Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Romans 11 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 So I ask: has our Father rejected his people? Never—I too am an Israelite, from Abraham's line, tribe of Benjamin. Ine ndikufunsa kuti kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Inenso ndine Mwisraeli, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini.
2 Our Father didn't reject his people, whom he foreknew. Or don't you know what Scripture says of Elijah, how he pleads with our Father against Israel? Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati,
3 "Father, they killed your prophets, tore down your altars; I alone remain, and they seek my life." “Ambuye, anthuwa apha aneneri anu ndi kugwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha wamoyo ndipo akufuna kundipha?”
4 God's reply: "I've kept 7,000 men for myself who haven't bowed the knee to Baal." Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.”
5 So too at the present time there is a remnant, chosen by grace. Chimodzimodzinso lero lino, alipo Aisraeli pangʼono osankhidwa mwachisomo.
6 But if by grace, no longer by works; otherwise grace would no longer be grace. Ndipo ngati ndi mwachisomo, sikungakhalenso mwa ntchito. Ngati zikanatero, chisomo sichikanakhalanso chisomo ayi.
7 What then? Israel didn't get what it sought; the chosen did, but the rest were hardened. Nʼchiyani tsopano? Chimene Aisraeli anachifuna ndi mtima wonse sanachipeze koma osankhidwawo anachipeza. Enawo anawumitsidwa mtima
8 As it is written: "Our Father gave them a dulled spirit, eyes that can't see and ears that can't hear, to this day." monga kwalembedwa kuti, “Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu, maso osatha kupenya; makutu osatha kumva mpaka lero lino.”
9 And David says, "Let their table become a snare, a trap, a stumbling block, and payback for them. Ndipo Davide akuti, “Maphwando awo asanduke msampha ndi diwa lowakola ndi chopunthwitsa kuti alandire chilango.
10 Let their eyes be darkened so that they cannot see, and bend their backs forever." Maso awo atsekedwe kuti asaone, ndi misana yawo ikhale yokhota nthawi zonse.”
11 So I ask: did they stumble to fall completely? By no means! Rather, their failure brought salvation to the Gentiles, to make Israel jealous. Ine ndikufunsanso kuti, kodi iwo anapunthwa ndi kugwa kotheratu? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo, chipulumutso chinafika kwa a mitundu ina kuti Aisraeli achite nsanje.
12 If their sin enriches the world, and their failure enriches the Gentiles, how much more their full inclusion! Koma ngati kulakwa kwawo kwapindulitsa dziko lapansi ndi kulephera kwawo kwapindulitsa a mitundu ina, nanga kudzakhala kupindula kwakukulu chotani iwo akadzabwera chonse!
13 I say this to you Gentiles: since I am apostle to the Gentiles, I honor my ministry, Ine ndikuyankhula kwa inu a mitundu ina monga ine ndili mtumwi wa kwa a mitundu ina ndipo ndimawunyadira utumiki wangawu.
14 in the hope that I may somehow make my own people jealous and save some of them. Ine cholinga changa nʼchakuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga kuti ena mwa iwo apulumutsidwe.
15 If their rejection reconciled the world, what will their acceptance bring but life from the dead? Pakuti ngati kukanidwa kwawo kunayanjanitsa anthu a dziko lapansi ndi Mulungu, nanga kudzatani, Iye akadzawalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka.
16 If the firstfruit is holy, so is the batch; if the root is holy, so are the branches. Ngati chigawo chimodzi cha buledi woperekedwa monga zipatso zoyamba ndi choyera, ndiye kuti zonsezo ndi zoyera. Ngati muzu ndi oyera, nʼchimodzimodzinso nthambi zake.
17 If some branches were broken off, and you, a wild olive shoot, were grafted in among them, sharing the olive tree's rich root, Ngati nthambi zina zinakhadzulidwa ndipo inu, inu ndiye nthambi za olivi wakuthengo, nʼkulumikizidwa pamalo pa nthambi zimenezo, ndipo tsopano mukulandira nawo zakudya zochokera ku mizu ya olivi,
18 don't boast over the branches. If you do, you don't support the root—the root supports you. musadzitame kunyoza nthambi zinazo. Ngati mutero, ganizirani ichi kuti Inu simugwiriziza mizu, koma muzu ukugwiriziza inu.
