Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 43 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 But now, this is what our Father says—he who created you, Jacob, he who formed you, Israel: Do not be afraid, for I have redeemed you; I have called you by name, you are mine. Koma tsopano, Yehova amene anakulenga, iwe Yakobo, amene anakuwumba, iwe Israeli akuti, “Usaope, pakuti ndakuwombola; Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
2 When you pass through the waters, I will be with you; and through the rivers, they will not overwhelm you. When you walk through fire, you will not be burned, and the flame will not consume you. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe; ndipo pamene ukuwoloka mitsinje, sidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto, sudzapsa; lawi la moto silidzakutentha.
3 For I am your Father, the Holy One of Israel, your Savior. I gave Egypt as your ransom, Cush and Seba in your place. Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako, Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako. Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe, ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
4 Because you are precious in my eyes, and honored, and I love you, I give people in exchange for you, and nations in exchange for your life. Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga, ndipo chifukwa ndimakukonda, ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
5 Do not be afraid, for I am with you. From the east I will bring your children, and from the west I will gather you. Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe; ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa, ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
6 To the north I will say, Release them, and to the south, Keep them no longer; bring back my sons from distant lands and my daughters from earth's farthest reaches, Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’ Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali, ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
7 everyone who is called by my name, whom I created for my glory, whom I formed and made. onsewo amadziwika ndi dzina langa; ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
8 Bring out the people who have eyes but are blind, and who have ears but are deaf. Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya, anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.
9 All the nations gather together, and the peoples assemble. Who among them can declare this and tell us the former things? Let the nations bring their witnesses to prove they are right, so that others may hear and say, It is true. Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi, anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu. Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi? Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale? Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona, kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
10 You are my witnesses, declares our Father, and my chosen servant, so that you can know and trust me and grasp that I am he. No god was formed before me, and none will come after me. Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga, ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha, kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina, ngakhale pambuyo panga sipadzakhalaponso wina.”
11 I, I am your Father, and besides me there is no savior. Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova, ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.
12 I declared and saved and proclaimed, when there was no foreign god among you; and you are my witnesses, declares our Father, and I am your Father. Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa; ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu. Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
13 From this day on I am he; there is no one who can deliver from my hand. I act, and who can turn it back? “Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse. Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga, ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”
14 This is what our Father says—your Redeemer, the Holy One of Israel: For your sake I send to Babylon and bring them all down as fugitives, the Babylonians, in the ships they are so proud of. Yehova akuti, Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti, “Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni ndi kukupulumutsani. Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
15 I am your Father, your Holy One, the Creator of Israel, your King. Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”
16 This is what our Father says—he who makes a way in the sea, a path through the mighty waters, Yehova anapanga njira pa nyanja, anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.
17 who brings out chariot and horse, army and warrior together—they lie down and cannot rise, snuffed out, quenched like a wick: Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo, gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu, ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
18 Do not remember the former things, nor consider the things of the past. “Iwalani zinthu zakale; ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.
19 Look, I am doing a new thing; now it springs up—do you not see it? I will make a way in the wilderness and rivers in the desert. Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano! Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona? Ine ndikulambula msewu mʼchipululu ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
20 The wild animals will honor me, the jackals and the ostriches, because I provide water in the wilderness and rivers in the desert, to give drink to my chosen people, Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi zinandilemekeza. Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa.
21 the people I formed for myself, that they might declare my praise. Anthu amene ndinadziwumbira ndekha kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.
22 "Yet you did not call on me, Jacob; you have grown weary of me, Israel. “Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo, munatopa nane, Inu Aisraeli.
23 You have not brought me sheep for your burnt offerings, nor honored me with your sacrifices. I did not burden you with grain offerings or weary you with frankincense. Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza, kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu. Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.
24 You have not bought me fragrant cane with money, nor satisfied me with the fat of your sacrifices. Instead, you have burdened me with your sins; you have wearied me with your wrongdoing. Simunandigulire bango lonunkhira kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
25 "I, I am he who blots out your rebellions for my own sake, and I will not remember your sins. “Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini, ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
26 Remind me; let us argue it out together; state your case, that you may be proved right. Mundikumbutse zakale, ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi; fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.
27 Your first father sinned, and your spokesmen rebelled against me. Kholo lanu loyamba linachimwa; ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.
28 So I profaned the officials of the sanctuary; I handed Jacob over to destruction and Israel to scorn." Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero, ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]