Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Romans 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 What advantage, then, does the Jew have? Or what is the value of circumcision? Nanga kodi pali ubwino wotani pokhala Myuda, kapena muli ubwino wanjinso mu mdulidwe?
2 Much in every way. First of all, they were entrusted with the very words of our Father. Ubwino wake ndi wambiri mʼnjira zonse! Choyambirira iwo anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti awasunge.
3 What then? If some were unfaithful, will their unfaithfulness nullify the faithfulness of our Father? Nanga zili bwanji ngati ena analibe chikhulupiriro? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawo kukanalepheretsa kukhulupirika kwa Mulungu?
4 No! Let our Father be true, though every person is a liar. As it is written: "You are proven right in your words, and win when judged." Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti, “Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi kupambana pamene muweruza.”
5 But if our wrongdoing highlights our Father's righteousness, what do we say? Is our Father unjust to bring wrath on us? (I speak in human terms.). Koma ngati kuyipa mtima kwathu kuonetsa poyera kuti Mulungu ndi wolungama, ife tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ndi wosalungama pamene aonetsa mkwiyo wake pa ife? (Ine ndikuyankhula monga mmene anthu ena amayankhulira).
6 Certainly not! For then how could our Father judge the world? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ngati zikanakhala zotero, kodi Mulungu akanaweruza bwanji dziko lapansi?
7 But if my lie makes our Father's truth overflow to his glory, why am I still judged as a sinner? Wina atanena kuti, “Ngati kunama kwanga kukuonetsa koposa kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemerero wake, nanga nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa kuti ndine wochimwa?”
8 Why not say, as some slander us as saying, "Let's do evil so good may come"? Their judgment is deserved. Nʼchifukwa chiyani osanena kuti, monga ena amanena mosasamala kuti, “Tiyeni tichite zoyipa kuti zabwino zionekere?” Anthu onena zoterewa kulangidwa kwawo ndi koyenera.
9 What then? Are we better off? Not at all—we've already charged that Jews and Greeks alike are all under sin's grip, Kodi timalize bwanji? Kodi Ayuda ndife oposa anthu ena? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ife tinanena kale kuti Ayuda ndi a mitundu ina omwe ndi ochimwa.
10 as it is written: "There is no one righteous, not even one; Monga kwalembedwa kuti, “Palibe munthu wolungama, inde palibe ndi mmodzi yemwe.
11 no one understands; no one seeks our Father. Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira, palibe amene amafunafuna Mulungu.
12 All have turned away; together they have become worthless; no one does good, not even one. Onse apatukira kumbali, onse pamodzi asanduka opandapake. Palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita zabwino, palibe ngakhale mmodzi.”
13 Their throat is an open grave; they use their tongues to deceive." "The venom of snakes is under their lips. “Kummero kwawo kuli ngati manda apululu; ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.” “Ululu wa mamba uli pa milomo yawo.”
14 Their mouth is full of cursing and bitterness. “Mʼkamwa mwawo ndi modzaza ndi zotemberera ndi mawu owawa.”
15 Their feet are swift to shed blood; “Mapazi awo afulumira kukakhetsa magazi.
16 ruin and misery mark their ways, Kusakaza ndi chisoni kumaonekera mʼnjira zawo,
17 and the way of peace they have not known. ndipo njira ya mtendere sayidziwa.”
18 There is no fear of our Father before their eyes." “Saopa Mulungu ndi pangʼono pomwe.”
19 We know whatever the law says applies to those under it, so every mouth is silenced and the whole world stands accountable to our Father. Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu.
20 No one is made right before him by works of the law; the law brings awareness of sin. Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo.
21 But now, apart from the law, our Father's righteousness has been revealed, testified to by the Law and the Prophets. Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni.
22 This righteousness of our Father comes through faith in Jesus Christ, to all who believe, for there's no distinction, Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina,
23 since all have sinned and fall short of the glory of our Father, pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu
24 and are justified freely by his grace through the redemption that is in Christ Jesus. ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.
25 Our Father presented him as the atoning sacrifice, through faith in his blood, to show his righteousness, since in his patience he had passed over sins committed before, Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale.
26 to show his righteousness now, so he is both just and the justifier of whoever trusts in Jesus. Iye anachita izi kuti aonetse chilungamo chake lero lino. Anthu azindikire kuti Iye ndi wolungama ndipo amalungamitsa aliyense amene akhulupirira Yesu.
27 Where then is boasting? Excluded. By what law? Of works? No—by the law of faith. Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Kunyadatu kwachotsedwa. Chifukwa cha Malamulo? Kodi Malamulo samafuna ntchito za munthu? Ayi, koma mwachikhulupiriro.
28 For we maintain that a person is justified by faith apart from works of the law. Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo.
29 Or is our Father the Father of Jews only? Not the Father of Gentiles too? Yes, of Gentiles too, Kodi Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si Mulungu wa a mitundu inanso? Inde wa a mitundu inanso,
30 since our Father is one, he will justify the circumcised by faith and the uncircumcised through faith. popeza ndi Mulungu mmodzi yemweyo amene adzalungamitsa mwachikhulupiriro ochita mdulidwe ndi osachita mdulidwe kudzera mʼchikhulupiriro chomwecho.
31 Do we cancel the law through this faith? Never—we confirm the law. Kodi tsono ife, tikutaya Malamulo pamene tikunena kuti pafunika chikhulupiriro? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Komatu ife tikukwaniritsadi Malamulo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]