19 Then you will say, "Branches were broken off so that I might be grafted in." Tsono mudzati, “Nthambizo zinakhadzulidwa kuti ine ndilumikizidwepo.”
20 True. They were broken off for lack of faith; you stand by faith. Don't be proud—fear instead. Nʼzoona. Koma iwo anakhadzulidwa chifukwa chosakhulupirira ndipo inu mukuyima mwachikhulupiriro. Musadzitukumule, koma muchite mantha.
21 For if our Father did not spare the natural branches, neither will he spare you. Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachibadwidwe, Iye sadzakulekererani inunso.
22 So see our Father's kindness and severity: severity to the fallen, kindness to you—if you continue in it; otherwise you too will be cut off. Nʼchifukwa chake ganizirani za kukoma mtima ndi za ukali wa Mulungu. Ukali uli kwa iwo amene anagwa koma kukoma mtima kwa inu, malinga ngati musamala kukoma mtima kwakeko kupanda kutero inunso mudzakhadzulidwanso.
23 And if they don't remain in lack of faith, they too will be grafted in—our Father can graft them in again. Ngati iwo asiya kukhala osakhulupirira, adzalumikizidwanso pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso.
24 If you were cut from an olive wild by nature and grafted, against nature, into a cultivated one, how much more will natural branches be grafted back into their own olive tree? Pakuti ngati inu, mwa chilengedwe munali mtengo wa olivi wa kuthengo, Mulungu anakukhadzulani nakulumikizani ku mtengo wa olivi wodzalidwa, zomwe ndi zotsutsana ndi chilengedwe, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuwalumikizanso mu mtengo wawowawo wa olivi?
25 Brothers and sisters, I don't want you unaware of this mystery, so you aren't wise in your own eyes: Israel is partly hardened, until the full number of Gentiles comes in. Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa za chinsinsi ichi, kuti mungadziyese nokha anzeru. Kuwuma mtima kumene Aisraeli akuchita ndi kwa kanthawi kufikira chiwerengero cha a mitundu chitalowa.
26 So all Israel will be saved, as it is written: "The rescuer will come from Zion and remove evil from Jacob, Kotero tsono Aisraeli onse adzapulumuka, monga kwalembedwa kuti, “Mpulumutsi adzachokera ku Ziyoni; Iye adzachotsa zoyipa zonse za Yakobo.
27 and this will be my covenant with them, when I take away their sins." Ndipo ili lidzakhala pangano langa ndi iwo pamene Ine ndidzachotsa machimo awo.”
28 In the gospel, they are enemies for your sake; in election, beloved because of the fathers. Chifukwa cha Uthenga Wabwino, Aisraeli asanduka adani a Mulungu kuti inu mupindule. Koma kunena za kusankhidwa, iwo ndi okondedwa ndi Mulungu chifukwa cha makolo awo aja.
29 For the gifts and the calling of our Father are irrevocable. Pakuti Mulungu akayitana munthu ndi kumupatsa mphatso sangasinthenso.
30 For just as you once disobeyed our Father, but now have received mercy through their disobedience, Monga mmene inu munalili, osamvera Mulungu pa nthawi ina, tsopano mwalandira chifundo chifukwa cha kusamvera kwawo.
31 so they too now disobeyed, so that by the mercy shown you, they too may now receive mercy. Chonchonso iwo akhala osamvera tsopano kuti iwonso alandire chifundo chifukwa cha chifundo cha Mulungu kwa inu.
32 For our Father has bound everyone over to disobedience, that he may have mercy on all. Pakuti Mulungu anasandutsa anthu onse a mʼndende ya kusamvera kuti Iye akaonetse chifundo kwa onse.
33 Oh, the depth of the riches and the wisdom and the knowledge of our Father! How unsearchable are his judgments and how untraceable his ways! Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri! Ndani angazindikire maweruzidwe ake, ndipo njira zake angazitulukire ndani?
34 "For who has known the mind of our Father, or who has been his counselor? “Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye? Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?”
35 Or who has given a gift to him that he might be repaid?" “Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezere iye?”
36 For from him and through him and to him are all things. To him be the glory forever. Amen. Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]