood and said, "Brothers, you know that in the early days our Father chose among you that the Gentiles would hear the gospel message through me and believe. Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira.
8 And our Father, who knows the heart, testified by giving them the Holy Spirit, just as he did to us. Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife.
9 He drew no line between us and them, cleansing their hearts by faith. Iye sanasiyanitse pakati pa ife ndi iwo, pakuti anayeretsa mitima yawo mwachikhulupiriro.
10 So why test our Father by putting a yoke on the disciples' neck that neither our ancestors nor we could bear? Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza?
11 But we believe we will be saved through the grace of the Lord Jesus, just as they will." Osatero! Ife tikukhulupirira kuti tinapulumutsidwa mwachisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, monga iwonso anachitira.”
12 The whole crowd fell silent, listening to Barnabas and Paul describe the signs and wonders our Father did among the Gentiles through them. Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo.
13 After they finished speaking, James answered, "Brothers, listen to me. Iwo atatha kuyankhula, Yakobo anayankhula nati: “Abale, tandimverani.
14 Simeon told how our Father first visited the nations, taking from them a people for his name. Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake.
15 And the words of the prophets agree with this, just as it is written: Mawu a aneneri akuvomereza zimenezi, monga kwalembedwa kuti,
16 "'After this I will return, and I will rebuild the tent of David that has fallen; I will rebuild its ruins, and I will restore it, “ ‘Zitatha izi Ine ndidzabwerera ndipo ndidzamanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzakonzanso malo amene anagumuka, ndi kuyimanganso,
17 that the rest of mankind may seek our Father, even all the Gentiles who are called by my name, says our Father, who makes these things, kuti anthu otsalawo afunefune Ambuye, ndi anthu onse a mitundu ina amene atchedwa ndi dzina langa, akutero Ambuye, amene amachita zinthu zimenezi
18 known from long ago.' zinaululidwa kuyambira kalekale.’
19 So I judge we shouldn't trouble the Gentiles turning to our Father, “Chifukwa chake, ine ndikuweruza kuti tisamavute anthu a mitundu ina amene atembenuka mtima kutsata Mulungu.
20 but write telling them to avoid things polluted by idols, sexual immorality, meat from strangled animals, and blood. Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi.
21 For Moses has been proclaimed in every city for generations, read aloud in synagogues every Sabbath." Pakuti malamulo a Mose akhala akulalikidwa mu mzinda uliwonse, kuyambira kalekale ndipo amawerengedwa mʼMasunagoge tsiku la Sabata.”
22 The apostles, elders, and whole church decided to choose men from among them and send them to Antioch with Paul and Barnabas: Judas called Barsabbas, and Silas, leaders among the brothers. Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale,
23 They sent this letter with them: "The apostles and elders, brothers, to the Gentile brothers in Antioch, Syria, and Cilicia: greetings. kuti akapereke kalata yonena kuti, Kuchokera kwa atumwi ndi akulu ampingo, abale anu, Kwa anthu a mitundu ina okhulupirira a ku Antiokeya, Siriya ndi Kilikiya: Tikupereka moni.
24 Since we have heard that some who went out from us troubled you with words, unsettling your hearts, though we gave them no such instructions, Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani.
25 we unanimously agreed to choose men and send them to you with our beloved Barnabas and Paul. Tsono ife tagwirizana kuti, tisankhe anthu ena ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa Paulo ndi Barnaba,
26 Men who have devoted their lives for the name of our Lord Jesus Christ. anthu amene anapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
27 So we sent Judas and Silas, who will themselves tell you the same things by word of mouth. Nʼchifukwa chake, tikutumiza Yudasi ndi Sila kuti adzachitire umboni ndi mawu a pakamwa pawo za zimene ife talemba.
28 The Holy Spirit and we agreed to place no greater burden on you than these necessities: Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi:
29 Avoid food offered to idols, blood, meat from strangled animals, and sexual immorality. Keep yourselves from these and you will do well. Farewell." Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi. Tsalani bwino.
30 So, sent off, they went down to Antioch, gathered the congregation, and delivered the letter. Anthu aja anatumidwa ndipo anafika ku Antiokeya, kumene anasonkhanitsa mpingo pamodzi napereka kalatayo.
31 And when they read it, they rejoiced at the encouragement. Anthuwo anawerenga kalatayo ndipo abalewo anakondwa chifukwa cha mawu ake achirimbikitso.
32 And Judas and Silas, who were themselves prophets, encouraged and strengthened the brothers with many words. Yudasi ndi Sila amene analinso aneneri, ananena zambiri zowalimbikitsa ndi kuwapatsa mphamvu abalewo.
33 After spending time there, the brothers sent them off in peace to those who sent them. Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abale aja anatsanzikana nawo mwamtendere kuti abwerere kwa amene anawatuma.
34 Not in this edition Koma Sila anasankha kuti akhale komweko.
35 But Paul and Barnabas remained in Antioch, teaching and preaching our Lord's word, with many others too. Koma Paulo ndi Barnaba anatsalira ku Antiokeya kumene iwo pamodzi ndi ena ambiri anaphunzitsa ndi kulalikira Mawu a Ambuye.
36 After some days, Paul told Barnabas, "Let's return and visit the brothers in every city where we announced our Lord's message, and see how they're doing." Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.”
37 Now Barnabas wanted to take with them John who was called Mark. Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo.
38 But Paul thought it best not to bring the one who deserted them in Pamphylia and didn't join them for the work. Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito.
39 Their clash grew so sharp they separated from each other; Barnabas took Mark and sailed to Cyprus, Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro.
40 but Paul chose Silas and set out, entrusted by the brothers to the grace of our Lord. Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka.
41 And he traveled through Syria and Cilicia, strengthening the churches. Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]