Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Matthew 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Seeing the crowds, Jesus went up the mountain; when he sat down, his disciples came to him. Iye ataona anthu ambiri, anakwera pa phiri nakhala pansi. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye,
2 And he opened his mouth and began to teach them, saying: ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuti,
3 "Blessed are the poor in spirit, for theirs is the kingdom of our Father. “Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.
4 Blessed are those who mourn, for they will be comforted. Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa.
5 Blessed are the meek, for they will inherit the earth. Odala ndi amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.
6 Blessed are those who hunger and thirst for righteousness, for they will be satisfied. Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhutitsidwa.
7 Blessed are the merciful, for they will receive mercy. Odala ndi amene ali ndi chifundo, chifukwa adzawachitira chifundo.
8 Blessed are the pure in heart, for they will see our Father. Odala ndi amene ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.
9 Blessed are the peacemakers, for they will be called children of our Father. Ndi odala amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
10 Blessed are those who are persecuted for righteousness' sake, for theirs is the kingdom of our Father. Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”
11 "Blessed are you when people insult, persecute, and lie about every kind of evil against you because of me. “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine.
12 Rejoice and be glad, for your reward is great in heaven, for they persecuted the prophets before you the same way. Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.
13 "You are the salt of the earth. But if salt loses its taste, how can it be salted again? It's no longer good for anything but being thrown out and trampled by people. “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.
14 "You are the light of the world. A city set on a hill cannot be hidden. “Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika.
15 No one lights a lamp and puts it under a basket, but sets it on a stand to light everyone in the house. Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo.
16 Likewise, let your light shine before people, so they see your good works and glorify your Father in heaven. Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.
17 "Don't think I came to abolish the Law or the Prophets—I didn't come to abolish them, but to fulfill them. “Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa.
18 For truly I tell you: until heaven and earth pass, not one letter, not one stroke, will pass from the Law until everything is done. Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa.
19 So whoever breaks one of these least commands and teaches others the same will be called least in the kingdom of our Father; but whoever keeps and teaches them will be called great in the kingdom of our Father. Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba.
20 For I tell you, unless you are more righteous than the scribes and Pharisees, you'll never enter the kingdom of our Father. Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.
21 "You've heard that it was said to those of old, 'Do not murder; whoever murders is subject to judgment.' “Munamva kuti kunanenedwa kwa anthu kale kuti, ‘Usaphe ndipo kuti aliyense amene apha munthu adzaweruzidwa.’
22 But I tell you: whoever is angry with his brother risks judgment. Whoever insults his brother risks the council, and whoever says, 'You fool!' risks fiery hell. Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena.
23 "So if you're offering your gift at the altar and recall there that your brother has something against you, “Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa,
24 leave your gift there before the altar, go make peace with your brother first, then come offer your gift. usiye choperekacho pa guwa lansembepo, choyamba pita kayanjane ndi mʼbale wako; ukatero bwera kudzapereka chopereka chakocho.
25 Make peace with your accuser quickly, while still on the way with him, or he may hand you over to the judge, the judge to the officer, and you may be thrown into prison. “Fulumira kuyanjana ndi mnzako amene unamulakwira nthawi ya milandu isanafike chifukwa angakupereke kwa oweruza amene angakupereke kwa mlonda ndipo mlondayo angakutsekere mʼndende.
26 Truly I tell you, you will never get out until you have paid the last penny. Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti sudzatuluka mʼndende mpaka utalipira zonse.
27 "You have heard that it was said, 'You shall not commit adultery.' “Munamva kuti kunanenedwa kuti, ‘Usachite chigololo.’
28 But I tell you: everyone who looks at a woman lustfully has already committed adultery with her in his heart. Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.
29 If your right eye makes you stumble, tear it out and throw it away—better to lose one part of your body than have your whole body thrown into hell. Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.
30 If your right hand makes you sin, cut it off and throw it away. Better to lose one part of you than have your whole body go into hell. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.
31 "It was also said, 'Whoever divorces his wife must give her a certificate of divorce.' “Ananena kuti, ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenera amupatse kalata ya chisudzulo.’
32 I tell you: whoever divorces his wife, except for sexual sin, makes her a victim of adultery; and whoever marries a divorced woman commits adultery. Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.
33 "Again, you've heard it was said to the ancients: 'Don't break your oath—fulfill it to our Father.' “Munamvanso kuti kunanenedwa kwa anthu akale kuti, ‘Musaphwanye lonjezo; koma sungani malonjezo anu amene mwachita kwa Yehova.’
34 But I tell you, do not swear an oath at all: neither by heaven, for it is our Father's throne, Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu.
35 nor by the earth, for it's the footstool for his feet, nor by Jerusalem, for it's the city of the great King. Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu.
36 And do not swear by your head, for you cannot make a single hair white or black. Ndipo musalumbire ndi mutu wanu chifukwa simungathe kuyeretsa ngakhale kudetsa tsitsi limodzi.
37 Let your 'Yes' be 'Yes,' and your 'No,' 'No'; anything beyond this comes from the evil one. Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.
38 "You have heard that it was said, 'Eye for eye and tooth for tooth.' “Munamva kuti, ‘Diso kulipira diso ndi dzino kulipira dzino.’
39 But I tell you: don't resist an evil person. If someone slaps your right cheek, turn the other cheek to him too. Koma ndikuwuzani kuti musamukanize munthu woyipa, akakumenya patsaya mupatseni tsaya linalo.
40 If anyone wants to sue you and take your tunic, let him have your cloak too. Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako.
41 And if anyone forces you to go one mile, go with him two. Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri.
42 Give to whoever asks you, and don't turn away whoever wants to borrow from you. Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.
43 "You have heard that it was said, 'You will love your neighbor and hate your enemy.' “Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’
44 But I tell you, love your enemies and pray for those who persecute you, Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani
45 so you may become children of your Father in heaven, because he makes his sun rise on evil and good and sends rain on just and unjust. kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’
46 If you love those who love you, what reward is that? Don't even tax collectors do the same? Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi?
47 If you greet only your brothers, what more do you do than others? Don't even the Gentiles do that? Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi?
48 Be perfect, therefore, as your heavenly Father is perfect." Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]