Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

2 Timothy 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 So then, my child, draw your strength from the grace that is in Christ Jesus. Tsono iwe, mwana wanga, limbika mʼchisomo chimene chili mwa Khristu Yesu.
2 And what you heard from me in the presence of many witnesses, entrust to faithful people able to teach others too. Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena.
3 Take your share of suffering like a good soldier of Christ Jesus. Umve nane zowawa, monga msilikali wa Khristu Yesu.
4 No soldier on duty gets tangled in civilian affairs—he wants to please the one who enlisted him. Palibe msilikali amene ali pa ntchito amagwiranso ntchito za anthu wamba, iye amafuna kukondweretsa bwana wolamulira.
5 And an athlete is not crowned unless he competes according to the rules. Chimodzimodzinso, munthu amene ali pa mpikisano waliwiro, salandira mphotho ya wopambana pokhapokha atatsiriza monga mwa malamulo a mpikisanowo.
6 The hard-working farmer ought to be the first to receive a share of the crops. Mlimi wolimbika ndi amene amayembekezereka kukhala woyambirira kulandira gawo la zokolola.
7 Think over what I am saying, for the Lord will give you understanding in everything. Lingalira zimene ndikunenazi, pakuti Ambuye adzakuzindikiritsa zonsezi.
8 Remember Jesus Christ, risen from the dead, a descendant of David, as told in my gospel, Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino
9 for which I suffer, chained like a criminal. But the word of our Father is not chained! umene ndikuwuvutikira choterewu mpaka kumangidwa ndi maunyolo ngati wakuba. Koma mawu a Mulungu sanamangidwe ndi maunyolo.
10 So I endure everything for the sake of the chosen, so they too may gain the salvation in Christ Jesus, with eternal glory. Choncho ndikupirira chilichonse chifukwa cha osankhidwa, kuti nawonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu ndi kulandira ulemerero wosatha.
11 This saying is trustworthy: If we have died with him, we will also live with him; Mawu oyenera kuwadalira ndi awa: Ngati ife tinafa naye pamodzi, tidzakhalanso moyo pamodzi naye.
12 if we endure, we will also reign with him; if we disown him, he also will disown us; Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.
13 if we are faithless, he remains faithful, for he cannot disown himself. Ngati ndife osakhulupirika, Iye adzakhalabe wokhulupirika popeza sangathe kudzikana.
14 Remind them of these things, and warn them before our Father not to quarrel over words—useless, and ruins those who listen. Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo.
15 Do your best to present yourself to our Father approved, a worker unashamed, rightly handling the word of truth. Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.
16 But avoid empty, godless chatter; it leads people further into wickedness, Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera.
17 and their talk will spread like gangrene. Among them are Hymenaeus and Philetus, Chiphunzitso chawo chidzafalikira ngati chilonda. Mwa anthuwa muli Humenayo ndi Fileto.
18 who wandered away from the truth, claiming the resurrection already happened, and are undermining some people's faith. Iwowa apatuka pa choonadi. Iwo amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kunachitika kale, motero amawononga chikhulupiriro cha anthu ena.
19 Yet our Father's firm foundation stands, sealed: "He knows those who are his," and "Let all who name his name turn from evil." Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.”
20 In a large house there are vessels not only of gold and silver, but also of wood and clay—some for honor, some for dishonor. Mʼnyumba yayikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zina zimakhala za ntchito yapamwamba, zina za ntchito wamba.
21 So if anyone purifies himself from these, he becomes a vessel of honor: holy, useful to the Master, ready for every good work. Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.
22 Flee youthful cravings; pursue righteousness, faith, love, and peace with those who call on the Lord from a pure heart. Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa.
23 Have nothing to do with foolish, ignorant controversies; you know they breed quarrels. Ukane matsutsano oyipa ndi opusa, chifukwa amayambitsa mikangano.
24 The Lord's servant must not be quarrelsome, but be gentle to all, able to teach, patient when wronged. Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa.
25 Gently correcting those who oppose him. Perhaps our Father will grant them repentance to know the truth, Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi.
26 and they may sober up, escaping the devil's trap where he has held them captive to do his will. Motero nzeru zawo zidzabweramo, ndipo adzathawa msampha wa mdierekezi, amene anawagwira ukapolo kuti azichita zofuna zake.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]