Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Judges 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The messenger of our Father went up from Gilgal to Bochim and said, "I brought you up out of Egypt into the land I swore to your fathers. I said, 'I will never break my covenant with you. Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu,
2 You will make no covenant with this land's people; tear down their altars.' But you have not obeyed my voice. What have you done? ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi?
3 So now I say: I won't drive them out before you; they'll be thorns in your sides, their gods a trap to you." Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.”
4 When the messenger of our Father spoke these words to all the Israelites, the people wept aloud. Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza,
5 And they named that place Bochim, and there they sacrificed to our Father. ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova.
6 When Joshua dismissed the people, the Israelites each went to claim their own land inheritance. Yoswa atawuza Aisraeli kuti achoke, iwo anapita kukatenga dzikolo, aliyense dera lake.
7 The people served our Father throughout the days of Joshua and the elders who outlived him, having seen all the great work our Father did for Israel. Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira.
8 Joshua son of Nun, servant of our Father, died at 110 years old. Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110.
9 They buried him in his inheritance land at Timnath-heres, in Ephraim's hill country, north of Mount Gaash. Ndipo anamuyika mʼmanda a mʼdziko lake, ku Timnati-Heresi mʼdziko la mapiri la Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
10 That whole generation was also gathered to their ancestors, and another generation rose after them who did not know our Father or the work he did for Israel. Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli.
11 Israel's people did evil in our Father's sight and served the Baals. Choncho Aisraeli anayamba kuchita zinthu zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anatumikira Abaala.
12 They abandoned our Father, the God of their fathers, who brought them out of the land of Egypt. They followed other gods of the surrounding peoples, bowed to them, and provoked our Father to anger. Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova.
13 They abandoned our Father and served Baal and the Ashtaroth. Iwo anasiya Yehova ndi kumatumikira Baala ndi Asiteroti.
14 So our Father's anger flared against Israel, and he handed them to raiders who plundered them, selling them to surrounding enemies, so they could no longer stand against them. Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse.
15 Everywhere they marched out, our Father's hand was against them for harm, as he had said and sworn to them. They were in dire distress. Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu.
16 Then our Father raised up judges who saved them from the hand of their raiders. Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo.
17 But they would not listen even to their judges. They prostituted themselves to other gods and bowed to them, quickly turning from the way their fathers walked, who had obeyed our Father's commands; they would not do the same. Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi.
18 When our Father raised up judges, he was with each judge and rescued them from their enemies all that judge's days; for our Father was moved to compassion by their groaning under their oppressors. Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa.
19 But when the judge died, they turned back and grew more corrupt than their fathers, following other gods to serve and bow down to them. They abandoned none of their practices or stubborn ways. Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani.
20 So our Father's anger flared against Israel, and he said, "Because this nation has broken my covenant that I commanded their fathers, and has not obeyed my voice, Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere,
21 I will no longer drive out any nation Joshua left when he died, Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira.
22 to test Israel by them: whether they'd keep our Father's way, walking in it as their fathers did, or not." Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.”
23 So our Father left those nations, not driving them out quickly, and did not give them into Joshua's hand. Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]