Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 These were the sons of Israel: Reuben, Simeon, Levi, Judah, Issachar, and Zebulun, Ana a Israeli anali awa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni,
2 Dan, Joseph, Benjamin, Naphtali, Gad, and Asher. Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri.
3 Judah's sons: Er, Onan, Shelah—three born to him by Shua's Canaanite daughter. Er, the firstborn, was evil in our Father's eyes, so he killed him. Ana a Yuda anali awa: Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha.
4 Tamar, Judah's daughter-in-law, bore him Perez and Zerah. Judah had five sons in all. Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.
5 The sons of Perez: Hezron and Hamul. Ana a Perezi anali awa: Hezironi ndi Hamuli.
6 The sons of Zerah: Zimri, Ethan, Heman, Calcol, and Dara—five of them in all. Ana a Zera anali awa: Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu.
7 Carmi's son: Achar, Israel's troubler, who broke faith over the devoted things. Mwana wa Karimi anali Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.
8 The son of Ethan: Azariah. Mwana wa Etani anali Azariya.
9 The sons born to Hezron: Jerahmeel, Ram, and Chelubai. Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali: Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai.
10 Ram fathered Amminadab, and Amminadab fathered Nahshon, leader of the people of Judah. Ramu anabereka Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda.
11 Nahshon fathered Salma, and Salma fathered Boaz, Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi,
12 Boaz fathered Obed, and Obed fathered Jesse. Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese.
13 Jesse fathered Eliab his firstborn, Abinadab the second, Shimea the third, Yese anabereka Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea,
14 Nethanel the fourth, Raddai the fifth, wachinayi Netaneli, wachisanu Radai,
15 Ozem the sixth, and David the seventh. wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide.
16 Their sisters were Zeruiah and Abigail. Zeruiah's sons: Abishai, Joab, and Asahel—three. Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli.
17 Abigail bore Amasa, and the father of Amasa was Jether the Ishmaelite. Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli.
18 Caleb son of Hezron had children by his wife Azubah and by Jerioth; her sons were Jesher, Shobab, and Ardon. Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni.
19 When Azubah died, Caleb married Ephrath, and she bore him Hur. Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri.
20 Hur fathered Uri, and Uri fathered Bezalel. Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli.
21 Afterward Hezron had relations with the daughter of Machir the father of Gilead, marrying her at sixty; she bore him Segub. Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu.
22 Segub fathered Jair, who held twenty-three towns in the land of Gilead. Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi.
23 But Geshur and Aram took Havvoth-jair from them, plus Kenath and its villages—sixty towns. All these were sons of Machir, father of Gilead. (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.
24 After Hezron died in Caleb-ephrathah, Abijah, Hezron's wife, bore him Ashhur, the father of Tekoa. Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa.
25 The sons of Jerahmeel, Hezron's firstborn: Ram his firstborn, then Bunah, Oren, Ozem, and Ahijah. Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali: Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya.
26 Jerahmeel had another wife, whose name was Atarah; she was the mother of Onam. Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu.
27 The sons of Ram, Jerahmeel's firstborn: Maaz, Jamin, and Eker. Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa: Maazi, Yamini ndi Ekeri.
28 The sons of Onam: Shammai and Jada. The sons of Shammai: Nadab and Abishur. Ana a Onamu anali awa: Shamai ndi Yada. Ana a Shamai anali awa: Nadabu ndi Abisuri.
29 Abishur's wife was named Abihail, and she bore him Ahban and Molid. Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi.
30 The sons of Nadab: Seled and Appaim. Seled died without children. Ana a Nadabu anali awa: Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31 The son of Appaim: Ishi. The son of Ishi: Sheshan. The child of Sheshan: Ahlai. Ana a Apaimu anali awa: Isi, amene anabereka Sesani. Sesani anabereka Ahilai.
32 The sons of Jada, Shammai's brother: Jether and Jonathan. Jether died without children. Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa: Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana.
33 The sons of Jonathan: Peleth and Zaza. These were the descendants of Jerahmeel. Ana a Yonatani anali awa: Peleti ndi Zaza. Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli.
34 Now Sheshan had no sons, only daughters. He had an Egyptian servant whose name was Jarha, Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha. Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha.
35 and Sheshan gave his daughter in marriage to Jarha his servant, and she bore him Attai. Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi.
36 Attai fathered Nathan, and Nathan fathered Zabad, Atayi anali abambo ake a Natani, Natani anali abambo ake a Zabadi,
37 Zabad fathered Ephlal, and Ephlal fathered Obed, Zabadi anali abambo a Efilali, Efilali anali abambo a Obedi,
38 Obed fathered Jehu, and Jehu fathered Azariah, Obedi anali abambo a Yehu, Yehu anali abambo a Azariya,
39 Azariah fathered Helez, and Helez fathered Eleasah, Azariya anali abambo a Helezi, Helezi anali abambo a Eleasa,
40 Eleasah fathered Sismai, and Sismai fathered Shallum, Eleasa anali abambo ake a Sisimai, Sisimai anali abambo a Salumu,
41 Shallum fathered Jekamiah, and Jekamiah fathered Elishama. Salumu anali abambo a Yekamiya, Yekamiya anali abambo a Elisama.
42 Sons of Caleb, Jerahmeel's brother: Mesha his firstborn, father of Ziph; and the sons of Mareshah the father of Hebron. Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa: Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni.
43 The sons of Hebron: Korah, Tappuah, Rekem, and Shema. Ana a Hebroni anali awa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema.
44 Shema fathered Raham, the father of Jorkeam, and Rekem fathered Shammai. Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai.
45 The son of Shammai was Maon, and Maon was the father of Beth-zur. Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri.
46 Ephah, Caleb's concubine, bore Haran, Moza, and Gazez; and Haran fathered Gazez. Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi.
47 The sons of Jahdai: Regem, Jotham, Geshan, Pelet, Ephah, and Shaaph. Ana a Yahidai anali awa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi.
48 Maacah, Caleb's concubine, bore Sheber and Tirhanah. Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana.
49 She bore Shaaph, father of Madmannah, and Sheva, father of Machbenah and Gibea. Caleb's daughter was Achsah. Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa.
50 These were the descendants of Caleb. The sons of Hur, the firstborn of Ephrathah: Shobal the father of Kiriath-jearim, Izi zinali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa: Sobala abambo a Kiriati Yearimu,
51 Salma the father of Bethlehem, and Hareph the father of Beth-gader. Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera.
52 Shobal the father of Kiriath-jearim had other sons: Haroeh, and half of the Menuhoth. Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi: Harowe, theka la banja la Manahati,
53 Kiriath-jearim's clans: Ithrites, Puthites, Shumathites, Mishraites—from them came the Zorathites and Eshtaolites. ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa.
54 The descendants of Salma: Bethlehem, the Netophathites, Atroth-beth-joab, half of the Manahathites, and the Zorites. Zidzukulu za Salima zinali izi: Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori,
55 The scribe clans living at Jabez: Tirathites, Shimeathites, Sucathites—Kenites who came from Hammath, father of the house of Rechab. ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]