Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Nehemiah 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Eliashib the high priest and his fellow priests rose and built the Sheep Gate. They dedicated it and set up its doors; they dedicated it up to the Tower of the 100, to the Tower of Hananel. Pambuyo pake Eliyasibu mkulu wa ansembe ndi ansembe anzake anayamba kugwira ntchito ndipo anamanganso Chipata cha Nkhosa. Iwo anachipatulira Mulungu ndipo anayika zitseko zake. Khoma limene analipatula linafika mpaka pa Nsanja ya Zana ndi Nsanja ya Hananeli.
2 Next to them the men of Jericho built, and next to them Zaccur son of Imri built. Anthu a ku Yeriko anamanga chigawo china pambali pake ndipo Zakuri mwana wa Imuri anamanga chigawo chinanso choyandikana nawo.
3 Hassenaah's sons rebuilt the Fish Gate, laid its beams, and set up its doors, bolts, and bars. Chipata cha Nsomba chinamangidwanso ndi ana a fuko la Hasena. Iwo anayika mitanda yake ndi zitseko, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake.
4 Next to them, Meremoth son of Uriah son of Hakkoz repaired. Next to them, Meshullam son of Berechiah son of Meshezabel repaired. Next to them, Zadok son of Baana repaired. Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, anakonza chigawo choyandikana nacho. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabeli anakonza chigawo china. Pambali pake, Zadoki mwana wa Baana anakonzanso chigawo china.
5 Next to them the Tekoites repaired, but their nobles wouldn't put their necks to their masters' work. Pambali pa iwowa anthu a ku Tekowa anakonza chigawo china. Koma wolemekezeka awo anakana kugwira ntchito imene akuluakulu awo anawapatsa.
6 Joiada son of Paseah and Meshullam son of Besodeiah repaired the Old Gate: laid its beams, set its doors, bolts, and bars. Chipata cha Yesana chinakonzedwa ndi Yoyada mwana wa Paseya ndi Mesulamu mwana wa Besodeya. Iwo anayika mitanda yake ndi kuyika zitseko, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake.
7 Next to them, Melatiah the Gibeonite and Jadon the Meronothite—men of Gibeon and Mizpah—repaired the section belonging to the seat of the governor of the province Beyond the River. Pambali pawo Melatiya Mgibeyoni ndi Yadoni Mmerenoti ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa anakonza chigawo chawo mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate.
8 Next to him, Uzziel son of Harhaiah, one of the goldsmiths, made repairs. Next to him, Hananiah, a perfumer, made repairs. They restored Jerusalem as far as the Broad Wall. Pambali pawo Uzieli mwana wa Harihaya wa mʼgulu amisiri osula golide anakonzanso chigawo china. Pambali pake Hananiya mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, anakonzanso chigawo china. Iwo anakonzanso Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka.
9 Next to them Rephaiah son of Hur, ruler of half the district of Jerusalem, made repairs. Refaya mwana wa Huri wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu anakonza chigawo china motsatana nawo.
10 Next to them Jedaiah son of Harumaph repaired opposite his house; next to him, Hattush son of Hashabneiah repaired. Kulumikiza ichi, Yedaya mwana wa Harumafi anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba yake, ndipo Hatusi mwana wa Hasabaneya anakonzanso motsatana naye.
11 Harim's son Malkijah and Pahath-moab's son Hasshub repaired another section and the Tower of the Ovens. Malikiya mwana wa Harimu ndi Hasubu mwana wa Pahati-Mowabu anakonzanso chigawo china ndiponso Nsanja ya Ngʼanjo.
12 Next to him Shallum son of Hallohesh, ruler of half the district of Jerusalem, repaired—he and his daughters. Salumu mwana wa Halohesi wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu, anakonzanso chigawo chotsatana nawo mothandizidwa ndi ana ake akazi.
13 Hanun and Zanoah's people repaired the Valley Gate, rebuilding it, setting up its doors, bolts, and bars, and repairing about 1,500 feet of wall to the Dung Gate. Chipata cha ku chigwa chinakonzedwa ndi Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa. Iwo anachimanganso ndi kuyika zitseko zake ndi zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iwo anakonzanso khoma lotalika mamita 450 mpaka ku Chipata cha Zinyalala.
14 Malkijah son of Rechab, ruler of the Beth-haccherem district, repaired the Dung Gate—rebuilding it and setting its doors, bolts, and bars. Chipata cha Zinyalala chinakonzedwa ndi Malikiya mwana wa Rekabu, wolamulira chigawo cha Beti-Hakeremu. Iye anachimanganso ndi kuyika zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo.
15 Shallun son of Col-hozeh, ruler of the Mizpah district, repaired the Fountain Gate—rebuilding it, roofing it, and setting its doors, bolts, and bars. He also repaired the wall of the Pool of Siloam by the King's Garden, to the stairs going down from the City of David. Chipata cha Kasupe chinakonzedwa ndi Saluni mwana wa Koli-Hoze, wolamulira chigawo cha Mizipa. Iye anachimanganso ndi kuyikanso denga ndiponso zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iye anakonzanso khoma la Dziwe la Siloamu limene lili pafupi ndi munda wa mfumu mpaka ku makwerero otsikira potuluka mzinda wa Davide.
