Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Numbers 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Our Father spoke to Moses, saying: Yehova anawuza Mose kuti,
2 "Make yourself two silver trumpets, hammered work; use them to call the community and to move the camps. “Sula malipenga awiri a siliva, ndipo uziwagwiritsa ntchito posonkhanitsa anthu pamodzi ndiponso powasamutsa mʼmisasa.
3 When both sound, the whole community must gather to you at the entrance to the tent of meeting. Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano.
4 But if only one is blown, the leaders—heads of Israel's clans—are to gather to you. Akaliza limodzi lokha, atsogoleri, akulu a mafuko a Aisraeli, asonkhane kwa iwe.
5 When you sound a blast, the camps on the east side are to set out. Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka.
6 Sound a second blast: camps on the south side set out. Sound a blast for their setting out. Akaliza lipenga lochenjeza lachiwiri, misasa yakummwera iyambe kusamuka. Kuliza kwa lipenga lochenjeza kudzakhala chizindikiro choyamba ulendo.
7 But when you call the assembly together, blow a steady note, not an alarm. Pofuna kusonkhanitsa anthu, muziliza malipenga, koma mosiyana ndi mmene malipenga ochenjeza amalizidwira.
8 Aaron's sons, the priests, are to blow the trumpets—a lasting law for you throughout your generations. “Ana a Aaroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipengawo. Zimenezi zikhale zokhazikika kwa inu ndi ku mibado yanu yonse.
9 When you go to war in your land against the enemy crushing you, sound an alarm on the trumpets—you will be remembered before me and saved from your enemies. Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu.
10 Also on your day of joy, at your appointed feasts and new moons, blow the trumpets over your burnt offerings and over your peace offerings—a memorial for you before our Father. I am your Father." Komanso pa nthawi yanu ya chisangalalo, pa maphwando anu oyikika ndi maphwando a mwezi watsopano, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu za chiyanjano, ndipo zidzakhala chikumbutso chanu pamaso pa Mulungu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”
11 In the second year, second month, on the twentieth day, the cloud lifted from over the tabernacle of the testimony. Pa chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la 20, mtambo unachoka pamwamba pa chihema cha umboni.
12 The Israelites set out from the Sinai wilderness, stage by stage; the cloud settled in the Paran wilderness. Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani.
13 This was their first setting out, at our Father's command through Moses. Kameneka kanali koyamba kuti Aisraeli anyamuke monga momwe Yehova analamulira Mose.
14 Judah's camp banner set out first, by their divisions, Nahshon son of Amminadab over his division. Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu.
15 Nethanel son of Zuar was over the division of the tribe of Issachar, Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanieli mwana wa Zuwara,
16 and Eliab son of Helon was over the division of the tribe of Zebulun. Eliabu mwana wa Heloni ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Zebuloni.
17 The tabernacle was taken down, and the sons of Gershon and sons of Merari set out, carrying it. Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka.
18 Reuben's camp standard set out by divisions, Elizur son of Shedeur over its division. Kenaka magulu a msasa wa fuko la Rubeni ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Elizuri mwana wa Sedeuri.
19 Shelumiel son of Zurishaddai was over the division of the tribe of Simeon, Mtsogoleri wa fuko la Simeoni anali Selumieli mwana wa Zurisadai,
20 and Eliasaph son of Deuel was over the division of the tribe of Gad. ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi.
21 The Kohathites set out carrying the holy things, and the tabernacle was set up before they arrived. Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike.
22 Ephraim's camp standard set out by division, Elishama son of Ammihud over its division. Magulu a msasa wa Aefereimu anatsatira potsatira mbendera yawo. Elisama mwana wa Amihudi ndiye anali mtsogoleri wawo.
23 Gamaliel son of Pedahzur was over the division of the tribe of Manasseh, Gamalieli mwana wa Pedazuri ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Manase.
24 and Abidan son of Gideoni was over the division of the tribe of Benjamin. Abidani mwana wa Gideoni ndiye anali mtsogoleri wa mtundu wa Benjamini.
25 Dan's camp standard set out, rear guard of all the camps, by their divisions, with Ahiezer son of Ammishaddai over its division. Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
26 Pagiel son of Ochran was over the division of the tribe of Asher, Pagieli mwana wa Okirani ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Aseri,
27 and Ahira son of Enan was over the division of the tribe of Naphtali. ndipo mtsogoleri wa mtundu wa Nafutali anali Ahira mwana wa Enani.
28 This was the order of march for the Israelites by their divisions as they set out. Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu.
29 Moses said to Hobab son of Reuel the Midianite, his father-in-law, "We are traveling to the place our Father said, 'I will give it to you.' Come with us; we will treat you well, for our Father has promised good to Israel." Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.”
30 But Hobab said to him, "I will not go; I am returning to my own land and my own people." Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.”
31 Moses said, "Please don't leave us, since you know where we should camp in the wilderness, and you'll be our eyes. Ndipo Mose anati, “Pepa usatisiye popeza ukudziwa kumene tingamange misasa mʼchipululu muno ndipo udzakhala maso athu.
32 If you come with us, whatever good our Father does for us, we'll do the same for you." Iweyo ukapita nafe, tidzagawana nawe zinthu zabwino zomwe Yehova adzatipatsa.”
33 They set out from the mountain of our Father on a three-day journey, and the ark of our Father's covenant went ahead of them that three-day journey, seeking a resting place for them. Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo.
34 The cloud of our Father was over them by day as they left the camp. Mtambo wa Yehova unkawaphimba masana pamene ankasamuka pa misasa yawo.
35 Whenever the ark set out, Moses said, "Rise, O Father! Let your enemies be scattered; let those who hate you flee before you." Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti, “Dzukani, Inu Yehova! Adani anu abalalike; Odana nanu athawe pamaso panu.
36 Whenever it rested, he'd say, "Return, O Father, to Israel's countless thousands." “Pamene likupumula, ankanena kuti, “Bwererani, Inu Yehova, ku chinamtindi cha Aisraeli.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]