Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

2 Timothy 2 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Asikali wokhulupilika wa Yesu Kilisito

1Chipano mwana wanga Timoseo, yendekela kukhala ni mbhavu kupitila ubwino uwo taupata pakumkhulupilila Kilisito Yesu. 2Pita niyajha waya vela niniyaluza pamaso pa wandhu ambili. Wapache wandhu wokhulupilika yawo sakhoze kwaayaluza wandhu wina.

3Limba mtima pa mavuto yako ngati asikali wokhulupilika wa Kilisito Yesu. 4Palibe asikali wabwino uyo wasiya kuchita njhito za uasikali, ni kuchita njhito izo osati za asikali. Wachita chimwecho ndande iye wafuna kumkondwelecha wamkulu wake. 5Nchichijha, uyo wathamanga liwilo siwakhoza kulandila mbhaso yake ya kukhoza, ngati siwathamanga kwa kuchata thauko la liwilo. 6Mlimi uyo wachita njhito kwa mbhavu, wafunika kukhala oyamba kupata gawo lake la vokolola. 7Ughanizile kupunda yayo nikukambila, pakuti Ambuye siakupache kuvijhiwa vindhu vimenevoo vonjhe.

8Mkumbukile kupunda nghani za Yesu Kilisito uyo wadahyukichidwa, uyo wadachokela kufuko la Daudi, ni umenewo nde Uthenga Wabwino uwo niilalikila, 9ndande ya kwauuzila wandhu Uthenga umenewo ine nivutika mbaka kunimanga maunyolo ngati mbala. Nambho Uthenga wa Mnungu siumangidwa. 10Chimwecho niyalimbila yonjhe mtima ndande ya yawo asanghidwa ni Mnungu, kuti nawonjho apate kulamichidwa kupitila Kilisito Yesu, pamojihi ni ukulu wa muyaya. 11Uwu ni uthenga wokhulupilika,“Ikakhala tafa pamojhi ni Kilisito,nafe sitikhale amoyo pamojhi ni iye.

12Ngati tiyendekela kulimba mtima,sitikhozenjho kulalamulila pamojhi ni iye.Ngati sitimkane iye, nayonjho siwatikane ife.

13Ngati ife sitikhulupilika kwa iye,iye siwayendekele kukhala wokhulupilika,pakuti iye siwangakhoze kujhikana mwene wake.”

Wochita njhito uyo wavomelezedwa ni Mnungu

14Uyendekele kwakambila wandhu vindhu ivi, ni kwauzila pamaso pa Mnungu kuti asiye kuyambana ndande ya mawu yayo yalibe mate, pakuti yangowawananga wandhu wajha ayavela. 15Jitaidi kujhilangiza kuti wavomelezeka ni Mnungu ngati mundhu ochita njhito uyo walibe njhoni pauchita njhito yake, uyo wakhoza kuyaluza kwa ubwino uthenga wa Mnungu. 16Ukhale patali ni michuchano yopande mate, yayo yapeleka wandhu kutali ni Mnungu. 17Mayaluzo yameneyo yaenela ngati chilonda chosapole. Wandhu achamewo nde yawo ayaluza mayaluzo yameneyo ni Hemanayo ni Fileto. 18Achamenewo ausiya uzene pa kukamba kuti kuhyuka kwa wandhu kwathochitika. Pakuyaluza chimwecho, apundula chikhulupi cha wandhu wina. 19Nambho msingi wa Mnungu uwo uli nganganga watho ima. Pamwamba pa msingi umenewo yalembedwa mawu kuti, “Ambuye Mnungu wajhiwa wandhu wake,” chimwecho, “Mundhu waliyonjhe uyo wakamba kuti iye ni wa Mnungu, ifunika wasiye kuchita voipa.”

20Mkati mwa nyumba yaikulu muli vindhu va mitundu yosiyanasiyana, vilimo va zahabu ni madini ya feza, muli vindhu va dothi ni vamitengo. Vina vichita njhito ya ulemu ni vina vichita njhito ya kawida. 21Chipano ngati mundhu wajhiyelecha pakusiya kuchita vindhu voipa, siwakhale chombo cho chapatulidwa, icho sichichitilidwe njhito ni Ambuye wake ni wafunika kwa kila njhito iliyonjhe iyo yabwino. 22Leka kuchita vindhu voipa va unyamata, siku zonjhe chata vindhu vivomeleka ni Mnungu ni kukhulupilila ni chikondi ni mtendele pamojhi ni wandhu wonjhe yawo waapembha Ambuye kwa mtima wabwino. 23Nambho leka kuchita michuchano yopusa ni yayo yalibe mate, pakuti ujhiwa kuti yameneyo yayambicha ndewo. 24Chimchijha mtumiki wa Mnungu siwafunika kukhala wandewo, wafunika kukhala wabwino kwa kila mundhu, uyo wakhoza kuyaluza, ni wolimba mtima. 25Ifunika wakhale wojhichicha yapo waaonya wandhu yawo achuchana naye, kwa kukhulupilila kuti Mnungu siwaachite alape ni kuujhiwa uzene, 26kuti njelu zao zaabwelelenjho, nawo saapulumuke mumsambha wa Satana. Iye waakodwecha nikwachita achite ivo wavifuna iye.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]