Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Matthew 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Jesus called his twelve disciples and gave them authority over unclean spirits, to drive them out and heal every disease and every sickness. Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.
2 The twelve apostles' names: first, Simon called Peter, and Andrew his brother; James son of Zebedee, and John his brother; Mayina a atumwi khumi ndi awiriwo ndi awa: woyamba, Simoni (wotchedwa Petro) ndi mʼbale wake Andreya; Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mʼbale wake Yohane,
3 Philip and Bartholomew; Thomas and Matthew the tax collector; James son of Alphaeus and Thaddaeus; Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo;
4 Simon the Zealot and Judas Iscariot, who also betrayed him. Simoni Mzerote ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
5 Jesus sent these twelve, instructing them: "Do not go to Gentile regions or enter a Samaritan town. Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya.
6 Go rather to the lost sheep of the house of Israel. Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli.
7 As you go, proclaim this message: 'The kingdom of our Father has come near.' Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’
8 Heal the sick, raise the dead, cleanse those with leprosy, drive out demons. Freely you received; freely give. Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.
9 Do not take any gold or silver or copper in your belts. “Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu;
10 No travel bag, no second shirt, no sandals, no staff—the worker deserves his food. musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake.
11 Whatever town or village you enter, find out who is worthy there, and stay there until you leave. Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka.
12 As you enter the home, greet it. Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni.
13 If the home is worthy, let your peace rest on it; if not, let it return to you. Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.
14 If anyone won't welcome you or hear your words, shake the dust off your feet as you leave that house or town. Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo.
15 Truly I tell you: Sodom and Gomorrah will fare better on judgment day than that town. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.
16 Look, I send you out as sheep among wolves; so be as shrewd as serpents, as innocent as doves. “Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda.
17 Beware of people; they will hand you over to councils and whip you in their synagogues. Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo.
18 For my sake you'll be brought before governors and kings, as testimony to them and the Gentiles. Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina.
19 But when they hand you over, don't worry about what to say or how—for what to say will be given you at that time, Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene,
20 for it will not be you speaking, but the Spirit of your Father speaking through you. pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.
21 Brother will betray brother to death, father his child; children will rise against their parents and have them killed. “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe.
22 Everyone will hate you because of my name, but whoever holds out to the end will be saved. Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka.
23 When persecuted in one town, flee to the next. I tell you truly: you won't finish Israel's towns before the Son of Man comes. Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.
24 The student is not above the teacher, nor the servant above his master. “Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo wantchito saposa bwana wake.
25 It's enough for the student to become like the teacher, and the servant like the master. If they call the head of the house Beelzebul, how much more his household! Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!
26 So do not be afraid of them. There is nothing concealed that will not be disclosed, or hidden that will not be made known. “Chifukwa chake musaope iwo. Pakuti palibe chinthu chobisika chimene sichidzavundukulidwa, ndi chobisika chimene sichidzadziwika.
27 What I tell you in the dark, say in daylight; what's whispered in your ear, proclaim from rooftops. Chimene ndikuwuzani Ine mu mdima, muchiyankhule poyera; chimene akunongʼonezani mʼkhutu, muchilalikire muli pa denga.
28 Don't fear those who kill the body but not the soul; instead fear the One able to destroy both soul and body in hell. Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.
29 Aren't two sparrows sold for a penny? Yet not one falls to the ground without your Father. Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu.
30 And even the very hairs of your head are all numbered. Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale.
31 So do not be afraid; you are worth more than many sparrows. Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.
32 Therefore, whoever acknowledges me before others, I will also acknowledge before my Father in heaven. “Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba.
33 But whoever denies me before others, I'll deny before my Father in heaven. Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.
34 Do not think I came to bring peace on earth; I came not to bring peace but a sword. “Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga.
35 For I came to pit a man against his father, a daughter against her mother, a daughter-in-law against her mother-in-law, Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa “ ‘Munthu ndi abambo ake, mwana wamkazi ndi amayi ake, mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake,
36 a man's enemies will be the members of his own household. adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’
37 Whoever loves father or mother above me is unworthy of me; whoever loves son or daughter above me is unworthy of me. “Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga.
38 Whoever does not take up his cross and follow me is not worthy of me. Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga.
39 Whoever finds his life loses it, and whoever loses his life for my sake finds it. Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza.
40 Whoever welcomes you welcomes me, and whoever welcomes me welcomes the One who sent me. “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine.
41 Whoever welcomes a prophet as a prophet gets a prophet's reward, and whoever welcomes a righteous person as a righteous person gets a righteous person's reward. Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama.
42 And whoever gives just a cup of cold water to one of these little ones because he is my disciple, truly I tell you, will never lose his reward." Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]