Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 13 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The oracle concerning Babylon that Isaiah son of Amoz saw. Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:
2 "Raise a banner on a bare hilltop; call out to them, beckon with your hand that they may enter the gates of the nobles. Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see, muwafuwulire ankhondo; muwakodole kuti adzalowe pa zipata za anthu olemekezeka.
3 I myself have commanded my consecrated ones; I have summoned my warriors to carry out my anger—those who exult in my majesty." Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga; ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira amene amadzikuza ndi chipambano changa.
4 Listen—an uproar on the mountains, like that of a great multitude! Listen—the roar of kingdoms, of nations massing together! The Father of heaven's armies is mustering an army for battle. Tamvani phokoso ku mapiri, likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu! Tamvani phokoso pakati pa maufumu, ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi! Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera kuchita nkhondo.
5 They come from a far-off land, from the ends of the heavens—our Father and the weapons of his wrath—to destroy the whole earth. Iwo akuchokera ku mayiko akutali, kuchokera kumalekezero a dziko Yehova ali ndi zida zake za nkhondo kuti adzawononge dziko la Babuloni.
6 Wail, for the day of our Father is near; it comes as devastation from the Almighty. Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
7 Because of this every hand goes limp, and every human heart melts. Zimenezi zinafowoketsa manja onse, mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
8 They are gripped with terror; pangs and agony seize them; they writhe like a woman in labor. They stare at one another in horror, their faces aflame. Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu, zowawa ndi masautso zidzawagwera; adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka. Adzayangʼanana mwamantha, nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.
9 Look—the day of our Father is coming, cruel, with fury and burning anger, to make the earth a desolation and to destroy the sinners on it. Taonani, tsiku la Yehova likubwera, tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo; kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.
10 The stars of the heavens and their constellations will give no light; the sun will be dark when it rises, and the moon will not shed its glow. Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga sizidzaonetsa kuwala kwawo. Dzuwa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzawala konse.
11 "I will bring judgment upon the world for its evil, and upon the wicked for their guilt; I will put an end to the arrogance of the proud and humble the pride of tyrants. Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake, anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza, ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
12 I will make people rarer than pure gold, mankind scarcer than the gold of Ophir. Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino. Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.
13 So I will make the heavens tremble, and the earth will shake from its place, at the wrath of the Father of heaven's armies, in the day of his burning anger." Tsono ndidzagwedeza miyamba ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.
14 Like a hunted gazelle, like sheep with no one to gather them, each will turn back to his own people, each will flee to his own land. Ngati mbawala zosakidwa, ngati nkhosa zopanda wozikusa, munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo, aliyense adzathawira ku dziko lake.
15 Whoever is found will be run through, and whoever is captured will fall by the sword. Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa adzaphedwa momubaya ndi lupanga.
16 Their infants will be dashed to pieces before their eyes; their houses will be plundered and their wives raped. Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona; nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.
17 "Look—I am stirring up the Medes against them, who care nothing for silver and take no delight in gold. Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva ndipo sasangalatsidwa ndi golide, kuti amenyane ndi Ababuloni.
18 Their bows will cut down the young men; they will show no mercy to infants; they will have no pity for the children." Adzapha anyamata ndi mauta awo; sadzachitira chifundo ana ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.
19 And Babylon, the jewel of kingdoms, the splendor and pride of the Babylonians, will be like Sodom and Gomorrah when our Father overthrew them. Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse. Anthu ake amawunyadira. Koma Yehova adzawuwononga ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
20 It will never be inhabited or settled through all generations; no Arab will camp there, no shepherds will bed down their flocks there. Anthu sadzakhalamonso kapena kukhazikikamo pa mibado yonse; palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake, palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.
21 But desert creatures will lie down there, and their houses will be full of howling beasts; there ostriches will dwell, and wild goats will leap about. Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko, nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe; mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi, ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.
22 Hyenas will howl in its strongholds, and jackals in its luxurious palaces. Her time is near, and her days will not last long. Mu nsanja zake muzidzalira afisi, mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe. Nthawi yake yayandikira ndipo masiku ake ali pafupi kutha.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]