Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Romans 9 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 I speak truth in Christ, not lying—my conscience testifies with me in the Holy Spirit, Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni.
2 that I have great sorrow and unceasing anguish in my heart. Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga.
3 I could wish myself cursed, cut off from Christ, for my brothers and sisters, my own people by blood. Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga,
4 They are Israelites: theirs the full rights as sons, the glory, the covenants, the lawgiving, the worship, the promises. anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake.
5 The ancestors are theirs; from them, by human descent, comes the Christ, who is God over all, blessed forever. Amen. Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.
6 This doesn't mean our Father's word has failed, for not all descended from Israel are Israel. Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli.
7 Not all Abraham's offspring are his children; rather, "Your offspring will be named through Isaac." Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.
8 That is, the children of the flesh are not children of our Father, but children of the promise count as offspring. Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu.
9 For the promise says: "At this time next year I will come, and Sarah will have a son." Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
10 Not only that, but Rebekah too conceived by one man, our father Isaac, Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake.
11 though not yet born, having done nothing good or bad—so our Father's purpose by election might stand, Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire,
12 not from works, but from him who calls, she was told: "the older will serve the younger." osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.”
13 As it is written, "Jacob I loved, but Esau I hated." Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”
14 What should we say then? Is there injustice with our Father? By no means! Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe!
15 For he tells Moses, "I will have mercy on whom I have mercy, and I will have compassion on whom I have compassion." Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti, “Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo, ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”
16 So then it depends not on human will or exertion, but on our Father, who has mercy. Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu.
17 For the Scripture says to Pharaoh: "I raised you up for this very reason, to show my power in you, and to have my name proclaimed in all the earth." Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.”
18 So then he has mercy on whomever he wills, and he hardens whomever he wills. Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.
19 So you'll ask me, "Why does he still find fault? Who resists his will?" Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?”
20 But who are you, mere human, to argue with our Father? Does the molded say to its molder, "Why did you make me like this?" Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ”
21 Does the potter not have authority over the clay, making from one lump a vessel for honor, another for dishonor? Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?
22 What if our Father, wanting to show his wrath and make known his power, patiently endured vessels of wrath prepared for destruction, Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko.
23 to reveal his glory's riches for vessels of mercy he prepared beforehand for glory, Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake
24 even us whom he has called, not from the Jews only but also from the Gentiles? ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina.
25 As he says in Hosea, "I will call those not my children, my children, and her not beloved, beloved." Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”
26 "And in the very place where it was said to them, 'You are not my people,' there they will be called 'children of the living Father.'" ndipo, “Pamalo omwewo pamene ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ ”
27 Isaiah cries out about Israel: "Though Israel's children number like sand of the sea, only a remnant will be saved, Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti, “Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiye adzapulumuke.
28 for our Father will carry out his sentence upon the earth, fully and without delay." Pakuti Ambuye adzagamula milandu ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”
29 And as Isaiah predicted: "Had the Father of heaven's armies not left us offspring, we'd have become like Sodom, made like Gomorrah." Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti, “Ngati Yehova Wamphamvuzonse akanapanda kutisiyira zidzukulu, ife tikanawonongeka ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”
30 What then should we say? Gentiles not pursuing righteousness attained righteousness, righteousness by faith; Kodi nanga tidzati chiyani? Tidzati a mitundu ina amene sanafune chilungamo analandira chilungamo chachikhulupiriro
31 but that Israel, who pursued a law of righteousness, did not reach that law. koma Aisraeli, amene anafuna chilungamo cha lamulo sanachilandire.
32 Why? Because they pursued it not through faith but as though through works. They stumbled on the stumbling stone, Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.”
33 as it is written, "See, I am placing in Zion a stumbling stone, a rock that offends; whoever trusts him won't be put to shame." Monga momwe kwalembedwa kuti, “Taonani, Ine ndikuyika mwala mu Ziyoni wopunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Koma amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]