Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Colossians 1 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Ine Poolo mtumwi wa Yesu Kilisito, kwa chikondi cha Mnungu, nilipano ni mbale Timoseo,

2nikulembelani anyiimwe wandhu a Mnungu yawo muli kumujhi wa Kolosayi, achabale wandhu wokhulupilika pakukhala pamojhi ni Kilisito. Mkhale ni chikondi ni mtendele ivo vichokela kwa Atate wathu a Mnungu.

Kupembha ni kuyamika

3Yapo tikupembhelelani, timuyamika Mnungu ndhawi zonjhe, Tate wa Ambuye wathu Kilisito Yesu. 4Pakuti tavela nghani ya chikhulupililo chanu mwa Kilisito Yesu, ni chikondi chanu kwa wandhu wonjhe a Mnungu. 5Kukhulupilila kwanu ni chikondi chanu vili ni msingi muchikhulupi icho mwaikidwa ku mwamba. Mudavela kuyambila kale nghani zimenezo kupitila mumawu ya uzene ya Uthenga. 6Nghani zimenezo zidafika kwanu, zayenele mumayiko yonjhe. Zaang'anamula wandhu ngati umo zidakung'anamulani anyiimwe kuyambiala siku lijha mdavela nghani za ubwino wa Mnungu, nikuujhiwa uzene wake umo uli. 7Mudauvela uzene umenewo kuchokela kwa Epafula, uyo wadali mtumwi wa Ambuye pamojhi ni ife. Iye wampotela njhito Kilisito mokhulupilika ndande yanu ayiimwe. 8Iye watikambila ife nghani za chikondi icho mwachilandila kuchokela kwa Mzimu wa Mnungu.

9Kwa ndande imeneyo, kuyambila siku lijha tidavela nghani zanu, sitidasiye kukupembhelelani kuti Mnungu wakukhozecheni kuchijhiwa chikondi chake, pakukupachani njelu ni kujhiwa konjhe kwa mzimu uwo muufuna. 10Ndiipo simukhoze kukhala ngati umo wafunila Ambuye, ni ndhawi zonjhe simuchite icho wafuna Mnungu, ni kumukondwelecha munjila zonjhe. Njhito zanu zabwino sizibale vindhu vonjhe vabwino ni kukula muchijhiwicho cha Mnungu. 11Tipembhelanjo kuti Mnungu wakulimbicheni kwa kukhoza kwake kwakukulu, dala mukhale wolimba mtima pa vindhu vonjhe ni mitima yolimba ni yosangalala, 12ni kwaayamika Atate ndhawi zonjhe. Ndande yake, iwo akukhozechani anyiimwe kulandila chijha wadaakambila kuti siwapache wandhu wake yawo akhala muufumu wake wa dangalila. 13Pakuti Mnungu watiombola kuchokela kumbhavu za kumdima za Satana, ni watilowecha muufumu wa Mwana wake uyo wamkonda, 14kupitila mwana mmeneyo, Mnungu watiombola ni kutilekelela machimo yathu.

Kilisito ni njhito yake

15Kilisito walingana kupunda ni Mnungu uyo siwaoneka. Iye ni mbadwa woyamba kwa vindhu vonjhe ivo vaumbidwa. 16Pakuti vindhu vonjhe ivo vili kumwamba kwa Mnungu ni ivo vili pajhiko lapanjhi, vidaumbidwa kwa kupitila mbhavu zake. Iye wadaumba vindhu vijha vionekana ni ivo sivionekana. Wadaumba alamuli wonjhe auzimu, ni waakuluakulu, ufumu ni ulamulilo. Mnungu wadampacha ulamulilo Mwanawake kuumba vindhu vonjhe dala Mwanawake walandile ulemu. 17Mwana wadalipo kuyambila yapo vindhu vonjhe vidali vikali osaumbidwa, ni iye ndeuyo wavichita vindhu vonjhe kuyendekela kukhala pamalo pake. 18Iye nde mchogoleli wamkhulu wa gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito. Iye nde chiyambo cha umoyo wachipano kwa wandhu wake, iye ndechiyambo cha wandhu wohyuka, dala kuti iye wakhale wamkulu pavindhu vonjhe. 19Pakuti ata ngati Kilisito wadali mundhu, Mnungu idamkwadilicha kuti kukwanila kwake kukhale mkati mwa mwana. 20Mnungu Tate wathu wavichita vindhu vonjhe kukhala mabwenji ni iye mwenewake kupitila mwazi wa Mwanawake uwo umamwazika yapo wadamwalila pamtanda.

21Kale yapo mudali mukali osamukhulupilila Kilisito, anyiimwe mudapatuchidwa patali ni Mnungu, ni mudali adani mmaganizo yanu ni vichito vanu voipa. 22Nambho chipano Mnungu wakuchitani kukhala achabwenji wake ndande ya kumwalila kwa Kilisito pamtanda, dala wakupelekeni kwake muli woyela, wopande mawanga kapina cholakwa chilichonjhe. 23Nambho ifunika muyendekele kukhulupilila uthenga wa uzene wa Mnungu uwo mudauvela. Musadalola kutingizidwa ni kusiya chikhulupi icho mudapata yapo mudavela uthenga. Ine poolo nakhala mtumiki wa Uthenga Wabwino uwo mudathouvela.

Njhito ya Poolo kwa wandhu yawo amkhulupilila Kilisito

24Chipano nili wokondwa yapo nivutika ndande ya anyiimwe kuti mupate phindu. Pali vindhu vambili ivo vichita kuti Kilisito wayendekele kuvutika. Nanenjho niyalandila mavuto yameneyo mokondwa mthupi langa ndande ya thupi la Kilisito, ilo lili gulu la wandhu yawo amkhulupilila iye. 25Ine nakhala mtumiki wa wandhu yawo amkhulupilila Kilisito kwa lamulo ilo Mnungu wadanipacha kuti nipeleke mawu la Mnungu mokwanila. 26Mawu ili lidabisidwa kwa mibadwa yonjhe yoyamba, nambho chipano wayalangiza kwa wandhu wake woyela mitima. 27Mnungu wadafuna kwaajhiwicha wandhu wake ubwino wa mpango umenewo wodabwicha. Mpango umenewo ni wa Kilisito kukhala mkati mwathu, nikuti iye ndeuyo watipacha chikhulupililo kuti sitigwilizane ni ulemelelo wa Mnungu. 28Ndendande timukambila kila mmojhi nghani za uthenga wa Kilisito. Timuonya kila mundhu kuti wamchate Kilisito, ni kumuyaluza kila mundhu kwa njelu zonjhe. Pakuti tifuna kumng'anamucha kila mmojhi ni kumpeleka kwa Kilisito wali wokhwima. 29Kwa ndande imeneyo, nichita njhito molimbika ni mwambhavu zonjhe izo iye wadaziika mkati mwanga.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]