16 After him Nehemiah son of Azbuk, ruler of half the district of Beth-zur, repaired up to the point opposite David's tombs, the built pool, and the House of the Warriors. Pambali pa iyeyo, Nehemiya mwana wa Azibuki, wolamulira theka la chigawo cha Beti Zuri anakonza chigawo china mpaka kumalo oyangʼanana ndi manda a Davide, mpaka ku dziwe lokumba ndi ku nyumba ya anthu ankhondo.
17 After him the Levites repaired: Rehum son of Bani. Next to him, Hashabiah, ruler of half the district of Keilah, repaired for his district. Pambali pake Alevi anakonza chigawo china, ndipo mtsogoleri wawo anali Rehumi mwana wa Bani. Pambali pa iye Hasabiya wolamulira theka la chigawo cha Keyila anagwira ntchito ku chigawo chake.
18 After him their fellow Levites repaired next: Binnui son of Henadad, ruler of half the district of Keilah. Pambuyo pa iyeyu abale awo anapitiriza kukonza, ndipo mtsogoleri wawo anali Bawai mwana wa Henadadi, wolamulira theka lina la chigawo cha Keyila.
19 Beside him, Ezer son of Jeshua, Mizpah's ruler, repaired a second section opposite the armory ascent at the Angle. Motsatana naye Ezeri mwana wa Yesuwa, wolamulira Mizipa anakonza chigawo chinanso choyangʼanana ndi chikweza chofikira ku nyumba yosungira zida za nkhondo pa ngodya.
20 After him Baruch son of Zabbai eagerly repaired another section, from the Angle to the entrance of Eliashib the high priest's house. Motsatana naye, Baruki mwana wa Zakai anakonzanso chigawo china kuchokera pa ngodya mpaka pa chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe.
21 After him Meremoth son of Uriah son of Hakkoz repaired another section, from the entrance to the end of Eliashib's house. Motsatana naye, Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi anakonzanso chigawo china kuchokera ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka kumapeto kwake.
22 After him the priests from the surrounding plain made repairs. Pambuyo pake ansembe okhala ku chidikha anakonzanso chigawo china.
23 Next, Benjamin and Hasshub repaired opposite their house. Next, Azariah son of Maaseiah son of Ananiah repaired beside his own house. Pambuyo pawo, Benjamini ndi Hasubu anakonza kutsogolo kwa nyumba zawo. Ndipo motsatana nawo, Azariya mwana wa Maaseya mwana wa Ananiya, anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba zawo.
24 After him Binnui son of Henadad repaired another section, from Azariah's house to the Angle and corner. Motsatana naye, Binuyi mwana wa Henadadi anakonzanso chigawo china, kuchokera pa nyumba ya Azariya kukafika potsirizira pa ngodya.
25 Palal son of Uzai repaired opposite the Angle and the tower jutting from the king's upper palace, by the guard's court. After him, Pedaiah son of Parosh. Palali mwana Uzai anakonza chigawo china choyangʼanana ndi ngodya ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Motsatana naye, Pedaya mwana wa Parosi,
26 The temple servants living on Ophel repaired up to opposite the Water Gate eastward, and the projecting tower. ndi otumikira mʼNyumba ya Mulungu amene amakhala pa khoma la Ofeli anakonza chigawo china mpaka pa malo oyangʼanana ndi Chipata cha Madzi kuloza kummawa ndiponso nsanja yayitali ija.
27 After them the Tekoites repaired a second section, from opposite the great projecting tower to the wall of Ophel. Motsatana nawo, anthu a ku Tekowa anakonzanso chigawo china choyangʼanana ndi nsanja ija yayikulu ndi yayitali mpaka ku khoma la Ofeli.
28 Above the Horse Gate the priests made repairs, each one opposite his own house. Kuyambira ku Chipata cha Akavalo anakonza ndi ansembe ena ndipo aliyense amakonza khoma loyangʼanana ndi nyumba yake.
29 After him Zadok son of Immer repaired, opposite his house. After him Shemaiah son of Shecaniah, keeper of the East Gate, repaired. Motsatana nawo, Zadoki mwana wa Imeri anakonza chigawo china choyangʼanana ndi nyumba yake. Motsatana naye, Semeya mwana wa Sekaniya, mlonda wa Chipata cha Kummawa, anakonzanso khoma.
30 After him Hananiah son of Shelemiah and Hanun, Zalaph's sixth son, repaired another section. After them Meshullam son of Berechiah repaired opposite his living quarters. Hananiya mwana wa Selemiya ndiponso Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi anakonza chigawo china. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya anakonza chigawo choyangʼanana ndi chipinda chake.
31 After him Malkijah, one of the goldsmiths, repaired as far as the house of the temple servants and traders, opposite the Inspection Gate, and to the upper room at the corner. Motsatana naye, Malikiya mmodzi mwa amisiri a golide anakonza chigawo china mpaka ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda moyangʼanana ndi chipata cha Mifikade ndiponso mpaka pa chipinda chapamwamba chapangodya.
32 Between the upper room at the corner and the Sheep Gate, the goldsmiths and merchants made repairs. Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza ndi amisiri a golide ndi anthu amalonda.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]